Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsopano Ndinu Mtundu wa Anthu a Mulungu”

“Tsopano Ndinu Mtundu wa Anthu a Mulungu”

“Kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.”—1 PET. 2:10.

1, 2. (a) Kodi zinthu zinasintha bwanji pa Pentekosite mu 33 C.E.? (b) Kodi ndani anakhala mtundu watsopano wa anthu a Yehova? (Onani chithunzi pamwambapa.)

PA PENTEKOSITE mu 33 C.E. zinthu zinasintha kwambiri m’gulu la Yehova. Pa tsikuli, Yehova anadzoza anthu ena ndi mzimu woyera kuti akhale mtundu watsopano womwe umatchedwa Isiraeli wauzimu kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Kuyambira nthawi ya Abulahamu, mdulidwe unali chizindikiro cha anthu a Mulungu koma pa nthawiyi zinthu zinasintha. Ponena za anthu a mu mtundu watsopanowu, Paulo analemba kuti: “Mdulidwe wake ndi wa mumtima wochitidwa ndi mzimu.”—Aroma 2:29.

2 Atumwi ndi anthu ena oposa 100, amene anasonkhana m’chipinda cham’mwamba ku Yerusalemu, ndi amene anali oyambirira kukhala mu mtundu watsopanowu. (Mac. 1:12-15) Anthuwa anadzozedwa ndi mzimu woyera n’kukhala ana a Mulungu. (Aroma 8:15, 16; 2 Akor. 1:21) Umenewu unali umboni wakuti pangano latsopano layamba kugwira ntchito. Mkhalapakati wa panganoli ndi Yesu ndipo magazi ake ndi amene anachititsa kuti liyambe kugwira ntchito. (Luka 22:20;  werengani Aheberi 9:15.) Anthu amene anadzozedwawa anakhala mtundu watsopano wa anthu a Yehova. Mzimuwo unawathandiza kulankhula ndiponso kumva zilankhulo zosiyanasiyana za anthu amene anabwera kudzachita chikondwerero cha Pentekosite. Choncho anatha kuphunzitsa anthuwo “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Mac. 2:1-11.

MTUNDU WATSOPANO WA ANTHU A MULUNGU

3-5. (a) Kodi Petulo anauza chiyani Ayuda pa tsiku la Pentekosite? (b) Kodi mtundu watsopano wa Yehova unakula bwanji kuchokera pa Pentekosite?

3 Yehova anagwiritsa ntchito Petulo potsegula njira yoti Ayuda ndiponso anthu olowa Chiyuda akhale mu mtundu watsopanowu kapena kuti mumpingo wa Akhristu odzozedwa. Pa Pentekosite, Petulo anauza Ayuda kuti ayenera kukhulupirira Yesu, yemwe iwo ‘anamukhomerera pamtengo,’ chifukwa “Mulungu anamuika kukhala Ambuye ndi Khristu.” Ayudawo atafunsa Petulo zimene ayenera kuchita, iye anati: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.” (Mac. 2:22, 23, 36-38) Pa tsikulo, anthu pafupifupi 3,000 anakhala mu mtundu watsopano wa Isiraeli wauzimu. (Mac. 2:41) Pambuyo pake, atumwi anapitiriza kulalikira mwakhama ndipo anthu ambiri analowa mu mtundu watsopanowu.—Mac. 6:7.

4 Kenako Akhristuwo anayamba kulalikiranso kwa Asamariya ndipo ambiri analowanso mu mtunduwu. Filipo anabatiza Asamariya ambiri koma iwo sanalandire mzimu woyera nthawi yomweyo. Ndiyeno bungwe lolamulira ku Yerusalemu linatumiza Petulo ndi Yohane kwa Asamariyawo. Atafika, “anayamba kuika manja awo pa anthuwo, ndipo analandira mzimu woyera.” (Mac. 8:5, 6, 14-17) Choncho Asamariyawo anadzozedwa n’kukhala mu mtundu wa Isiraeli wauzimu.

Petulo analalikira kwa Koneliyo ndi anthu a m’nyumba yake (Onani ndime 5)

5 Mu 36 C.E., Yehova anagwiritsanso ntchito Petulo kuti athandize anthu ena kulowa mu mtundu watsopanowu. Anachita zimenezi pamene analalikira kwa Koneliyo ndi achibale ake komanso anzake. Koneliyo anali kazembe wankhondo wachiroma. (Mac. 10:22, 24, 34, 35) Baibulo limati: “Pamene Petulo anali kulankhula . . . , mzimu woyera unagwa pa [anthu a mitundu ina] onse amene anali kumvera mawu amenewo. Ndipo okhulupirika amene anabwera ndi Petulo, amene anali odulidwa anadabwa, chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inalinso kuthiridwa pa anthu a mitundu ina.” (Mac. 10:44, 45) Choncho anthu osadulidwa a mitundu ina analoledwanso kukhala mu mtundu wa Isiraeli wauzimu.

“ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LAKE”

6, 7. Kodi mtundu watsopanowo unasonyeza bwanji kuti ndi wa ‘anthu odziwika ndi dzina la Yehova’?

6 Pa msonkhano wa bungwe lolamulira mu 49 C.E., Yakobo ananena kuti: “Sumeoni  [Petulo] wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Anthu odzakhala m’gululi anali Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina. (Aroma 11:25, 26a) Kenako Petulo analemba kuti: “Kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.” Iye anafotokozanso ntchito yawo ponena kuti: “Ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri’ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9, 10) Iwo anayenera kulengeza za Yehova komanso kumutamanda chifukwa chakuti iye ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse.

7 Mofanana ndi Aisiraeli akale, Yehova anasankha Isiraeli wauzimu kuti akhale ‘anthu ake, komanso kuti anene za ulemerero wake.’ (Yes. 43:21) Akhristuwo ankasonyeza kuti milungu ina ndi yabodza ndipo ankauza anthu za Yehova Mulungu woona. (1 Ates. 1:9) Iwo anachitira umboni za Yehova ndi Yesu “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Mac. 1:8; Akol. 1:23.

8. Kodi Paulo anachenjeza anthu a Mulungu za chiyani?

8 Mtumwi Paulo anali m’gulu la ‘anthu odziwika ndi dzina la Yehova’ ndipo anali mboni yolimba mtima kwambiri. Iye analankhula mopanda mantha za ulamuliro wa Yehova pamene ankalalikira kwa anthu ophunzira kwambiri amene sankalambira Mulungu. Iye anati Yehovayo ndi “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu . . . Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” (Mac. 17:18, 23-25) Koma chakumapeto kwa ulendo wake wachitatu waumishonale, Paulo anauza anthu ena a mu mtundu watsopanowu kuti: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (Mac. 20:29, 30) Mpatuko umene analoserawu unayamba kuonekera chaka cha 100 C.E. chisanafike.—1 Yoh. 2:18, 19.

9. Kodi chinachitika n’chiyani atumwi atamwalira?

9 Atumwi atamwalira, anthu ampatuko anachuluka kwambiri moti n’zimene zinachititsa kuti pakhale matchalitchi ambiri amene amati ndi achikhristu. M’malo mosonyeza kuti ndi ‘anthu odziwika ndi dzina la Mulungu,’ anthu a m’matchalitchiwa anachotsa dzina lake m’Mabaibulo awo ambiri. Iwo anayamba kutengera miyambo ya anthu osalambira Mulungu. Amanyozetsanso dzina la Mulungu pophunzitsa zinthu zabodza, kumenya nkhondo m’dzina la Mulunguyo komanso kuchita zinthu zina zoipa. Choncho kwa zaka zambiri, anthu olambira Yehova anali ochepa chabe ndipo panalibe gulu ‘lodziwika ndi dzina lake.’

MULUNGU ANASONKHANITSANSO ANTHU AKE

10, 11. (a) Kodi Yesu analosera za chiyani m’fanizo lake la tirigu ndi namsongole? (b) Kodi fanizo la Yesu linakwaniritsidwa bwanji?

10 M’fanizo lake lonena za tirigu ndi namsongole, Yesu analosera kuti mpatukowo udzachititsa kuti Akhristu oona asadziwike bwinobwino. Iye ananena kuti “anthu ali m’tulo,” Mdyerekezi adzabwera kudzafesa namsongole m’munda umene Mwana wa munthu anafesa tirigu. Ananenanso kuti tirigu ndi namsongoleyo adzakulira limodzi mpaka “pa mapeto a nthawi ino.” Yesu anafotokoza kuti “mbewu zabwino” zikuimira  “ana a ufumu” ndipo “namsongole” akuimira “ana a woipayo.” Ananenanso kuti pa mapeto a nthawi ino, Mwana wa Mulungu adzatumiza “okolola,” kapena kuti angelo, kuti asiyanitse tirigu ndi namsongole. Ndiyeno ana a Ufumu adzasonkhanitsidwa. (Mat. 13:24-30, 36-43) Kodi fanizoli linakwaniritsidwa bwanji?

11 “Mapeto a nthawi ino” anayamba mu 1914. M’chakachi, nkhondo inayamba ndipo padzikoli panali Akhristu odzozedwa masauzande ochepa chabe. Pa nthawiyi, odzozedwawa, kapena kuti “ana a ufumu,” anali adakali mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. Koma mu 1919, Yehova anawamasula ku ukapolowo n’kuwasiyanitsa ndi “namsongole,” kapena kuti Akhristu onyenga. Iye anasonkhanitsa “ana a ufumu” kuti akhale m’gulu lake ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa Yesaya wakuti: “Kodi dziko limatulutsidwa ndi zowawa za pobereka tsiku limodzi lokha? Kapena kodi mtundu umabadwa nthawi imodzi? Pakuti Ziyoni wamva zowawa za pobereka ndipo wabereka ana ake aamuna.” (Yes. 66:8) M’lembali, Ziyoni akuimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Ndiyeno Ziyoniyo anabereka ana ake aamuna pamene odzozedwawo anasonkhanitsidwanso n’kukhala m’gulu la Yehova.

12. Kodi masiku ano odzozedwa asonyeza bwanji kuti ndi ‘anthu odziwika ndi dzina la Yehova’?

12 Mofanana ndi Akhristu oyambirira, ‘ana a ufumuwo’ amachitira umboni za Yehova. (Werengani Yesaya 43:1, 10, 11.) Choncho amakhala osiyana ndi ena chifukwa cha khalidwe lawo labwino ndiponso ntchito yawo yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:14; Afil. 2:15) Chifukwa cha zimenezi, athandiza anthu ambirimbiri kuti akhale olungama pamaso pa Yehova.—Werengani Danieli 12:3.

“TIPITA NANU LIMODZI”

13, 14. (a) Kodi anthu omwe si odzozedwa ayenera kuchita chiyani kuti azilambira Yehova m’njira yovomerezeka? (b) Kodi Baibulo linalosera bwanji zimenezi?

13 Mu nkhani yapita ija, tinaona kuti anthu  a mitundu ina ankafunika kugwirizana ndi anthu a Yehova kuti ayambe kumulambira m’njira yovomerezeka. (1 Maf. 8:41-43) Masiku anonso, anthu amene si odzozedwa ayenera kugwirizana ndi “ana a ufumu” omwe ndi Akhristu odzozedwa.

14 Aneneri awiri analosera zoti anthu ambiri adzakhamukira m’gulu la Yehova. Yesaya analosera kuti: “Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: ‘Bwerani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.’ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.” (Yes. 2:2, 3) Nayenso mneneri Zekariya analosera kuti: “Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu ya anthu idzabweradi kudzafunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu. Idzabwera kudzakhazika pansi mtima wa Yehova.” Pofotokoza za anthuwo, iye anati: “Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” adzayamba kulambira Mulungu limodzi ndi Aisiraeli auzimu. Anati iwo adzanena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zek. 8:20-23.

15. Kodi a “nkhosa zina” ‘amapita limodzi’ ndi odzozedwa kukagwira ntchito iti?

15 A “nkhosa zina” ‘amapita limodzi’ ndi odzozedwa kukalalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Maliko 13:10) Iwo amakhala ‘m’gulu limodzi’ ndi odzozedwawo n’kumatsogoleredwa ndi Khristu Yesu, yemwe ndi “m’busa wabwino.”—Werengani Yohane 10:14-16.

KHALANI OTETEZEKA M’GULU LA YEHOVA

16. Kodi Yehova adzachita chiyani kuti mbali yomaliza ya “chisautso chachikulu” iyambe?

16 M’tsogolomu tidzayenera kutetezedwa ndi Yehova chifukwa chakuti Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, anthu a Yehova adzaukiridwa modetsa nkhawa. Pa nthawi yake, Yehova adzachititsa kuti nkhondo ya Aramagedo, yomwe ndi mbali yomaliza ya “chisautso chachikulu,” iyambe. (Mat. 24:21; Ezek. 38:2-4) Pa nthawiyo, Gogi adzaukira “anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina.” (Ezek. 38:10-12) Ndiyeno Gogi ndi anzake akadzangochita zimenezi, Yehova adzalowerera n’kumenyana nawo kuti alanditse anthu ake. Iye adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira ndiponso adzayeretsa dzina lake. Paja iye anati: ‘Ndidzachititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’—Ezek. 38:18-23.

Pa nthawi ya “chisautso chachikulu” tidzafunika kugwirizana kwambiri ndi mpingo wathu (Onani ndime 16 mpaka 18)

17, 18. (a) Kodi anthu a Yehova adzalandira malangizo otani akadzaukiridwa ndi Gogi? (b) Ngati tikufuna kudzatetezedwa ndi Yehova, kodi tiyenera kuchita chiyani?

17 Gogi akadzayamba kutiukira, Yehova adzatiuza kuti: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Pa nthawi yovutayi, Yehova adzatipatsa malangizo amene angatipulumutse. N’kutheka kuti ‘zipinda zamkatizi’ zikuimira zinthu zina zokhudza mipingo yathu.

18 Choncho ngati tikufuna kudzapulumuka pa chisautso chachikulu, tiyenera kuzindikira kuti Yehova ali ndi gulu lake padzikoli. Tiyenera kupitiriza kukhala m’gululi ndiponso kugwirizana ndi mpingo wathu. Tiyeni tonse tizitsanzira wamasalimo yemwe analengeza ndi mtima wonse kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso anu ali pa anthu anu.”—Sal. 3:8.