NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) August 2014

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 29 mpaka October 26, 2014.

Kodi Mukulandira “Chakudya pa Nthawi Yoyenera?”

Kodi munthu ayenera kukhala ndi mabuku onse ochokera kwa kapolo wokhulupirika kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunakhudzira amuna ndi akazi. M’nkhaniyi tafotokoza za akazi ena akale omwe anali okhulupirika. Komanso muona zimene akazi achikhristu akuchita masiku ano potumikira Mulungu.

Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Chifukwa Ndi Amoyo

A Mboni za Yehova onse amafuna kuti azilalikira mogwira mtima. Onani zimene tingachite kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu komanso timapepala pokambirana ndi anthu.

Zimene Yehova Wachita Kuti Tiyandikane Naye

Tiyenera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. M’nkhaniyi muona kuti dipo komanso Baibulo zimasonyeza kuti Yehova amafuna kuti tiyandikane naye.

Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse

Werengani kuti muone ubwino womvetsera mawu a Yehova komanso kupemphera nthawi zonse. Nkhaniyi itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tisasokonezedwe ndi Satana komanso mtima wathu n’kusiya kumvetsera Yehova.

‘Ubwerere Ukalimbikitse Abale Ako’

Kodi m’bale amene wasiya kutumikira monga mkulu ‘angayesetse kuti akhalenso woyang’anira’?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Pamene Yesu ananena kuti anthu oukitsidwa “sadzakwatira kapena kukwatiwa,” kodi ankanena za anthu amene adzakhale padzikoli?

KALE LATHU

Sewero Limene Linathandiza Ambiri Kuphunzira Baibulo

Anthu ankatha kuonetsa chidule cha “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” kumadera akutali ngakhale kumene kunalibe magetsi.