Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

N’CHIFUKWA chiyani woimba wina wotchuka anasiya kuimba n’cholinga choti azigwira ntchito yolalikira nthawi zonse? Nanga n’chiyani chinachititsa chigawenga china kusintha khalidwe lake, ngakhale kuti woweruza milandu wina ananena kuti chigawengacho sichingasinthe zivute zitani? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa.

“Kapolo sangatumikire ambuye awiri.”​—ANTOLINA ORDEN CASTILLO

CHAKA CHOBADWA: 1962

DZIKO: SPAIN

POYAMBA: NDINALI KATSWIRI WAZISUDZO KOMANSO WOIMBA

KALE LANGA: Ndinabadwira m’mudzi wina waung’ono wa Tresjuncos womwe uli m’dera lina lotchedwa La Mancha ku Spain. Makolo anga anali alimi ndipo amayi anali Mkatolika pomwe bambo anali Mpolotesitanti. Bambo anandiuza kuti ndizilemekeza Baibulo ndipo nthawi zambiri ndinkawaona iwo akuliwerenga. Koma mayi ankandiphunzitsa Chikatolika ndipo Lamlungu lililonse ankanditenga popita ku Misa.

Ndili ndi zaka 15, ndinachoka kumudzi n’kupita kumakakhala ndi achemwali anga aakulu mumzinda wa Madrid. Poyamba ndinkalakalaka kuonana ndi makolo anga koma kenako ndinazolowera moyo wa m’tauni. Ndili ndi zaka 17 ndinapeza mwayi wogwira ntchito kwa miyezi ingapo m’gulu lina lochita zisudzo ndiponso kuimba nyimbo zachikhalidwe cha ku Spain. Pa nthawi imeneyi ndinkasangalala kwambiri ndipo ndinkafunitsitsa kudzakhala katswiri wa zisudzo. Ndinasiya maphunziro anga a zausekilitale ndipo ndinayamba kugwira ntchito ndi makampani osiyanasiyana ochita zisudzo. Nthawi imeneyinso ndi imene ndinayamba chibwenzi ndi mchimwene wa mnzanga wina wake. Ndinkaona kuti zinthu zikundiyendera bwino chifukwa ndinali pa ntchito yabwino, ndinali ndi ndalama komanso ndinali ndi chibwenzi.

Kenako ndinayamba kuyenda ndi magulu osiyanasiyana ochita zisudzo ndipo tinayenda m’madera osiyanasiyana m’dziko lonse la Spain komanso m’mayiko ena monga Colombia, Costa Rica, Ecuador, ndi Venezuela. Ndinkaimbanso ndi magulu osiyanasiyana oyimba nyimbo zotchuka mumzinda wa Madrid. Nyimbo zimenezi zinali za chamba cha “La movida madrileña.” Limodzi mwa magulu amene ine ndinkaimba mawu otsogolera linatchuka kwambiri.

Ntchito imeneyi ndinkaikonda kwambiri koma ndinkadana ndi makhalidwe oipa a anthu amene ndinkaimba nawowo. Komanso, nthawi zonse ndinkayesetsa kuti ndizioneka wokongola kwambiri ndipo ndinkachita zinthu zoti anthu azindionabe kuti ndine wotchuka. Ndinkasala kwambiri zakudya n’cholinga chakuti ndisanenepe. Chifukwa cha zimenezi ndinayamba kudwala matenda amene amayamba chifukwa chosala kudya poopa kunenepa.

Komabe cholinga changa chinali chomwe chija chofuna kukhala katswiri wa zisudzo. Patapita nthawi anandisankha kuti ndipite ku sukulu ina yophunzitsa luso lovina komanso kuchita zisudzo. (Madrid School of Dramatic Arts) Ku sukuluko, ankatiphunzitsa kuti pochita zisudzo munthu amafunika kuganizira kaye mmene akumvera mumtima mwake kenako n’kuganiziranso za mmene munthu amene akumuyerekezerayo akumvera mumtima mwake, ndiyeno n’kuchita mogwirizana ndendende ndi zimenezo. Nditatsatira malangizo amenewa, ndinaona kuti ndinali munthu wopanda chifundo, ndinkaganiza mwachibwanabwana kwambiri komanso ndinali wodzikonda.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndinkadziwa kuti, ngati ndikufuna kukhala ndi makhalidwe abwino ndinafunika kuchita khama. Koma sindinkadziwa kuti ndingayambire pati. Ndinapita kutchalitchi china cha evanjeliko mumzinda wa Madrid, chomwenso ndinapitako ndi makolo anga ndili wamng’ono. Kenako ndinapemphera kwa Mulungu pogwiritsa ntchito dzina lake lakuti Yehova.

Pasanapite nthawi, kunyumba kwathu kunabwera a Mboni za Yehova awiri. Ndinasangalala kukambirana nawo mfundo za m’Baibulo, koma ndinkatsutsanso zambiri zimene ankaphunzitsa. Mayi wina wa Mboni za Yehova dzina lake Esther anayamba kundiphunzitsa Baibulo ndipo anali woleza mtima kwambiri. Iye ndi banja lake ankandikonda kwambiri komanso ankandisonyeza chifundo. Ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo pasanapite nthawi ndinazindikira kuti ndapeza choonadi chomwe ndinkafunafuna.

Pa nthawiyi n’kuti nditangomaliza kumene maphunziro azisudzo, ndipo panali makampani ambiri amene ankafuna kundilemba ntchito. Nthawi ina, ndinapatsidwa mbali yoti ndikachite mu sewero lina limene anakonza kuti adzaliwonetse pamalo ena otchuka oonetsera zisudzo mumzinda wa Madrid. Ndinkadziwa kuti ngati ndikufuna zinthu zindiyendere bwino monga katswiri wa zisudzo, ndinayenera kuika maganizo anga onse pa zisudzo basi. Koma patapita nthawi ndinaganiza zopeza ntchito ina imene ingamandipatse nthawi yambiri yotumikira Mulungu. Ndinaona kuti mawu amene Yesu ananena ndi oona. Iye anati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mateyu 6:24) Pa nthawiyi n’kuti nditakhala pachibwenzi ndi mnyamata uja kwa zaka 8. Koma iye sankagwirizana ndi zimene ndinayamba kuphunzira, choncho ndinaganiza zothetsa chibwenzicho. Komabe kuchita zonsezi kunali kovuta kwambiri.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndimagwira ntchito yangayi mwaganyu kusangalatsa anthu okalamba. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndizipeza nthawi yambiri yophunzitsa Baibulo anthu a m’dera lathu olankhula Chiarabu. Ndikudziwa kuti ndifunika kuchita khama kuti ndichidziwe bwino chinenerochi. Komabe ndimasangalala kwambiri kuuza anthu ena zinthu zabwino zimene ndaphunzira. Anthu amenewa ndi ochezeka komanso ndi ofunitsitsa kuphunzira za Mulungu.

Panopa ndikusangalala kwambiri ndi moyo kusiyana ndi mmene ndinalili pomwe ndinkachita maphunziro a zisudzo chifukwa panopa ndikuona kuti moyo wanga ndi waphindu. Ndikuona kuti Yehova wandithandiza kuti ndikhale munthu wabwino komanso wosangalala.

“Ndasonyeza kuti zimene woweruza wina ananena zinali zabodza.”​—PAUL KEVIN RUBERY

CHAKA CHOBADWA: 1954

DZIKO: ENGLAND

POYAMBA: NDINALI CHIGAWENGA CHOOPSA

KALE LANGA: Ndinabadwira m’tawuni ya Dudley m’chigawo cha West Midlands ku England ndipo m’ntawuni imeneyi muli mafakitale ambiri. Kuyambira ndili mwana, bambo anga ankandiphunzitsa kuti ndizikonda kuwerenga. Ankandilimbikitsanso kuti ndizikonda zinthu zachilengedwe ngakhale kuti iwo ankakhulupirira kuti zinachita kusintha kuchoka kuzinthu zina. Komanso ankakonda kundiuza kuti kulibe Mulungu. Ngakhale zinali choncho, makolo anga ankandipititsa ku Sande sukulu ya tchalitchi cha Methodist chomwe chinali kudera lathu.

Ndili ndi zaka 8, tsiku lina ndinaona anyamata ena akuwotcha boti limene linali m’madzi. Anyamatawa anandiwopseza kuti ndisaulule moti apolisi atafika sindinauluredi. Chifukwa cha zimenezi anandiyimba mlandu wootcha botilo ndipo zimenezi zinandikwiyitsa kwambiri. Pofuna kusonyeza kukwiya ndinayamba kuwononga masukulu, matchalitchi komanso mafakitale ndipo zinthu zimene ndinawonongazo zinali za ndalama zambirimbiri. Mmene ndimakwanitsa zaka 10 n’kuti nditayamba kuthyola nyumba za anthu ndi masitolo n’kumaba. Kuwotcha zinthu za eni kunkandisangalatsa moti ndinapalamula milandu yambiri yootcha masitolo ndi nyumba. Kusukulu kwathu aphunzitsi anatopa nane ndipo ankati ndine nkhutukumve.

Ndili ndi zaka 12, ndinayamba kuwerenga buku la zamizimu moti ndinakonza thabwa langalanga la zamatsenga. Popeza makolo anga sankakhulupirira Mulungu, anaganiza kuti kuchita zinthu zokhudzana ndi zamizimu kulibe voto lililonse ndipo kungandithandize kuti ndisiye kupalamula milandu. Koma pa nthawi imene ndinkamaliza sukulu n’kuti nditaimbidwapo milandu kambirimbiri kukhoti la ana chifukwa chopalamula milandu yosiyanasiyana. Ndinalowa m’gulu lina la achinyamata ochita zauchigawenga moti nthawi zambiri ndinkayenda ndi lezala ndi tcheni cha njinga kuti ndizidzitetezera. Ndinapeza ntchito koma pasanapite nthawi anandimanga ndipo ntchitoyo inathera pompo. Atandimasula, ndinayambiranso kuwononga katundu wa anthu ndipo anandimanganso n’kundilamula kuti ndikhale m’ndende zaka ziwiri. Woweruza wina anafika ponena kuti sindingasinthe khalidwe langa zivute zitani ndipo ndine munthu woopsa kwambiri.

Nditatuluka kundende ndinakumana ndi mtsikana yemwe kale ndinali naye pachibwenzi, dzina lake Anita. Kenako tinakwatirana ndipo kwakanthawi ndinasiya kuba ndiponso kuchita zachiwawa. Koma patapita zaka zingapo ndinayambiranso khalidwe langa loipa. Ndinayamba kutchola masitolo ndi makampani n’kumaba ndalama. Ndinayambanso kumwa mankwala osokoneza bongo, kuledzera ndipo nthawi zambiri ndinkayenda ndi mfuti. Kenako ndinagwidwanso n’kutsekeredwa m’ndende.

Mkazi wanga Anita ankavutika kwambiri maganizo chifukwa cha khalidwe langali. Dokotala wina anamupatsa makhwala othandiza kuti asamakhale ndi nkhawa kwambiri koma anamulangiza kuti ayenera kuthetsa banja chifukwa ndi zimene zikanathandiza kuti vuto lakelo lithe. Mwamwayi iye sanatsatire malangizo amenewa.

MMENE BAIBULO LINASINTHILA MOYO WANGA: Titangokwatirana kumene, mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova koma kenako anasiya. Tsiku lina, a Mboni za Yehova anabweranso kunyumba kwathu kudzakambirana ndi Anita Mawu a Mulungu. Pa nthawi imeneyi n’kuti ine ndikugwira ukaidi komaliza chifukwa atanditukutsa sindimangidwenso. Zinangochitika kuti tsiku limene a Mboni anabwera kunyumba kwathuli, ndi tsiku limenenso ineyo ndinapemphera kwa Mulungu ndili m’ndende kuti: “Mulungu, chonde ndipatseni umboni wosonyeza kuti mulikodi.”

Patatha miyezi ingapo ndinatuluka kundende ndipo ndinapita kwa wansembe wa Angilikani n’kumupempha kuti azitiphunzitsa Baibulo. Koma iye ananena kuti chomwe angatiphunzitse ndi malamulo atchalitchi chawo komanso pemphero basi.

Kenako ndinangoyamba kuwerenga ndekha Baibulo. Ndinadabwa kwambiri nditaphunzira kuti Baibulo limaletsa kuchita zilizonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. (Deuteronomo 18:10-12) Tsiku lina ndinapeza magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe a Mboni anamusiira Anita tsiku lomwe ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize lija. Zimene ndinawerenga mu Nsanja ya Olonda imeneyi zinandichititsa kupempha a Mboni za Yehova kuti ayambe kutiphunzitsa Baibulo.

Achibale athu, anzathu komanso anzanga amene ndinkaba nawo sanasangalale atamva kuti tikuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ena ankanena kuti a Mboni akundisokoneza maganizo. Koma sikuti a Mboni ankandisokoneza maganizo chifukwa iwo ankandithandiza kuti ndiyambe kuganiza bwino. Ndinali ndi khalidwe loipa ndipo chikumbumtima changa sichinkagwira bwino ntchito. Kuwonjezera pa mavuto enanso ambirimbiri, ndinkasuta ndudu 60 patsiku. A Mboni za Yehova amene anatithandiza kuphunzira Baibulo komanso amene tinkakumana nawo ku Nyumba ya Ufumu anali anthu oleza mtima kwambiri ndiponso achifundo. Patapita nthawi ndinasiya makhalidwe onse oipa aja.​—2 Akorinto 7:1.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa ine ndi Anita takhala m’banja zaka 35. Mwana wathu ndiponso adzukulu athu awiri nawonso akutumikira Yehova. Masiku ano ine ndi Anita timatha nthawi yambiri tikuthandiza anthu kuphunzira Baibulo.

Kutumikira Yehova Mulungu kwachititsa kuti moyo wathu ukhale waphindu. Mu 1970, woweruza wina anauza anthu m’khoti kuti ineyo sindingasinthe. Koma mothandizidwa ndi Mulungu komanso pogwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo ndasonyeza kuti zimene woweruzayu anena zinali zabodza.