NSANJA YA OLONDA January 2014 | Kodi Anthu Omwe Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?

Anthu ambiri safuna kukamba za imfa. Anthu ambiri safuna kuti adzafe. Kodi pali amene angagonjetse imfa?

NKHANI YAPACHIKUTO

Imfa Ndi Yopweteka Kwambiri

Tonse tikhoza kudzamwalira. Chifukwa choti imfa ndi yopweteka kwambiri, anthu ambiri amafuna kudziwa zambiri zokhudza imfa.

NKHANI YAPACHIKUTO

Nkhondo Yolimbana ndi Imfa

Kuyambira kale, anthu afufuza njira zothetsera imfa. Kodi n’zotheka kuthetsa imfa?

NKHANI YAPACHIKUTO

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo

N’chifukwa chiyani Yesu anayerekezera imfa ndi tulo? Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani za m’Baibulo za anthu amene anaukutsidwa?

KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?

Buku loyambirira la m’Baibulo limafotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika ngakhale kuti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto.

Kodi Mukudziwa?

Kodi anthu a m’nthawi ya Yesu, ankapereka bwanji zopereka zawo? Kodi zimene zili m’Baibulo zomwe Luka analemba ndi zolondola?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Yehova Sanandiiwale”

Mzimayi wokonda kupemphera ameneyu anapeza mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso oti, N’chifukwa chiyani anthufe timafa? komanso, N’chiyani chimachitika tikamwalira? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene moyo wake unasinthira atadziwa zinthu zolondola.

Akufa Adzaukitsidwa

Atumwi a Yesu anali ndi chikhulupiriro cholimba chakuti akufa adzakhalanso ndi moyo. N’chifukwa chiyani ankakhulupirira ndi mtima wonse zimenezi?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi inuyo mumadziwa zotani zokhudza Mulungu? Kodi tingaphunzire bwanji za Mulungu?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizichita Chiyani?

Kodi mukufunika kuona masomphenya kapena chizindikiro chinachake kuti mudziwe zimene Mulungu akufuna kuti muzichita? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe yankho la m’Baibulo.