Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Yehova Wachita Kuti Tiyandikane Naye

Zimene Yehova Wachita Kuti Tiyandikane Naye

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—YAK. 4:8.

1. Kodi anthufe timafunitsitsa kugwirizana ndi ndani?

TONSEFE timafunitsitsa kugwirizana kwambiri ndi anthu ena. Anthu amakhala ogwirizana kwambiri ngati amakondana ndiponso kudziwana bwino. Timamva bwino kwambiri ngati timagwirizana ndi achibale komanso anzathu amene amatikonda, kutiyamikira ndiponso kutimvetsa. Koma Mlengi wathu Wamkulu ndi amene tiyenera kukhala naye pa ubwenzi wabwino kuposa wina aliyense.—Mlal. 12:1.

2. (a) Kodi Yehova amalonjeza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti zimenezi n’zosatheka?

2 Yehova amatilimbikitsa m’Mawu ake kuti ‘timuyandikire’ ndipo amalonjeza kuti tikachita zimenezi nayenso ‘adzatiyandikira.’ (Yak. 4:8) Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri. Koma anthu ambiri amaganiza kuti zimenezi n’zosatheka. Iwo amaona kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri ndipo iwo ndi osayenera kumuyandikira. Koma kodi n’zothekadi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?

3. Kodi tiyenera kuzindikira mfundo iti yokhudza Yehova?

3 Yehova “sali kutali ndi aliyense” amene akufunitsitsa kumudziwa. (Werengani Machitidwe 17:26, 27; Salimo 145:18.)  Mulungu wathu akufuna kuti ngakhale anthu ochimwafe tikhale naye pa ubwenzi wolimba. (Yes. 41:8; 55:6) Wamasalimo ankadziwa bwino zimenezi ndipo analemba kuti: “Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu. Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu.” (Sal. 65:2, 4) Nkhani ya m’Baibulo yokhudza Mfumu Asa ya Yuda imasonyeza zimene Mulungu amachita munthu akamuyandikira. *

ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA ASA

4. Kodi Asa anapereka chitsanzo chotani kwa Ayuda?

4 Mfumu Asa anasonyeza kuti ankafunitsitsa kulambira koyera. Iye anachotsa mahule a pakachisi komanso mafano amene anthu ankalambira. (1 Maf. 15:9-13) Atatero, anali ndi ufulu wouza anthu onse kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo.” Yehova anapatsa Ayuda mtendere pa zaka 10 zoyambirira za ulamuliro wa Asa. Kodi Asa anati mtenderewo wabwera chifukwa chiyani? Iye anauza anthu ake kuti: “Malo m’dzikoli akadalipo chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu. Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulira.” (2 Mbiri 14:1-7) Tiyeni tione zimene zinachitika pambuyo pake.

5. Kodi Asa anakumana ndi vuto liti, ndipo linatha bwanji?

5 Tayerekezerani kuti inuyo munali Asa. Ndiye Zera wa ku Itiyopiya akubwera ku Yuda ndi asilikali 1 miliyoni komanso magaleta 300. (2 Mbiri 14:8-10) Kodi mukanatani poona kuti asilikali anu alipo 580,000 okha ndipo tingati ndi hafu chabe ya adani anuwo? Mwina mukanadzifunsa kuti kodi Yehova akuloleranji kuti izi zichitike? Kodi mukanayamba kuchita zinthu modalira nzeru zanu basi? Zimene Asa anachita zimasonyeza kuti anali pa ubwenzi ndi Yehova ndipo ankamudalira kwambiri. Iye anapemphera kuchokera pansi pa mtima kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu, ndipo tabwera m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.” Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero la Asa? Iye “anagonjetsa Aitiyopiyawo” ndipo palibe mdani ngakhale mmodzi amene anapulumuka.—2 Mbiri 14:11-13.

6. Kodi tingatsanzire bwanji Asa?

6 N’chiyani chinathandiza Asa kukhulupirira kuti Mulungu amutsogolera komanso kumuteteza? Baibulo limanena kuti “Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova” ndipo “anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:11, 14) Ifenso tiyenera kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu. Zimenezi n’zofunika kwambiri ngati tikufuna kuti tikhale naye pa ubwenzi panopa mpaka m’tsogolo. Timayamikira kwambiri kuti Yehova wachita zinthu zothandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene wachita.

YEHOVA ANAPEREKA DIPO KUTI TIYANDIKANE NAYE

7. (a) Kodi Yehova wachita chiyani potithandiza kuti tiyandikane naye? (b) Kodi chinthu chachikulu chimene Yehova wachita kuti tiyandikane naye n’chiyani?

7 Yehova anasonyeza kuti amatikonda potilengera dziko lokongolali. Iye amasonyezabe chikondichi potipatsa zinthu zofunika pa moyo wathu. (Mac. 17:28; Chiv. 4:11) Koma chofunika kwambiri n’chakuti amatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. (Luka 12:42) Iye amatitsimikiziranso kuti amamvetsera mapemphero athu. (1 Yoh. 5:14) Koma chinthu chachikulu chimene  wachita kuti tiyandikane naye ndi kupereka dipo. (Werengani 1 Yohane 4:9, 10, 19.) Yehova anatumiza “Mwana wake wobadwa yekha” kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa.—Yoh. 3:16.

8, 9. Kodi Yesu ali ndi udindo wotani pokwaniritsa cholinga cha Yehova?

8 Yehova wakonza zoti dipo lithandizenso anthu amene anakhalapo Khristu asanabwere. Yehova atangolosera kuti kudzabwera Mpulumutsi, zinali ngati dipo laperekedwa kale. Zinali choncho chifukwa Mulungu ankadziwa kuti cholinga chake sichingalephereke. (Gen. 3:15) Patapita zaka zambirimbiri, mtumwi Paulo anayamikira Mulungu chifukwa chomasula anthu “ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.” Iye ananenanso kuti Mulungu ankakhululuka “machimo amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga.” (Aroma 3:21-26) Choncho Yesu ali ndi udindo wapadera potithandiza kuti tiyandikane ndi Mulungu.

9 Anthu odzichepetsa angadziwe Mulungu n’kukhala naye pa ubwenzi ngati atakhulupirira Yesu. Kodi Malemba amasonyeza bwanji zimenezi? Paulo analemba kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:6-8) Mulungu anapereka nsembe ya dipo ya Yesu chifukwa chotikonda kwambiri osati chifukwa chakuti ndife oyenerera. Yesu anati: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” Pa nthawi inanso anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 6:44; 14:6) Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti akoke anthu kudzera mwa Yesu ndipo amawathandiza kuchita zinthu zoyenera kuti akapeze moyo wosatha. (Werengani Yuda 20, 21.) Tiyeni tione chinthu china chimene Yehova wachita kuti tiyandikane naye.

WATIPATSA MAWU AKE KUTI TIYANDIKANE NAYE

10. Kodi m’Baibulo muli mfundo ziti zimene zingatithandize kuyandikira Mulungu?

10 Kuyambira kumayambiriro kwa nkhaniyi mpaka pamene tafikapa, tatchula malemba ochokera m’mabuku 14 a m’Baibulo. Kodi pakanapanda Baibulo tikanadziwa bwanji zoti tikhoza kuyandikira Mlengi wathu? Nanga tikanadziwa bwanji za dipo komanso zoti tikhoza kugwirizana ndi Yehova kudzera mwa Yesu? Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake pouzira anthu kuti alembe mfundo zokhudza makhalidwe ake abwino komanso zolinga zake. Mwachitsanzo, pa Ekisodo 34:6, 7, Yehova anauza Mose kuti iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” Kodi alipo amene sangakonde Mulungu wa makhalidwe amenewa? Yehova amadziwa kuti anthufe tikamaphunzira za makhalidwe ake m’Baibulo tikhoza kumudziwa bwino komanso kumukonda kwambiri.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuphunzira za makhalidwe a Yehova komanso njira zake? (Onani chithunzi patsamba 16.)

11 Pofotokoza zimene tingachite kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu, mawu oyamba m’buku la Yandikirani kwa Yehova amati: “Pa ubwenzi uliwonse umene timapanga, timagwirizana ndi munthuyo chifukwa chakuti timamudziwa, ndiponso kuti ali ndi khalidwe lapadera limene timalisirira ndi kuliona kukhala labwino zedi. Motero makhalidwe a Mulungu ndiponso kachitidwe kake ka zinthu, monga zasonyezedwera m’Baibulo, ndi nkhani yofunika kwambiri kuiphunzira.” Timayamikira kwambiri kuti Yehova anachititsa kuti Mawu ake alembedwe m’njira yoti anthufe tizimva.

12. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha zoti anthu alembe Baibulo?

 12 Yehova akanatha kuuza angelo kuti alembe Baibulo. Paja iwo amachita chidwi ndi anthufe komanso zimene timachita. (1 Pet. 1:12) N’zodziwikiratu kuti iwo akanalemba uthenga wa Mulungu. Koma kodi iwo akanatha kuona zinthu mmene ife timazionera? Kodi akanamvetsa bwinobwino zimene timafuna, zimene zimativuta komanso zimene timalakalaka? Yehova anadziwiratu kuti iwo sangathe. Choncho posankha anthu kuti alembe Baibulo, zinathandiza kuti nkhani zake zizitifika pamtima. Timatha kumvetsa mmene anthu olemba Baibulo ndiponso anthu ena otchulidwa m’Malemba ankaganizira komanso mmene ankamvera mumtima mwawo. Timamvetsa bwino zimene zinkawachititsa kukhumudwa, kukayikakayika, kuchita mantha, kulakwitsa, kusangalala ndiponso kuchita bwino zinthu zina. Mofanana ndi Eliya, olemba Baibulo onse ‘anali anthu monga ife tomwe.’—Yak. 5:17.

Kodi zimene Yehova anachita ndi Yona komanso Petulo zimathandiza bwanji kuti tizimukonda kwambiri? (Onani ndime 13 ndi 15)

13. Kodi inuyo mumamva bwanji mukawerenga pemphero la Yona?

13 Mwachitsanzo, kodi mngelo akanatha kufotokoza bwino mmene Yona ankamvera mumtima mwake pamene ankathawa ntchito imene Mulungu anamupatsa? Yehova anachita bwinotu posankha Yona kuti alembe zimene zinamuchitikira komanso zimene ananena pochonderera Mulungu ali m’nyanja. Yona anati: “Pamene ndinalefuka kwambiri, ndinakumbukira Yehova.”—Yona 1:3, 10; 2:1-9.

14. N’chifukwa chiyani timamvetsa zimene Yesaya analemba?

14 Taganiziraninso zimene Yesaya analemba. Iye ataona ulemerero wa Mulungu anadzimvera chisoni kwambiri chifukwa chakuti anali wochimwa ndipo anadandaula kuti: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Nditsikira kuli  chete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa, ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.” (Yes. 6:5) Kodi mngelo akanatha kulemba zimenezi? Ayi. Yesaya ndi amene akanatha ndipo ife timamvetsa zimene ankatanthauza.

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani sitivutika kumvetsa mmene anthu ena akumvera? Perekani zitsanzo. (b) N’chiyani chingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

15 Kodi angelo akanatha kulemba mawu a Yakobo akuti “ndine wosayenerera” kapena mawu a Petulo akuti “ndine munthu wochimwa”? (Gen. 32:10; Luka 5:8) Nanga angelo ‘akanachita mantha’ ngati ophunzira a Yesu? (Yoh. 6:19) Kapena kodi akanavutika kulimba mtima kuti alalikire ngati mmene zinalili ndi Paulo ndi anzake? (1 Ates. 2:2) Ayi. Paja iwotu ndi angwiro ndiponso amphamvu kwambiri kuposa ifeyo. Koma anthu ochimwa akafotokoza zinthu ngati zimenezi, timawamvetsa chifukwa nafenso ndi ochimwa. Choncho tikamawerenga Mawu a Mulungu ‘timasangalala ndi anthu amene akusangalala komanso kulira ndi anthu amene akulira.’—Aroma 12:15.

16 Tikamaganizira kwambiri mmene Yehova ankachitira zinthu ndi atumiki ake akale, timaona umboni wakuti iye ndi Mulungu woleza mtima komanso wachikondi ndipo amafuna kukhala pa ubwenzi ndi anthufe. Zimenezi zimatithandiza kuti timudziwe bwino, tizimukonda kwambiri komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.—Werengani Salimo 25:14.

MUZILIMBITSA KWAMBIRI UBWENZI WANU NDI MULUNGU

17. (a) Kodi Azariya anapereka malangizo abwino ati kwa Asa? (b) Kodi Asa ananyalanyaza bwanji malangizowo ndipo zotsatira zake zinali zotani?

17 Mfumu Asa itagonjetsa asilikali a Aitiyopiya, Azariya yemwe anali mneneri wa Mulungu anapereka malangizo anzeru kwa mfumuyo ndiponso anthu ake. Iye anati: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye. Mukamufunafuna iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.” (2 Mbiri 15:1, 2) Koma Asa atakalamba anasiya kutsatira malangizowo. Pa nthawi imene ufumu wakumpoto wa Isiraeli unkafuna kuukira Yuda, Asa anapempha thandizo kwa Asiriya. Iye anachita pangano ndi anthu osalambira Mulungu m’malo mopempha Yehova kuti amuthandize. Choncho Asa anauzidwa kuti: “Mwachita zopusa pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.” Kuyambira nthawiyo, mu ulamuliro wa Asa munkachitika nkhondo zokhazokha. (2 Mbiri 16:1-9) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi?

18, 19. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati ubwenzi wathu ndi Yehova wayamba kusokonekera? (b) Kodi tingalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

18 Tisalole kuti ubwenzi wathu ndi Yehova usokonekere. Ngati zimenezi zayamba kuchitika, tiyenera kutsatira malangizo a pa Hoseya 12:6 akuti: “Ubwerere kwa Mulungu wako. Usonyeze kukoma mtima kosatha ndi chilungamo ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.” Tiyeni tizilimbitsa kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova. Tiziganizira ndiponso kuyamikira dipo komanso tiziphunzira mwakhama Mawu ake.—Werengani Deuteronomo 13:4.

19 Wamasalimo analemba kuti: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.” (Sal. 73:28) Choncho tiyeni tonsefe tipitirize kuphunzira za Yehova n’kumaona zifukwa zotichititsa kumukonda kwambiri. Tikatero, Yehova adzapitiriza kutiyandikira panopa mpaka muyaya.

^ ndime 3 Onani nkhani yonena za Asa yakuti “Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2012.