NSANJA YA OLONDA October 2013 | Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

Baibulo limatiuza za komwe tinachokera ndiponso zoti Mulungu wakonza zopulumutsa anthu kudzera mwa Mesiya.

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?

Baibulo silimangonena zokhudza Mulungu koma limanenanso kuti linachokera kwa Mulungu. Kodi lingakuthandizeni bwanji?

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Zinachitika Kuti Tizikumana ndi Mavuto

Buku la Genesis lomwe ndi buku loyamba m’Baibulo limafotokoza mwachidule koma momveka bwino chimene chinachitika kuti dzikoli likhalepo. Kodi tingaphunzirepo chiyani m’buku la Genesis?

NKHANI YAPACHIKUTO

Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu

Kodi Mesiya anathandiza bwanji kuti zimene Mulungu analonjeza Abulahamu zitheke? Werengani nkhaniyi kuti muone mmene Mulungu adzathetsere mavuto a anthu monga matenda komanso imfa.

NKHANI YAPACHIKUTO

“Tapeza Mesiya”

Anthu ambiri ankakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya koma ena sanamukhulupirire. Werengani Baibulo kuti mudziwe chifukwa chake.

NKHANI YAPACHIKUTO

Uthenga Wabwino Wopita ku Mitundu Yonse

Kodi uthenga wochokera kwa Mulungu wopezeka m’Baibulo ungakuthandizeni bwanji panopo komanso m’tsogolo?

Zimene Mungachite Ngati Banja Latha

Anthu ambiri amene amathetsa banja amaona kuti zinthu siziyendabe bwino ngati mmene amaganizira. Mfundo za m’Baibulo zikhoza kukuthandizani kuti zinthu ziziyendabe bwino ngakhala banja lanu latha.

YANDIKIRANI MULUNGU

“Yehova Anakukhululukirani ndi Mtima Wonse”

Yehova Mulungu amakhululukira anthu amene alapa. Kodi ifeyo tizitani munthu wina akatilakwira? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukirana?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Anthu Ambiri Ankadana Nane”

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene kuphunzira Baibulo kunathandizira munthu yemwe anali wankhanza kusintha n’kukhala munthu wokonda mtendere.

Kodi Mitundu ya Kaonekedwe ka Zinthu Imakukhudzani Bwanji?

Mitundu imakhudza mmene anthu amaganizira. Werengani kuti mudziwe mmene mitundu itatu imakhudzira mmene mumaonera zinthu.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Kunyumba ndi Nyumba?

Dziwani zimene Yesu anauza ophunzira ake oyambirira kuti azichita.