Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungadandaule Ngati Anthu Saona Ntchito Yanu?

Kodi Mungadandaule Ngati Anthu Saona Ntchito Yanu?

BEZALELI ndi Oholiabu ankadziwa ntchito zomangamanga. Paja ali ku Iguputo, ankaumba njerwa zambirimbiri. Koma kenako anapemphedwa kuti agwire ntchito imene inkafunika luso lapadera. Anauzidwa kuti atsogolere pa ntchito yopanga chihema chopatulika. (Eks. 31:1-11) Koma anapanga zinthu zina zokongola kwambiri zimene anthu ambiri sanazione. Kodi iwo ankadandaula ndi zimenezi? Nanga inuyo mumadandaula ngati anthu saona zimene mumachita?

ANTHU OCHEPA CHABE ANKAONA ZIMENE ANAPANGA

Zinthu zina za m’chihema chopatulika zinali zokongola kwambiri. Mwachitsanzo, panali akerubi agolide amene ankakhala pamwamba pa likasa. Mtumwi Paulo ananena kuti akerubiwo anali “aulemerero” posonyeza kuti anali okongola kwambiri. (Aheb. 9:5) Kodi inuyo mukuganiza kuti akerubiwo ankaoneka bwanji?—Eks. 37:7-9.

Zinthu zimene Bezaleli ndi Oholiabu anapanga zikanakhalapobe, bwenzi anthu ambirimbiri akupita kukaziona. Koma pa nthawi imene akerubiwo anapangidwa, ndi anthu ochepa okha amene ankawaona chifukwa ankakhala m’Malo Oyera Koposa. Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kulowa m’malowo kamodzi pa chaka pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. (Aheb. 9:6, 7) Choncho iye yekha ndi amene ankaona akerubiwo.

TISAMADANDAULE NGATI ANTHU SAKUYAMIKIRA NTCHITO YATHU

Tiyerekeze kuti inuyo munali Bezaleli kapena Oholiabu ndipo mwagwira ntchitoyi mwaluso kwambiri. Kodi mukanamva bwanji mukaganizira zoti anthu ochepa chabe ndi amene angaone zinthuzo? Anthu ambiri masiku ano amamva bwino pokhapokha ngati anthu ena awayamikira chifukwa cha ntchito imene agwira. Zikatero amaona kuti ntchito yawoyo yayenda bwino. Koma atumiki a Yehova sakhala ndi maganizo amenewa. Iwo amatsanzira Bezaleli ndi Oholiabu ndipo amamva bwino akaona kuti zimene achita zasangalatsa Yehova.

Yesu ali padzikoli, atsogoleri achipembedzo ankakonda kupemphera m’njira yoti anthu ena awaone. Koma Yesu ananena kuti munthu ayenera  kupemphera kuti Yehova amve osati kuti anthu amutame. Anati munthu akapemphera m’njira yoyenera, ‘Atate wathu amene amaona kuchokera kosaoneka’ adzamuyankha. (Mat. 6:5, 6) Choncho tiyenera kupemphera kuti tisangalatse Yehova osati anthu. Tikutero chifukwa chakuti maganizo a Yehova ndi ofunika kwambiri kuposa a anthu. N’chimodzimodzi ndi zina zonse zimene timachita potumikira Mulungu. Sitiganiza kuti zayenda bwino pokhapokha ngati ena atiyamikira. M’malomwake timamva bwino tikadziwa kuti tasangalatsa Yehova amene ‘amaona kuchokera kosaoneka.’

Bezaleli ndi Oholiabu atamaliza ntchito yawo “mtambo unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho.” (Eks. 40:34) Uwu unali umboni wakuti Yehova akusangalala ndi zimene achita. Kodi mukuganiza kuti anthu awiriwa anamva bwanji izi zitachitika? Ngakhale kuti mayina awo sanalembedwe pa zinthu zimene anapangazo, iwo ayenera kuti anasangalala podziwa kuti Yehova wawadalitsa pa ntchito imene ankagwira. (Miy. 10:22) Ayenera kuti anasangalalanso kuona kuti zinthuzo zikugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri potumikira Yehova. Bezaleli ndi Oholiabu akadzaukitsidwa adzasangalala kumva kuti chihemacho chinagwiritsidwa ntchito polambira Mulungu kwa zaka pafupifupi 500.

Mwina anthu saona mukamagwira ntchito modzichepetsa ndiponso mwakhama koma Yehova amaona

M’gulu la Yehova mulinso anthu amene amapanga mavidiyo, kukonza nyimbo, kujambula zithunzi, kulemba ndiponso kumasulira mabuku. Mayina a anthu amene amachita zinthu ngati zimenezi sadziwika. Choncho zili ngati anthu saona zimene amachita. Ndi mmene zililinso m’mipingo yoposa 110,000 padziko lonse. Abale ena akamalemba mapepala okhudza ndalama za mpingo sitiwaona. Sitionanso alembi akulemba lipoti la utumiki. Mwinanso sitiona abale ndi alongo ena akugwira ntchito zokonza pa Nyumba ya Ufumu.

Bezaleli ndi Oholiabu sanapatsidwe mamendulo kapena zikalata zosonyeza kuti anagwira ntchito zotamandika. Koma chofunika kwambiri n’chakuti Yehova ankaona zimene anthuwa anachita ndipo ankasangalala nazo. Tiyeni tonse tiziwatsanzira ndipo tizitumikira Yehova modzichepetsa komanso mwakhama.