Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Tizivutika?

Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Tizivutika?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limayankha mosapita m’mbali kuti ayi. Yehova Mulungu sanalenge anthu kuti azivutika. Koma anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, anakana kugonjera ulamuliro wa Mulungu n’kumayendera mfundo zawozawo pa nkhani yokhudza zinthu zabwino ndi zoipa. Iwo anasankha kusamvera Mulungu ndipo anayamba kuvutika.

 Masiku ano tikuvutikanso chifukwa choti Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu. Koma si Mulungu amene anachititsa kuti anthufe tizivutika.

 Baibulo limati, “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Choncho munthu wina aliyense amavutika, ngakhale amene Mulungu amamukonda.