Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika Komanso Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika Komanso Kuti Anthu Azivutika?

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika Komanso Kuti Anthu Azivutika?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi zoipa zinayamba bwanji?

Zoipa zinayamba pamene Satana ananena bodza lake loyamba. Satana analengedwa ali wabwinobwino. Poyamba iye anali mngelo wangwiro koma “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Iye anayamba kulakalaka kuti anthu azimulambira pomwe Mulungu yekha ndi amene ayenera kulambiridwa. Satana ananamiza Hava ndipo anamupangitsa kuti amvere iyeyo m’malo momvera Mulungu. Nayenso Adamu anagwirizana ndi Hava pakusamvera Mulungu. Zimene Adamu anachitazi n’zimene zapangitsa kuti anthu azivutika ndiponso kufa.​—Werengani Genesis 3:1-6, 17-19.

Zimene Satana anachita pouza Hava kuti asamvere Mulungu, zinatanthauza kuti iye akuyambitsa gulu lotsutsa ulamuliro wa Mulungu. Anthu ambiri agwirizana ndi Satana kukana ulamuliro wa Mulungu. Choncho Satana ndi “wolamulira wa dziko.”​—Werengani Yohane 14:30; Chivumbulutso 12:9.

2. Kodi vuto linali mmene Mulungu analengera anthu ndi angelo?

Anthu komanso angelo amene Mulungu analenga anali angwiro komanso anawalenga m’njira yakuti akanatha kumvera zonse zimene Mulungu ankafuna. (Deuteronomo 32:5) Mulungu anatilenga ndi ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. Chifukwa cha ufulu umenewo tingathe kusonyeza kuti timakonda Mulungu.​—Werengani Yakobo 1:13-15, 1 Yohane 5:3.

3. N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti zoipa zizichitika?

Yehova walola anthu opandukira ulamuliro wake kukhalapobe mpaka pano. Komabe zimenezi sizichitika mpaka kalekale. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti anthu opandukira ulamuliro wake akhalepobe mpaka pano? Iye wachita zimenezi pofuna kusonyeza kuti ulamuliro wa anthu sungayende bwino chifukwa Mulungu yekha ndiye woyenera kulamulira. (Yeremiya 10:23) Padutsa zaka 6,000 kuchokera pamene Satana anapandukira ulamuliro wa Mulungu ndipo zoona zake zadziwika kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Maboma a anthu alephera kuthetsa nkhondo, kuphana, kupanda chilungamo komanso matenda padzikoli.​—Werengani Mlaliki 7:29; 8:9; Aroma 9:17.

Mosiyana ndi mabomawa, anthu amene akuvomereza Mulungu kukhala Wolamulira wawo zinthu zikuwayendera bwino. (Yesaya 48:17, 18) Posachedwapa, Yehova awononga maboma onse a anthu ndipo okhawo amene asankha kulamulidwa ndi Mulungu ndi amene adzakhale padziko lapansi.​—Yesaya 2:3, 4; 11:9; werengani Danieli 2:44.

  4. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mwayi wotani?

Satana ananena kuti palibe munthu aliyense amene angakhale wokhulupirika kwa Yehova. Koma kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mwayi wosonyeza ngati timakonda ulamuliro wa Mulungu kapena wa anthu. Zimene tikuchita pa moyo wathu n’zimene zimasonyeza ngati tikusankha ulamuliro wa Mulungu kapena ayi.​—Werengani Yobu 1:8-11; Miyambo 27:11.

5. Kodi munthu amasankha bwanji Mulungu monga Wolamulira wake?

Tikamalambira Mulungu m’njira yoyenera ndiponso mogwirizana ndi Mawu ake Baibulo, ndiye kuti tikusankha Mulungu kuti akhale Wolamulira wathu. (Yohane 4:23) Komanso mofanana ndi Yesu, timapewa kulowa ndale ndiponso kumenya nawo nkhondo.​—Werengani Yohane 17:14.

Satana akugwiritsa ntchito mphamvu zake kulimbikitsa anthu kuti azichita zoipa. Ifeyo tikamakana kuchita makhalidwe amenewa, anzathu ndiponso achibale athu ena angamatinyoze kapena kutitsutsa. (1 Petulo 4:3, 4) Choncho m’pofunika kusankha. Kodi tisankha kugwirizana ndi anthu amene amakonda Mulungu? Kodi tipitiriza kumvera malamulo a Mulungu omwe ndi othandiza ndiponso achikondi? Ngati tidzachita zimenezi, tidzasonyeza kuti Satana ananama pamene ananena kuti palibe munthu amene angamvere Mulungu.​—Werengani 1 Akorinto 6:9, 10; 15:33.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 11 wa buku ili Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

Adamu anasankha kusamvera Mulungu

[Chithunzi patsamba 17]

Zimene tasankha zimasonyeza ngati tikufuna kuti Mulungu akhale Wolamulira wathu kapena ayi