NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) November 2014

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa December 29, 2014 mpaka pa February 1, 2015.

Kodi Kuuka kwa Yesu Kumatithandiza Bwanji?

Pali zifukwa zinayi zotsimikizira kuti Yesu anauka. Kodi kudziwa zoti Yesu ali moyo kungatithandize bwanji?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oyera?

Kodi mumavutika kuwerenga buku la Levitiko? Mfundo zofunika za m’bukuli zingakuthandizeni kukhala oyera polambira Mulungu.

Tikhale Oyera M’makhalidwe Athu Onse

N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza mfundo za Yehova? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupatsa Yehova zonse zimene tingathe komanso kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo?

“Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”

Kodi Mulungu amaona kuti anthu ake okhulupirika amapezeka m’zipembedzo zosiyanasiyana?

“Tsopano Ndinu Mtundu wa Anthu a Mulungu”

Kodi tingatani kuti tilowe m’gulu la anthu a Mulungu? Nanga tingatani kuti tisachokemo?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi akulu ndi atumiki othandiza amaikidwa bwanji mumpingo? Kodi Mboni Ziwiri za M’chaputala 11 cha Chivumbulutso Ndi Ndani?

KALE LATHU

Uthenga Wabwino Unayamba Kuwala ku Japan

Makalavani otchedwa Yehu ankathandiza kwambiri polalikira uthenga wa Ufumu ku Japan.