Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Russia

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Russia

MU 1991, a Mboni za Yehova anasangalala kwambiri boma la Russia litachotsa bani yomwe inalipo kwa nthawi yaitali. Pa nthawiyo, abale ambiri sankayembekezera kuti chiwerengero cha ofalitsa chingafike pa 170,000. Koma pali abale ndi alongo ambiri amene anasamukira ku Russia kuti akathandize pa ntchito yolalikira. (Mat. 9:37, 38) Tiyeni timve zomwe ena mwa iwo anena.

ABALE ADZIPEREKA KUKATHANDIZA MIPINGO

M’bale wina wa ku Great Britain dzina lake Matthew anali ndi zaka 28 pamene bani inkachotsedwa ku Russia. Chaka chimenecho pa msonkhano wina, panakambidwa nkhani imene inafotokoza kuti pakufunika anthu oti akathandize m’mipingo ya kum’mawa kwa Europe. Wokamba nkhaniyo ananena kuti mpingo wina wa mumzinda wa St. Petersburg ku Russia uli ndi mtumiki wothandiza mmodzi ndipo ulibiretu akulu. Koma ofalitsa a mumpingowo ali ndi maphunziro ambirimbiri. Matthew ananena kuti: “Nditamva nkhaniyo ndinkaganizira kwambiri za ku Russia ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kusamukira kumeneko.” Iye anayamba kusunga ndalama komanso anagulitsa katundu wake wambiri ndipo mu 1992 anasamukira ku Russia. Kodi zinthu zinamuyendera bwanji?

Matthew

Matthew ananena kuti: “Vuto loyamba linali chilankhulo ndipo ndinkavutika kulalikira bwinobwino.” Vuto lina linali malo ogona. Iye ananenanso kuti: “Nthawi zambiri ndinkauzidwa kusamuka mwadzidzidzi.” Ngakhale kuti ankakumana ndi mavutowa, Matthew anati: “Ndinachita bwino kwambiri kusamukira kuno ku Russia.” Iye anafotokozanso kuti: “Kutumikira kuno kwandithandiza kuti ndizidalira kwambiri Yehova ndipo ndaona kuti akundithandizadi.” Kenako Matthew anakhala mkulu ndiponso mpainiya wapadera ndipo tsopano akutumikira pa nthambi ya m’dzikoli.

Mu 1999, m’bale wina wa ku Japan dzina lake Hiroo anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Pa nthawiyi anali ndi zaka 25 ndipo mlangizi wake wina anamulimbikitsa kuti akatumikire kudziko lina.  Hiroo atamva kuti ku Russia kukufunika anthu ambiri olalikira, anayamba kuphunzira Chirasha. Pofuna kuti aone ngati angakwanitse kukakhala ku Russia, anapita kukakhala m’dzikoli kwa miyezi 6. Iye anati: “Popeza kuti kumazizira kwambiri kuyambira mu November, ndinakonza zopitako m’mwezi umenewu kuti ndikaone ngati ndingakwanitse.” Atakhala miyezi 6 anabwerera ku Japan ndipo anayamba kukhala moyo wosafuna zinthu zambiri n’cholinga choti asunge ndalama zokwanira kuti asamukire ku Russia.

Hiroo ndi Svetlana

Tsopano Hiroo wakhala ku Russia kwa zaka 12 ndipo watumikira m’mipingo yosiyanasiyana. Nthawi zina, iye ankakhala mkulu mmodzi yekha mumpingo wa ofalitsa oposa 100. Mumpingo wina, mlungu uliwonse ankakamba nkhani zambiri mu Msonkhano wa Utumiki, ankachititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso Maphunziro a Buku a Mpingo okwana 5. Iye ankachitanso maulendo aubusa ambirimbiri. Ponena za nthawi imeneyo, Hiroo anati: “Ndinkasangalala kwambiri kuthandiza abale ndi alongo kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova.” Kodi kusamukaku kunamuthandiza bwanji? Iye anati: “Ndisanasamukire ku Russia ndinali mkulu ndiponso mpainiya koma pamene ndasamukira kuno ndikuona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri. Ndaphunzira kumudalira pa zochita zanga zonse.” Mu 2005, Hiroo anakwatira mlongo wina dzina lake Svetlana ndipo akuchitirabe limodzi upainiya.

Michael, Olga, Marina ndi Matthew

Chitsanzo china ndi cha abale awiri ochokera ku Canada. Wina dzina lake Matthew ali ndi zaka 34 ndipo mng’ono wake dzina lake Michael ali ndi zaka 28. Iwo anapita ku Russia ndipo anaona kuti anthu ambiri ankafika ku misonkhano koma panali abale ochepa oti achititse misonkhanoyo. Matthew anati: “Mumpingo wina anthu 200 anafika pa misonkhano koma panali mkulu mmodzi wachikulire ndi mtumiki wothandiza mmodzi wachinyamata amene ankachititsa misonkhano yonse. Nditaona zimenezi ndinayamba kuganizira zokathandiza kumeneko.” Iye anasamukira ku Russia mu 2002.

Patapita zaka 4, Michael anasamukiranso ku Russia ndipo anaonadi kuti kulibe abale okwanira. Popeza anali mtumiki wothandiza, ankayang’anira ndalama za mpingo, mabuku ndiponso magawo. Ankapemphedwanso kugwira ntchito za mlembi, kukamba nkhani za onse, kuthandiza pokonzekera misonkhano ikuluikulu ndiponso pomanga Nyumba za Ufumu. Ngakhale masiku ano pakufunikabe abale ambiri kuti akathandize m’mipingo yosiyanasiyana. N’zoona kuti kugwira ntchito zosiyanasiyana si kophweka, koma Michael anati: “Ndimasangalala kwambiri kuthandiza abale ndi alongo. Ndimaona kuti palibe ntchito yabwino kwambiri kuposa imene ndikugwirayi.”

Matthew anakwatira mlongo wina dzina lake Marina. Nayenso Michael, yemwe panopa ndi mkulu, anakwatira mlongo wina dzina lake Olga. Mabanja awiriwa ndiponso mabanja ena ambiri akuthandizabe mipingo ya ku Russia imene ikuwonjezeka.

ALONGO AKUTHANDIZA KWAMBIRI PA NTCHITO YOLALIKIRA

Tatyana

Mu 1994, apainiya apadera 6 anasamukira mumpingo wina ku Ukraine. Iwo anali ochokera m’dziko la Czech Republic, Poland ndi Slovakia. Mumpingowo munali mtsikana wina wazaka 16 dzina lake Tatyana. Iye ankakonda kwambiri apainiyawa ndipo anati: “Iwo anali akhama kwambiri, ochezeka, okoma mtima ndipo ankadziwa bwino Baibulo.” Iye anaona kuti Yehova ankawadalitsa chifukwa cha kudzipereka kwawo. Tatyana ankafuna kutsatira chitsanzo chawo.

Chifukwa cholimbikitsidwa ndi apainiyawa, iye akakhala pa holide ankapita kumadera akutali kukalalikira. Ankapita kumadera a m’dziko la Ukraine komanso la Belarus kumene a Mboni sanalalikirepo. Tatyana anasangalala kwambiri ndi maulendowo moti anayamba kuganiza zosamukira ku Russia. Poyamba, anapita  kumeneko kwa nthawi yochepa kuti akacheze ndi mlongo wina amene anasamukirako. Pa ulendowu anafufuzanso ntchito imene ingamuthandize pochita upainiya. Kenako mu 2000, anasamuka. Kodi anakumana ndi mavuto ati?

Tatyana anati: “Ndinali ndi ndalama zochepa choncho ndinkangochita lendi chipinda cha m’nyumba ya anthu ena. Kukhala m’nyumba ya eniake kunali kovuta moti nthawi zina ndinkafuna kubwerera kwathu. Koma Yehova ankandithandiza kuona kuti ndikapitiriza utumiki wanga ndipeza madalitso.” Panopa Tatyana ndi mmishonale ku Russia. Iye anati: “Pa zaka zonse zimene ndatumikira kuno ndaphunzira zinthu zambiri zabwino ndiponso ndapeza anzanga ambiri. Koma chofunika kwambiri n’chakuti chikhulupiriro changa chalimba.”

Masako

Mlongo wina wa ku Japan dzina lake Masako ankafunitsitsa kuchita umishonale koma ankakayikira zoti angakwanitse chifukwa choti ankadwaladwala. Koma atayamba kupezako bwino anaganiza zosamukira ku Russia. Zinali zovuta kuti apeze nyumba yabwino komanso ntchito. Koma anayamba kuphunzitsa Chijapanizi ndiponso kugwira ntchito yoyeretsa. Kodi n’chiyani chamuthandiza kupitiriza utumiki wake?

Panopa, Masako ali ndi zaka zoposa 50 ndipo watumikira ku Russia kwa zaka 14. Iye anati: “Mavuto amene ndakumana nawo ndi ochepa ndikawayerekezera ndi madalitso amene ndapeza mu utumiki. Munthu ukamalalikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri zimasangalatsa kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Kunena zoona Yehova wandichitira zodabwitsa. Ndaona akundithandiza kupeza chakudya, zovala ndi malo ogona pa zaka zonsezi.” Masako anatumikiranso m’dziko la Kyrgyzstan ndipo anathandizanso m’timagulu ta Chingelezi, Chitchainizi ndi Chiwigera. Panopa mlongoyu akuchita upainiya ku St. Petersburg.

MABANJA ADALITSIDWA CHIFUKWA CHODZIPEREKA

Inga ndi Mikhail

Mabanja ambiri amasamukira kudziko lina n’cholinga choti akapeze ntchito yabwino. Koma mabanja ena amatsatira chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara ndipo  amasamukira kudziko lina kuti akathandize pa ntchito yolalikira. (Gen. 12:1-9) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi banja la Mikhail ndi Inga. Iwo anachoka ku Ukraine n’kupita ku Russia mu 2003. Pasanapite nthawi, anapeza anthu ofuna kuphunzira za Mulungu.

Mikhail anati: “Tsiku lina tinakalalikira kudera limene chiyambire sikunafike a Mboni. Panyumba ina bambo wachikulire anatuluka n’kunena kuti, ‘Kodi mwabwera kudzalalikira?’ Titayankha kuti inde, ananena kuti: ‘Ndimadziwa kuti tsiku lina mufika basi. Mawu a Yesu sangakhale osakwaniritsidwa.’ Kenako bamboyo anatchula mawu a pa Mateyu 24:14.” Mikhail ananenanso kuti: “Kudera limeneli tinapezanso gulu la azimayi a mpingo wa Baptist amene ankafuna kuphunzira Baibulo. Iwo anali ndi buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha ndipo mlungu uliwonse ankaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito bukulo. Tinayankha mafunso awo kwa maola ambiri, tinaimba nawo nyimbo ndipo pomaliza tinadya chakudya. Ulendo umenewu tinasangalala kwambiri ndipo ndi wosaiwalika.” Mikhail ndi Inga akuona kuti kutumikira kudera limene kulibe ofalitsa okwanira kwawathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova, kukonda kwambiri anthu ndiponso kukhala osangalala. Panopa banjali likugwira ntchito yoyang’anira dera.

Oksana, Aleksey, ndi Yury

Mu 2007, m’bale wina wa ku Ukraine dzina lake Yury ndi mkazi wake dzina lake Oksana anapita kukaona ofesi ya nthambi ku Russia. Anali limodzi ndi mwana wawo dzina lake Aleksey. Atafika anaona mapu a dzikolo ndipo anapeza kuti pali madera ambiri kumene kulibe ofalitsa. Oksana anati: “Titangoona mapuwo tinazindikira kuti pakufunika anthu ambiri okathandiza m’maderawo. Izi zinachititsa kuti tiganize zosamukira ku Russia.” Koma panali chinthu chinanso chimene chinawathandiza. Yury anati: “Tinkawerenga nkhani za m’magazini athu monga yakuti ‘Kodi Mungakatumikire Kudziko Lina?’ * Ndiyeno ofesi ya nthambi inatiuza dera limene tingakatumikire ndiyeno tinapita kukaonako n’cholinga choti tipezeretu nyumba ndi ntchito.” Mu 2008, iwo anasamukira ku Russia.

Poyamba, ntchito zinkasowa kwambiri ndipo tinkangokhalira kusamukasamuka m’nyumba. Yury anati: “Tinkakonda kupemphera kuti tisafooke ndipo tinkangopitiriza kulalikira podziwa kuti Yehova atithandiza. Iye anatithandizadi chifukwa chakuti tinkaika zinthu zokhudza Ufumu pa malo oyamba. Kunena zoona utumikiwu unathandizanso banja lathu kuti likhale logwirizana.” (Mat. 6:22, 33) Kodi kukatumikira kudera lina kwathandiza bwanji Aleksey? Oksana anati: “Nayenso wamuthandiza kwambiri. Anadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa ali ndi zaka 9. Iye ataona kuti pakufunika anthu ambiri olalikira, anayamba kuchita upainiya wothandiza pa holide iliyonse. Timasangalala kuona mwana wathu akukonda kwambiri utumiki.” Panopa banjali lili ndi zaka za m’ma 30 ndipo likuchita upainiya wapadera. Mwana wawoyu ali ndi zaka 13.

“KODI NDIMACHEDWA KUTI?”

Zimene abale ndi alongo anena m’nkhaniyi zimasonyeza kuti munthu akasamukira kudera lina amafunika kudalira kwambiri Yehova. N’zoona kuti amakumana ndi mavuto ena koma amasangalala chifukwa cholalikira anthu ofuna kumva uthenga wa Ufumu. Kodi inuyo mungakwanitse kupita kudera limene kulibe ofalitsa okwanira? Mukasankha kuchita zimenezi mudzakhala ndi maganizo ofanana ndi a Yury. Iye anati: “Ndimangodzifunsa kuti, kodi ndimachedwa kuti?”

^ ndime 20 Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999, tsamba 23 mpaka 27.