NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) July 2015

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa August 31 kufika pa September 27, 2015.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Russia

Werengani kuti mumve za abale ndi alongo amene anasamukira ku Russia kuti akathandize. Ena ndi apabanja ena ayi ndipo onse aphunzira kudalira kwambiri Yehova.

Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova

Kodi paradaiso wauzimu ndi wofanana ndi kachisi wauzimu? Kodi Paulo anaona ‘paradaiso’ uti “kumwamba kwachitatu”?

Pitirizani Kutumikira Yehova ‘M’masiku Oipa’

Kodi mungatani kuti mukhalebe ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuchita khama potumikira Yehova? Werengani za atumiki achikulire a Yehova amene ankamutumikira mosangalala m’mbuyomo.

“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”

Kodi tizidzapereka uthenga wotani chisautso chachikulu chikadzayamba? N’chiyani chidzachitikira odzozedwa pa nthawiyo?

Kodi Mungadandaule Ngati Anthu Saona Ntchito Yanu?

Chitsanzo cha Bezaleli ndi Oholiabu chimatithandiza kudziwa kuti Yehova amaona ntchito yathu ngakhale ena asaone.

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Mulungu

Kodi Akhristu angadziphunzitse bwanji kukhala okhulupirika kwa Yehova?

Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova

Kodi tingalemekeze bwanji malo athu olambirira? Kodi ndalama zomangira ndiponso kukonzera Nyumba za Ufumu zimachokera kuti?

Kodi Mukudziwa?

Baibulo limasonyeza kuti m’madera ena a dziko lolonjezedwa munali mitengo yambiri. Koma masiku ano m’madera ambiri m’dzikoli mulibe mitengo. Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona?