NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) April 2014

Magaziniyi ikufotokoza mmene tingasonyezere chikhulupiriro ngati Mose. Kodi Yehova amaona bwanji udindo wosamalira banja, nanga amatithandiza bwanji kuti tiukwaniritse?

Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose

Kodi chikhulupiriro chinathandiza bwanji Mose kukana zilakolako za thupi n’kumaona kuti kutumikira Mulungu n’kofunika kwambiri? N’chifukwa chiyani Mose ankayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire?

Kodi ‘Mukuona Wosaonekayo’?

Kodi chikhulupiriro chinathandiza bwanji Mose kuti asamaope anthu komanso kuti asamakayikire malonjezo a Mulungu? Limbitsani chikhulupiriro chanu kuti muziona Yehova ngati munthu weniweni amene akufunitsitsa kukuthandizani.

MBIRI YA MOYO WANGA

Madalitso Amene Ndapeza mu Utumiki wa Nthawi Zonse

M’bale Robert Wallen akufotokoza zimene wachita mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 65. Werengani nkhaniyi kuti mumve zomwe zachititsa kuti moyo wake ukhale wosangalatsa komanso wopindulitsa.

Simungatumikire Ambuye Awiri

Anthu ena amapita kukagwira ntchito m’mayiko akunja. Kodi zimenezi zimasokoneza bwanji ubwenzi wawo m’banja komanso ndi Mulungu?

Limbani Mtima Yehova Akuthandizani

Kodi bambo wina atabwerera kwawo anatani kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino m’banja lake? Nanga Yehova anamuthandiza bwanji kuti azitha kusamalira bwino banja lake ngakhale kuti ankapeza ndalama zochepa?

Yehova Amaona Mavuto Athu N’kutithandiza

Werengani nkhaniyi kuti muone njira 5 zimene Mulungu amasonyezera kuti amatikonda. Komanso muona kuti zinthu zimatiyendera bwino chifukwa chakuti Mulungu amaganizira munthu aliyense payekha.

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani anthu ena otchulidwa m’Baibulo ankang’amba zovala zawo?