Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Mukuona Wosaonekayo’?

Kodi ‘Mukuona Wosaonekayo’?

“Anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.”—AHEB. 11:27.

1, 2. (a) N’chiyani chikanachititsa kuti Mose aope kupita kwa Farao? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani Mose sanaope mkwiyo wa mfumu?

AIGUPUTO ankaona kuti Farao anali mfumu yoopsa ndiponso mulungu wawo. Buku lina linanena kuti iwo ankaona kuti Farao “anali ndi nzeru komanso mphamvu kuposa wina aliyense.” (When Egypt Ruled the East) Kuti aziopedwa, Farao ankavala chipewa chachifumu chokhala ndi chifaniziro cha njoka yolusa. Zimenezi zinkasonyeza kuti anali wokonzeka kuononga adani ake onse. Ndiye taganizirani mmene Mose anamvera Yehova atamuuza kuti: “Ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.”—Eks. 3:10.

2 Mose anapita ku Iguputo n’kukanena uthenga wa Mulungu ndipo Farao atamva, anakwiya kwambiri. Mulungu atagwetsera Aiguputo miliri 9, Farao anachenjeza Mose kuti: “Ndisadzakuonenso, chifukwa ndikadzangokuonanso udzafa.” (Eks. 10:28) Mose asanachoke kwa Farao, ananeneratu kuti mwana woyamba wa Farao adzafa. (Eks. 11:4-8) Kenako Mose anauza mabanja onse a Aisiraeli kuti aphe mbuzi kapena nkhosa ndipo awaze magazi ake pamafelemu a nyumba zawo. (Eks. 12:5-7) Aiguputo ankaona kuti nyama zimenezi zinali zopatulika pamaso pa mulungu wotchedwa Ra. Mose sanachite  mantha ndi zimene Farao angachite atamva zimenezi. Iye anali ndi chikhulupiriro ndipo anamvera Yehova moti ‘sankaopa mfumu ayi, pakuti anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.’—Werengani Aheberi 11:27, 28.

3. Kodi tikambirana mafunso ati okhudza chikhulupiriro cha Mose?

3 Kodi muli ndi chikhulupiriro cholimba chomwe chingakuthandizeni kuti muzikhala ngati ‘mukuona Mulungu’? (Mat. 5:8) Tiyeni tikambirane nkhani ya Mose kuti nafenso tizikhala ngati ‘tikuona Wosaonekayo.’ Kodi kukhulupirira Yehova kunathandiza bwanji Mose kuti asamaope anthu? Kodi iye anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira malonjezo a Mulungu? Nanga kodi “kuona Wosaonekayo” kunamuthandiza bwanji pamene iye ndi anthu ake anali pa mavuto aakulu?

SANAOPE MKWIYO WA MFUMU

4. Kodi anthu ena ankaona bwanji Mose akamuyerekezera ndi Farao?

4 Anthu ena ankaona kuti Mose si munthu woti angauze Farao zochita. Ankaganiza kuti moyo wake komanso tsogolo lake zili m’manja mwa Faraoyo. Ngakhale Mose weniweniyo anafika pofunsa Yehova kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” (Eks. 3:11) Mose anali atathawa ku Iguputo komweko zaka 40 zapitazo. Choncho, mwina ankadzifunsa kuti, ‘Koma zoona ndipitedi ku Iguputo? Kodi mfumu ija siikandipha?’

5, 6. N’chiyani chinathandiza Mose kuti aziopa Yehova osati Farao?

5 Mose asanabwerere ku Iguputo, Mulungu anamuphunzitsa mfundo ina yofunika kwambiri yomwe Moseyo anailemba m’buku la Yobu. Mfundo yake ndi yakuti: “Kuopa Yehova ndiko nzeru.” (Yobu 28:28) Pothandiza Mose kuti aziopa Mulungu ndi kuchita zinthu mwanzeru, Yehova anamufotokozera kusiyana kwa munthu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Iye anafunsa Mose kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?”—Eks. 4:11.

6 Kodi pamenepa Yehova ankatanthauza chiyani? Mose sanafunike kuchita mantha. Iye anatumidwa ndi Yehova ndipo Yehovayo akanatha kumupatsa chilichonse chomuthandiza kuti akapereke uthengawo kwa Farao. Ndipotu Farao sangafanane ndi Yehova m’pang’ono pomwe. Akanso sikanali koyamba kuti anthu a Mulungu aopsezedwe ndi mfumu ya ku Iguputo. N’kutheka kuti Mose ankaganizira mmene Yehova anatetezera Abulahamu, Yosefe komanso iyeyo pa nthawi ya ulamuliro wa mafumu ena a Iguputo. (Gen. 12:17-19; 41:14, 39-41; Eks. 1:22–2:10) Mose ankakhulupirira Yehova yemwe ndi “Wosaonekayo” ndipo analimba mtima n’kupita kukauza Farao zonse zimene Yehova anamutuma.

7. Kodi chikhulupiriro chinateteza bwanji mlongo wina?

7 Kuopa Yehova kunathandizanso mlongo wina dzina lake Ella kuti asamaope anthu. Mu 1949, mlongoyu anagwidwa ndi apolisi ku Estonia n’kuvulidwa zovala zonse ndipo apolisi achinyamata ankamuonera. Ella anati: “Ndinachita manyazi koopsa. Koma nditapemphera kwa Yehova, mtima wanga unakhala m’malo.” Kenako, Ella anatsekeredwa m’chipinda chayekha kwa masiku atatu. Iye anati: “Apolisi ankanena mofuula kuti: ‘Tithana nawe ndipo dzina lakuti Yehova silidzamvekanso ku Estonia kuno. Iwe upita kundende ndipo anzako tiwapititsa ku Siberia.’ Ankanenanso mwachipongwe kuti, ‘Yehova wakoyo ali kuti?’” Kodi Ella anaopa anthu kapena anakhulupirira Yehova? Pa nthawi imene apolisi ankamufunsa mafunso, mlongoyu anayankha kuti: “Nkhaniyitu ndaiganizira mofatsa. Ndingalolere kukhala m’ndende koma ubwenzi wanga ndi Mulungu uli bwinobwino, kusiyana ndi kumasulidwa koma n’kukwiyitsa Mulungu.” Apatu Ella ankaona bwinobwino Yehova ngati mmene ankaonera anthu amene ankamufunsawo. Chikhulupiriro chinamuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika.

8, 9. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamaope anthu? (b) Kodi tizidalira ndani ngati tayamba kuopa anthu?

 8 Inunso mukamakhulupirira Yehova simudzachita mantha. Akuluakulu aboma akamachita zinthu zimene zingakulepheretseni kulambira Mulungu, zingaoneke ngati mulibenso tsogolo lililonse. Mwinanso mungayambe kuganiza kuti kuli bwino kusiya kutumikira Yehova kuti musangalatse akuluakulu abomawo. Koma muyenera kukumbukira kuti kukhulupirira Mulungu ndi komwe kungakuthandizeni kuti musamaope anthu. (Werengani Miyambo 29:25.) Nthawi ina Yehova anafunsa kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani iwe ukuopa munthu woti adzafa, ndi mwana wa munthu yemwe adzakhale ngati udzu wobiriwira?”—Yes. 51:12, 13.

9 Nthawi zonse tiyenera kudalira Atate wathu Wamphamvuyonse. Iye amaona komanso amakhudzidwa anthu akamaponderezedwa ndi olamulira opanda chilungamo ndipo amachitapo kanthu kuti awathandize. (Eks. 3:7-10) Ngati pakufunika kuti mulankhule za chikhulupiriro chanu pamaso pa akuluakulu aboma, “musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.” (Mat. 10:18-20) Olamulira adzikoli kapena akuluakulu aboma sangafanane ndi Yehova. Choncho muyenera kulimbitsa chikhulupiriro chanu panopa kuti muziona Yehova ngati munthu weniweni amene akufunitsitsa kukuthandizani.

MOSE ANKAKHULUPIRIRA MALONJEZO A MULUNGU

10. (a) Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Aisiraeli m’mwezi wa Nisani mu 1513 B.C.E.? (b) N’chifukwa chiyani Mose anamvera malangizo a Mulungu?

10 M’mwezi wa Nisani m’chaka cha 1513 B.C.E., Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti akapereke malangizo ovuta kumvetsa kwa Aisiraeli. Malangizo ake anali akuti asankhe nkhosa kapena mbuzi yamphongo yathanzi n’kuipha ndipo magazi akewo awaze pamafelemu a nyumba zawo. (Eks. 12:3-7) Kodi Mose anachita chiyani? Patapita nthawi, mtumwi Paulo analemba zimene anachita. Anati: “Mwa chikhulupiriro, iye anachita pasika ndiponso anawaza magazi pamafelemu a pakhomo, kuti wowonongayo asakhudze ana awo oyamba kubadwa.” (Aheb. 11:28) Mose ankadziwa kuti Yehova ndi wodalirika, ndipo ankakhulupirira malonjezo ake akuti adzapha ana onse oyamba kubadwa a Aiguputo.

11. N’chifukwa chiyani Mose anachenjeza Aisiraeli?

11 Zikuoneka kuti ana a Mose anali ku Midiyani, kutali ndi “wowonongayo.” * (Eks. 18:1-6) Koma Mose anamvera Mulungu ndipo anapereka malangizowo kwa Aisiraeli anzakewo kuti ana awo oyamba kubadwa asaphedwe. Mose ankakonda anthu ndipo sankafuna kuti aliyense aphedwe. Baibulo limanena kuti: “Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli ndi kuwauza kuti: ‘Sankhani nkhosa ndi mbuzi . . . muiphere nsembe ya pasika.’”—Eks. 12:21.

12. Kodi Yehova akufuna kuti tilengeze uthenga wofunika uti?

12 Motsogoleredwa ndi angelo, anthu a Yehova akulengeza uthenga wofunika kwambiri wakuti: “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:7) Ino ndiye nthawi yoti tilengeze uthengawo. Tiyenera kuchenjeza anthu kuti atuluke mu Babulo Wamkulu, kuti ‘asalandire nawo ina ya miliri yake.’ (Chiv. 18:4) A “nkhosa zina” limodzi ndi Akhristu odzozedwa akuchonderera anthu amene atalikirana ndi Mulungu kuti ‘agwirizanenso’ naye.—Yoh. 10:16; 2 Akor. 5:20.

Mukamakhulupirira malonjezo a Yehova mudzakhala ofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino(Onani ndime 13)

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe ofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino?

13 Sitikukayikira kuti “ola lakuti [Mulungu] apereke chiweruzo” lafika. Tikukhulupiriranso  kuti Yehova sakukokomeza potiuza kuti tikufunika kugwira mwamsanga ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu. M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “angelo anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi za dziko lapansi.” (Chiv. 7:1) Kodi chikhulupiriro chanu chikukuthandizani kuona kuti angelowo atsala pang’ono kusiya mphepoyo kuti iwononge dzikoli pa chisautso chachikulu? Ngati zili choncho, mudzalengeza uthenga wabwino molimba mtima.

14. N’chifukwa chiyani timafunitsitsa ‘kuchenjeza anthu oipa kuti asiye njira yawo yoipayo’?

14 Akhristufe timasangalala kuti tili pa ubwenzi ndi Yehova komanso tikuyembekezera kudzalandira moyo wosatha. Komabe, tikudziwa kuti tili ndi udindo ‘wochenjeza anthu oipa kuti asiye njira yawo yoipa n’cholinga choti akhalebe ndi moyo.’ (Werengani Ezekieli 3:17-19.) Komatu sikuti timangolalikira chifukwa choopa mlandu wamagazi. Timalalikira chifukwa chakuti timakonda Yehova komanso anthu. Mu fanizo la Msamariya wachifundo Yesu anasonyeza tanthauzo lenileni la chikondi komanso chifundo. Choncho tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimamvera anthu ena chifundo ngati Msamariya uja, moti ndimalalikira uthenga wabwino?’ Sitingafune kukhala ngati wansembe ndi Mlevi a mufanizoli amene ‘anangolambalala’ munthu wovulazidwa uja. (Luka 10:25-37) Tikamakhulupirira malonjezo a Mulungu ndi kukonda anthu tidzakhala ofunitsitsa kugwira ntchito yolalikira nthawi isanathe.

“ANAWOLOKA NYANJA YOFIIRA”

15. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankaona ngati alibiretu mtengo wogwira?

15 Mose ankakhulupirira kwambiri “Wosaonekayo” ndipo zimenezi zinamuthandiza pa nthawi imene Aisiraeli anali pa  mavuto aakulu. Baibulo limanena kuti: “Ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.” (Eks. 14:10-12) Koma kodi anayenera kudabwa nazo zimenezi? Ayi, chifukwa Yehova anali atanena kale kuti: “Ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo adzawathamangira. Ndidzapezerapo ulemerero mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo, ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Eks. 14:4) Komatu Aisiraeliwo ankangoona zooneka ndi maso. Ankangoona kuti mtsogoleri wawo ndi m’busa wa zaka 80 koma kutsogolo kuli Nyanja Yofiira ndipo kumbuyo kuli Farao ndi magaleta ankhondo aliwiro. Choncho ankaona kuti alibiretu mtengo wogwira.

16. Kodi chikhulupiriro chinathandiza bwanji Mose pa Nyanja Yofiira?

16 Koma Mose sankadandaula chilichonse. Chifukwa cha chikhulupiriro chake, iye ankaona “chipulumutso cha Yehova” yemwe ndi wamphamvu kuposa Nyanja Yofiira komanso asilikali a Farao. Ankadziwa kuti Yehova amenyera nkhondo Aisiraeliwo. (Werengani Ekisodo 14:13, 14.) Chikhulupiriro cha Mose chinalimbikitsa kwambiri anthuwo. Baibulo limati: “Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma, koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.” (Aheb. 11:29) Zitatero, “Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.”—Eks. 14:31.

17. Kodi m’tsogolomu chikhulupiriro chathu chidzayesedwa bwanji?

17 Posachedwapa, nafenso tidzakumana ndi mavuto aakulu. Chisautso chachikulu chikadzafika pachimake, maboma a dzikoli adzakhala atawononga zipembedzo zimene panopa n’zamphamvu komanso zili ndi anthu ambiri kuposa gulu lathu. (Chiv. 17:16) Yehova ananeneratu kuti ife tizidzaoneka ngati “dziko lokhala ndi midzi yopanda mipanda” komanso yopanda “zotsekera ndiponso zitseko.” (Ezek. 38:10-12, 14-16) Pa nthawiyo, zidzaoneka ngati mwayi wopulumuka palibiretu. Ndiyeno kodi tidzatani pamenepo?

18. N’chifukwa chiyani sitidzafunika kuchita mantha pa chisautso chachikulu?

18 Pa nthawiyo, sitidzafunika kuopa chilichonse. Tikutero chifukwa chakuti Yehova walosera kale kuti anthu ake adzaukiridwa. Koma waneneratunso zotsatira zake. Paja Ambuye Wamkulu Koposa anati: “Pa tsiku limenelo, tsiku limene Gogi adzabwere m’dziko la Isiraeli, mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno mwanga, . . . Ine ndidzalankhula mwaukali wanga woyaka moto komanso nditakwiya kwambiri.” (Ezek. 38:18-23) Yehova adzawononga onse amene angafune kuwononga anthu ake. Ndiyeno kukhulupirira zimene Yehova wanena kuti zidzachitika pamapeto pa “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova,” kudzatithandiza kuti tizidzaona “chipulumutso cha Yehova” komanso kuti tidzakhalebe okhulupirika.—Yow. 2:31, 32.

19. (a) Kodi ubwenzi wa Yehova ndi Mose unali wotani? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati tikumbukira Yehova m’njira zathu zonse?

19 Choncho tiyeni tizikonzekera zimene zidzachitike m’tsogolozi popitiriza ‘kukhala ngati tikuona Wosaonekayo.’ Tiziyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu pophunzira Mawu ake komanso kupemphera nthawi zonse. Mose anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo anagwiritsidwa ntchito kuti achite zinthu zamphamvu. M’pake kuti Baibulo limati Yehova ankadziwa Mose “pamasom’pamaso.” (Deut. 34:10) N’zoona kuti Mose anali mneneri wapadera kwambiri. Koma ifenso chikhulupiriro chingatithandize kukhala pa ubwenzi wapadera ndi Yehova n’kumakhala ngati tikuonana naye pamasom’pamaso. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti ‘tizim’kumbukira m’njira zathu zonse.’ Tikatero iye ‘adzawongola njira zathu.’—Miy. 3:6.

^ ndime 11 Zikuoneka kuti Yehova anatumiza angelo kuti akapereke chiweruzo kwa Aiguputo.—Sal. 78:49-51.