Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Yehova Sanandiiwale”

“Yehova Sanandiiwale”
  • CHAKA CHOBADWA: 1922

  • DZIKO: SPAIN

  • POYAMBA: NDINALI MPHUNZITSI WA KATIKISIMU

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wa Bilbao kumpoto kwa dziko la Spain ndipo anthu a m’derali sanali osauka. M’banja mwathu tinalimo ana 4, koma ine ndinali wachiwiri. Banja lathu linali lakatolika ndipo tsiku lililonse ndinkapita ku Misa. Ndili ndi zaka 23 ndinayamba ntchito yauphunzitsi ndipo ndinagwira ntchitoyi kwa zaka 40. Ndinkaphunzitsanso phunziro lina lokhudza ziphunzitso zachikatolika. Madzulo ndinkaphunzitsa katikisimu atsikana oyamba kumene.

Nditakhala m’banja kwa zaka 12, mwamuna wanga anamwalira n’kundisiira ana aakazi 4 amene ndinkafunika kuwasamalira. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 33 zokha. Ndinkaganiza kuti ndikamapita ku tchalitchi ndizilimbikitsidwa pa nthawi yovutayi, koma m’malomwake ndinali ndi mafunso ambirimbiri opanda mayankho. Ndinkadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anthu akufabe ngakhale kuti Yesu anatiwombola? Ngati anthu abwino amapita kumwamba, n’chifukwa chiyani timapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere?’ Komanso ndinkaganiza kuti: ‘Ngati anthufe tikamwalira Mulungu amatiweruza kuti ndife oyenera kupita kumwamba, kupuligatoliyo kapena kumoto, n’chifukwa chiyani tidzafunika kuti Mulungu atiweruzenso pa tsiku la chiweruzo?’

Ndinafunsapo ansembe athu mafunso amenewa. Wina anandiyankha kuti: “Inenso sindikudziwa. Mwina mukafunse a bishopu. Komanso palibe chifukwa choti muzivutika ndi zimenezi. M’mesa mumakhulupirira Mulungu? Ingozisiyani zimenezo.” Koma ine ndinapitirizabe kufufuza kuti ndipeze mayankho. Kenako ndinayamba kumapita kukamvera ulaliki wa matchalitchi a Pentekosite, wa Anositiki, kapena kuti ampatuko, komanso ansembe ena achikatolika amene amati amatsatira kwambiri Yesu. Koma palibe amene anayankha mafunso anga mogwira mtima.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Ndili ndi zaka 60, mwana wanga wa sukulu wa zaka 7 anandiitanira ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ndinapitadi. Ndinasangalala kwambiri ndi zomwe ndinamva komanso kuona kumeneko. Koma chifukwa choti ndinkakhala wotanganidwa kwambiri sindinapitirize kusonkhana ndi a Mboni. Patatha zaka ziwiri, Juan ndi mkazi wake Maite, omwe anali a Mboni, anabwera kunyumba kwathu. Anthuwa anapitirizabe kumabwera kunyumba kwathu ndipo kwa miyezi itatu ndinkawafunsa mafunso ambiri komanso ovuta ndipo kenako anayamba kundiphunzitsa Baibulo.

Ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira moti  sindinkafuna kuti pathe mlungu, ndisanaphunzire. Ndinkafufuza zimene ndaphunzira pogwiritsa ntchito Mabaibulo atatu osiyanasiyana kuti nditsimikizire ngati zimene a Mboni za Yehova ankandiphunzitsa zinali zoona. Pasanapite nthawi yaitali ndinazindikira kuti zimene ndinaphunzira kutchalitchi kwathu sizinali zolondola. Ndinaona kuti zimene ndinaphunzira kutchalitchi kwathu zinali zosiyana kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira m’Baibulo. Zinali ngati munthu akuzula mumtima mwanga zinthu zimene ndinazikhulupirira kwa nthawi yaitali.

Ndinkaona kuti ndinapeza chuma chamtengo wapatali

Kenako mwamuna amene ndinakwatirananso naye anadwala kwambiri n’kumwalira. Pa nthawiyi ndinasiya ntchito ndipo ndinachoka mumzinda wa Bilbao. Banja limene linkandiphunzitsa Baibulo lija nalonso linasamuka mumzindawu. Choncho ndinasiya kuphunzira Baibulo. Komabe pansi pa mtima ndinkaona kuti ndinapeza chuma chamtengo wapatali chomwe sindidzachiiwala. Patapita nthawi ndinabwereranso mumzinda wa Bilbao.

Patatha zaka 20, ndili ndi zaka 82, Juan ndi Maite anabwereranso ku Bilbao ndipo anabwera kunyumba kwathu kudzandiona. Ndinasangalala kwambiri kukumana nawonso. Ndinazindikira kuti Mulungu sanandiiwale ndipo ndinayambiranso kuphunzira Baibulo. Ngakhale kuti nthawi zina ndinkafunsa mafunso omweomwewo, Juan ndi Maite ankandilezera mtima. Ndinkafunika kuphunzira mfundo za m’Baibulo mobwerezabwereza kuti ndisiye kukhulupirira zinthu zolakwika zomwe ndinkakhulupirira poyamba. Ndinafunikanso kudziwa bwino mfundo za m’Baibulo kuti ndizitha kufotokozera bwinobwino mfundozi anzanga komanso achibale anga.

Ndili ndi zaka 87, ndinabatizidwa pamsonkhano wina wa Mboni za Yehova ndipo ili linali tsiku losangalatsa kwambiri pa moyo wanga. Pamsonkhanowu panakambidwa nkhani yochokera m’Baibulo yomwe cholinga chake chinali kulimbikitsa anthu amene tinabatizidwa tsiku limenelo. Nkhaniyi inandikhudza mtima kwambiri moti ndinalira. Ndikamamvetsera nkhaniyi ndinkangomva ngati Yehova akulankhula nane. Nditabatizidwa, a Mboni za Yehova ambiri anabwera kudzandiyamikira ndipo ambiri mwa anthuwa kanali koyamba kukumana nawo.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Kuyambira kale ndinkadziwa kuti Yesu Khristu ndi “njira” koma sindinkaganizira kwambiri kuti ndi njira yopita kuti. (Yohane 14:6) Koma zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kudziwa kuti Yesu ndi njira yotithandiza kudziwa Yehova. Zinandithandizanso kumudziwa bwino Yehovayo. Panopa ndimaona kuti Mulungu ndi Atate wanga komanso Bwenzi langa ndipo ndimapemphera kwa iye momasuka. Buku lakuti Yandikirani kwa Yehova * linandithandizanso kwambiri. Ndinawerenga bukuli usiku wonse mpaka kulimaliza. Ndinaona kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo kwambiri ndipo zimenezi zinandikhudza mtima kwambiri.

Ndikaganizira zaka zonse zimene ndakhala ndikufufuza mayankho a mafunso anga aja, ndimaona kuti zimene Yesu ananena ndi zoona. Iye anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Mateyu 7:7) Panopa ndinapeza mayankho a mafunso onse amene ndinali nawo ndipo ndimasangalala kwambiri kuthandizanso ena kudziwa zolondola.

Ngakhale kuti panopa ndili ndi zaka 90, ndimaona kuti padakali zambiri zokhudza Yehova zoti ndiphunzire. Tsiku lililonse ndikapita kukasonkhana ku Nyumba ya Ufumu ndimasangalala kwambiri. Ndimasangalala ndi zimene ndimaphunzira komanso kucheza ndi a Mboni anzanga. Ndimafunitsitsa kudzakhalanso mphunzitsi m’dziko lapansi la Paradaiso limene Mulungu walonjeza. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndimalakalaka kudzakumana ndi okondedwa anga amene anamwalira, n’kudzakhala ndi mwayi wowaphunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Machitidwe 24:15Ndidzasangalala kwambiri kuwafotokozera mfundo za m’Baibulo zimene ndaphunzira nditakalamba, zomwe ndimaona kuti ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova wandipatsa.)

^ ndime 15 Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.