Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzipewa Kucheza Ndi Anthu a Makhalidwe Oipa

Muzipewa Kucheza Ndi Anthu a Makhalidwe Oipa

 Zoti Achinyamata Achite

Muzipewa Kucheza Ndi Anthu a Makhalidwe Oipa

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Dina, Sekemu, Yakobo, Simiyoni ndi Levi.

Chidule cha Nkhaniyi: Dina anagwiriridwa ndi Sekemu, azichimwene ake anakwiya kwambiri ndi zimenezi ndipo anakonza zokabwezera.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 34:1-31.

Kodi mukuganiza kuti Dina ankachita zotani ndi anzake a ku Kanani?

․․․․․

Polankhula ndi Dina, kodi mukuganiza kuti ndi nkhani zotani zomwe Sekemu “ankalankhula naye momunyengerera”?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yakobo ankamva bwanji pamene ankakalipira Simiyoni ndi Levi, zomwe zalembedwa m’vesi 30?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Dina ankakonda kukacheza ndi ana akazi a Akanani? (Mwachitsanzo, kodi n’kutheka kuti anali ofanana pa zinthu ziti? Kodi ndi zinthu ziti zimene ankazipeza kwa anthu a ku Kanani zomwe mwina kwawo kunalibe?)

․․․․․

Kodi ndi makhalidwe ati a Sekemu amene Dina ayenera kuti ankakopeka nawo? (Werenganinso vesi 312, ndi 19.)

․․․․․

 Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Dina sanachite kufuna kuti agone ndi Sekemu? (Werenganinso vesi 2.)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Simiyoni ndi Levi anachita bwino kupha anthu a mumzinda umene Sekemu ankakhala, pobwezera zimene Sekemu anachita? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA  . . .

Kufunika kosankha mwanzeru anthu ocheza nawo.

․․․․․

Kufunika kodziletsa kuti usabwezere ngakhale utakhala kuti wakwiya pa zifukwa zomveka.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi mungadziteteze bwanji kuti anthu amene satsatira malamulo a Mulungu asakugwiririreni?

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati mulibe Baibulo, uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.