Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Limbani Mtima Yehova Akuthandizani

Limbani Mtima Yehova Akuthandizani

“Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga.’”—AHEB. 13:6.

1, 2. Kodi anthu amene anali kumayiko ena amakumana ndi mavuto otani akabwerera kwawo? (Onani chithunzi pamwambapa.)

M’BALE wina dzina lake Eduardo * anati: “Ndinkagwira ntchito kunja ndipo ndinali pa ntchito yapamwamba komanso ndinkalandira ndalama zambiri. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinaona kuti ndili ndi udindo wina wofunika kwambiri, wosamalira banja langa komanso kuliphunzitsa za Yehova. Choncho ndinabwerera kwathu.”—Aef. 6:4.

2 Eduardo anazindikira kuti akabwerera kukakhala ndi banja lake, Yehova adzasangalala. Koma mofanana ndi Marilyn, yemwe tam’tchula m’nkhani yapitayi, iye atabwerera anafunika kukonza ubwenzi wake ndi anthu a m’banja lake. Ankasowanso ndalama zosamalira banja lake. Kodi akanatani pamenepa? Nanga anthu ena mumpingo akanamuthandiza bwanji?

KUKONZA ZINTHU KUTI ZIYAMBENSO KUYENDA BWINO

3. Kodi kuchoka kwa makolo kumakhudza bwanji ana?

3 Eduardo anavomereza kuti: “Ndinkadziwa kuti ana anga ndinawasiya pa nthawi yolakwika. Ndinachoka pa nthawi imene ndinkafunika kuti ndiziwatsogolera, ndiziwawerengera nkhani za m’Baibulo, kupemphera nawo, kuwanyamula komanso kusewera nawo.”  (Deut. 6:7) Mwana wawo wamkazi, dzina lake Anna anati: “Ndikaganiza kuti bambo sitikukhala nawo panyumba, ndinkaona kuti ndilibe munthu woti azindilimbikitsa. Atabwera sindinkawaonanso ngati bambo anga, moti ndinangowadziwira mawu ndi nkhope yawo. Atandikumbatira, sindinamve ngati ndakumbatiridwa ndi munthu amene amandikonda.”

4. Kodi mwamuna akachoka zimakhudza bwanji udindo wake wotsogolera banja?

4 Bambo akachoka pakhomo sangathenso kutsogolera banja lake. Ruby, yemwe ndi mkazi wa Eduardo anati: “Ndinali ndi maudindo awiri. Ndinkakhala ngati bambo komanso mayi ndipo ndinazolowera kusankhira banja langa zochita. Koma Eduardo atabwera, ndinafunika kuphunzira kugonjera. Ngakhale panopa ndimachita kudzikumbutsa kuti hii, paja mwamuna wanga ali pompano.” (Aef. 5:22, 23) Eduardo ananenanso kuti: “Ana anga anazolowera kupempha amayi awo akafuna kuchita chilichonse. Choncho tinaona kuti makolofe tinkafunika kuchita zinthu mogwirizana pouza ana anthuwo zochita, ndipo ndinafunika kuphunzira kutsogolera banja langa motsanzira Khristu.”

5. Kodi m’bale wina anachita chiyani pokonzanso zinthu m’banja lake, nanga zotsatira zake zinali zotani?

5 Eduardo anayesetsa kukonza ubwenzi wake ndi banja lake komanso kulithandiza kuti lizikonda Mulungu. Iye anati: “Ndinali n’cholinga chophunzitsa ana anga kuti azikonda Mulungu. Sindinkafuna kuti ndizingonena kuti ndimakonda Yehova, koma ndinkafuna kuti zochita zanga zizisonyeza zimenezo.” (1 Yoh. 3:18) Kodi Yehova anadalitsa Eduardo chifukwa cha chikhulupiriro chake? Anna ananena kuti: “Tinkaona kuti bambo akuyesetsa kuti azichita zinthu bwino komanso kuti tiyambenso kuchitira zinthu limodzi. Zimenezi zinathandiza kwambiri, ndipo tinasangalala titaona kuti akuyesetsa kuti akhale ndi udindo mumpingo. Dzikoli linkafuna kutisiyanitsa ndi Yehova. Koma tinkaona kuti makolo athu akukonda kwambiri kutumikira Mulungu, ndipo ifenso tinachita zomwezo. Bambo analonjeza kuti sadzatisiyanso, ndipo ankanena zoona. Akanachokanso, mwina si bwenzi pano ndili m’gulu la Yehova.”

TIKALAKWITSA TIZIVOMEREZA

6. Kodi makolo ena anaphunzira chiyani pa zimene zinachitika nthawi ya nkhondo?

6 Pali umboni wakuti pa nthawi imene kum’mwera chakum’mawa kwa Ulaya kunali nkhondo, ana a Mboni za Yehova a kumeneko ankaoneka osangalala ngakhale kuti anali pa mavuto. N’chifukwa chiyani zinali choncho? Makolo anasiya kupita kuntchito. M’malomwake, ankakhala kunyumba n’kumaphunzira ndi ana awo komanso kucheza nawo. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ana amafuna kukhala ndi makolo awo osati kungowapatsa ndalama kapena mphatso. Malemba amanenanso kuti ana zimawayendera bwino ngati amasamaliridwa komanso kuphunzitsidwa ndi makolo awo.—Miy. 22:6.

7, 8. (a) Kodi makolo ena akabwerera kunyumba amamva bwanji? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti ayambenso kuwakonda ndi kuwalemekeza?

7 Makolo ena akabwerera kunyumba salandiridwa bwino ndi ana awo. Choncho anganene kuti: “Koma inu ndi ana otani inu? Simungaone kuti kuvutika konseku ndikuvutika chifukwa cha inu?” Amaiwala kuti anawo akuchita zimenezo chifukwa chakuti makolowo anachoka. Ngati ndinu makolo, kodi mungatani kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino?

8 Muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kuwamvetsa anthu a m’banja lanu. Komanso pokambirana ndi banja lanu, muyenera kuvomereza kuti munalakwitsa pochoka ndipo zimenezo zayambitsa mavuto. Zingakhale bwinonso kuwapepesa kuchokera pansi pa mtima. Anthu a m’banja lanu akaona kuti mukuyesetsa ndi mtima wonse kuti mukonze zinthu, adzayamikira kwambiri. Musafooke ndipo khalani oleza mtima. Mukatero, pang’ono ndi pang’ono anthu a m’banja lanu adzayambanso kukukondani ndiponso kukulemekezani.

 ‘UDINDO WOSAMALIRA A M’BANJA LATHU’

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti si bwino kufunafuna chuma pofuna ‘kusamalira a m’banja lathu’?

9 Mtumwi Paulo anapereka malangizo akuti ngati Akhristu achikulire sangathe kudzisamalira, ana ndi adzukulu awo ayenera “kubwezera kwa makolo ndi agogo awo zowayenerera.” Koma Paulo analimbikitsanso Akhristu kuti ayenera kukhutira ngati ali ndi zinthu zofunika kwambiri monga chakudya, zovala komanso malo ogona. Sitiyenera kulakalaka moyo wapamwamba kapena chuma choti tidzagwiritse ntchito m’tsogolo. (Werengani 1 Timoteyo 5:4, 8; 6:6-10.) Kuti munthu athe ‘kusamalira a m’banja lake,’ sikuti ayenera kufunafuna chuma m’dziko limene likupitali. (1 Yoh. 2:15-17) Tisalole kuti “chinyengo champhamvu cha chuma” kapena “nkhawa za moyo” zilepheretse banja lathu ‘kugwira mwamphamvu moyo weniweniwo’ m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—Maliko 4:19; Luka 21:34-36; 1 Tim. 6:19.

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timatsatira nzeru yochokera kwa Mulungu pa nkhani ya ngongole?

10 Yehova amadziwa kuti anthufe timafunika ndalama. Koma ndalama sizingatiteteze ngati mmene ingatitetezere nzeru yochokera kwa Mulungu. (Mlal. 7:12; Luka 12:15) Nthawi zambiri, anthu amanyalanyaza mavuto amene angabwere ngati atapita kukagwira ntchito kunja. Ndipo ena akapita kunjako sapeza ndalama zimene ankafunazo. M’malomwake amakumana ndi mavuto aakulu. Ambiri mwa anthuwa amabwerera kwawo ali ndi ngongole zikuluzikulu. M’malo motumikira Yehova, amatumikira anthu amene anawakongoza ndalamawo. (Werengani Miyambo 22:7.) Choncho ndi bwino kungopeweratu ngongoleyo.

11. Kodi kukhala ndi bajeti kungathandize bwanji kuti banja lizigwiritsa ntchito bwino ndalama?

11 Eduardo ankadziwa kuti ayenera kugwiritsa ntchito bwino ndalama kuti asapitenso kunja. Iye ndi mkazi wake anakonza bajeti ya zinthu zofunika zokhazokha. Iwo ankadzimana zinthu zina zimene anali nazo poyamba. Koma onse m’banjamo anagwirizana nazo ndipo sankawononga ndalama pa zinthu zosafunika. * Eduardo anati: “Ndinachotsa ana anga kusukulu zapulaiveti n’kuwapititsa kusukulu zaboma zabwino.” Iye ndi banja lake ankapemphera kuti apeze ntchito imene singamasokoneze zinthu zokhudza kulambira. Kodi Yehova anayankha bwanji mapemphero awo?

12, 13. (a) Kodi bambo wina anachita zotani kuti athandize banja lake? (b) Nanga Yehova anamudalitsa bwanji chifukwa choyesetsa kuti akhale ndi moyo wosalira zambiri?

12 Eduardo anati: “Kunena zoona tinavutika kwa zaka ziwiri zoyambirira. Ndalama zanga zinayamba kutha ndipo zimene ndinkapeza zinali zosakwanira. Ndinkatopanso kwambiri. Koma tonse tinkapezeka pa misonkhano yonse ndipo tinkalalikira.” Eduardo anatsimikiza kuti sadzalolanso kukagwira ntchito kutali ndi banja lake kwa miyezi kapena zaka zambiri. Iye anati: “Ndaphunzira ntchito zosiyanasiyana kuti ngati ina sikupezeka, ndizigwirabe inayo.”

Kodi mungaphunzire ntchito zosiyanasiyana kuti zizikuthandizani kupeza zofunika posamalira banja lanu? (Onani ndime 12)

13 Popeza kuti Eduardo ankabweza pang’onopang’ono ngongole imene anali nayo, zinachititsa kuti aperekenso ndalama za chiwongoladzanja zochuluka. Koma ankaona kuti limenelo si vuto lalikulu chifukwa ankapeza nthawi yokwanira yochitira limodzi zinthu ndi banja lake. Ndipo ankasangalala chifukwa chodziwa kuti akuchita zimene Yehova amafuna kuti makolo azichita. Iye anati: “Panopa ndimapeza ndalama zochepa kwambiri poyerekezera ndi zomwe ndinkapeza pamene ndinkagwira ntchito kunja, komabe sitinagonepo ndi njala. N’zoona kuti ‘dzanja la Yehova silinafupike.’ Tinaganiza zoyamba upainiya. Ndipo titangoyamba upainiyawo, vuto la zachuma lija linayamba kuchepa ndipo sitinkavutika kupeza zinthu zofunika.”—Yes  59:1.

 KUTHANDIZA ACHIBALE

14, 15. (a) Kodi mabanja angatani ngati akukakamizidwa kuti azikonda kwambiri chuma osati kulambira Mulungu? (b) Kodi chitsanzo chawo chabwino chingakhale ndi zotsatira zotani?

14 M’madera ambiri anthu amaona kuti akuyenera kupereka ndalama kapena mphatso kwa achibale awo ndiponso anzawo. Eduardo anati: “Ndi mmene chikhalidwe chathu chilili ndipo zimatisangalatsa. Koma tiyenera kudziwa malire. Ndimafotokozera achibale anga mosamala kuti ndizingowapatsa zimene ndingathe chifukwa sindikufuna kuti zimenezi zindilepheretse kukwaniritsa udindo wanga wothandiza banja langa pa nkhani zokhudza kulambira.”

15 Anthu amene abwerera kwawo kuchokera kudziko lina komanso amene amakana kusiya mabanja awo chifukwa cha ntchito amakumananso ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, achibale awo omwe amayembekezera kuti aziwathandiza, amawanyoza ndiponso kuwakwiyira. Ena amawanena kuti alibe chikondi. (Miy. 19:6, 7) Anna ananena kuti: “Koma tikamakana kunyalanyaza zinthu zauzimu chifukwa chofuna kupeza chuma, patapita nthawi achibale ena angamvetse kuti kwa ifeyo chofunika kwambiri n’kutumikira Mulungu. Koma sangamvetse zimenezi ngati titachita zofuna zawo.”—Yerekezerani ndi 1 Petulo 3:1, 2.

MUZIKHULUPIRIRA MULUNGU

16. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu akhoza ‘kudzinyenga ndi maganizo onama.’ (Yak. 1:22) (b) Kodi Yehova amadalitsa anthu otani?

16 Mlongo wina anasiya mwamuna wake komanso ana ake n’kupita kudziko lina kuti akagwire ntchito. Atafika m’dzikolo anauza akulu kuti: “Sinalitu nkhani ya masewera kuti ndibwere kuno. Tadzimana kwabasi. Moti mwamuna wanga anasiya kutumikira monga mkulu. Sindikukayikira kuti Yehova atidalitsa.” Yehova amadalitsa anthu amene zosankha zawo zimasonyeza kuti amamukhulupirira. Koma mwadala, anthuwa analolera kuti wina asiye udindo umene anali nawo mumpingo. Ndiyeno kodi n’zoona kuti Yehovayo angawadalitse pamene akuchita zinthu zosemphana ndi chifuniro chake?—Werengani Aheberi 11:6; 1 Yohane 5:13-15.

17. (a) Kodi tiyenera kufufuza malangizo a Yehova pa nthawi iti ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Nanga tingafufuze bwanji malangizowo?

17 Ndi bwino kufufuza malangizo a Yehova  tisanasankhe zochita osati titasankha kale. Tizipempha kuti atitsogolere komanso atipatse mzimu woyera ndi nzeru. (2 Tim. 1:7) Tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikhoza kumvera Yehova ngakhale pamene ndikuzunzidwa?’ Ngati ndi choncho, ndiye zingatikanike bwanji kumumvera n’kulolera kuti tizipeza ndalama zochepa? (Luka 14:33) Pemphani akulu kuti akupatseni malangizo ochokera m’Malemba ndipo muzikhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzakuthandizani ngati mumvera malangizo ake. N’zoona kuti akulu sangakusankhireni zochita koma akhoza kukuthandizani kusankha zinthu zimene zingakuthandizeni.—2 Akor. 1:24.

18. (a) Kodi ndani apatsidwa udindo wosamalira banja? (b) Kodi tingathandize bwanji anzathu?

18 Yehova anapatsa mitu ya mabanja udindo wosamalira anthu a m’banja lawo. Masiku ano, anthu ambiri amakakamizika kupita kumayiko ena kuti akagwire ntchito. Choncho tiyenera kuyamikira kwambiri anthu amene amasamalira mabanja awo popanda kupita kudziko lina. Pakagwa masoka achilengedwe kapena wina akadwala tiyenera kuthandizana. Tikatero tidzasonyeza kuti tikutsanzira chikondi cha Khristu komanso tikumverana chisoni. (Agal. 6:2, 5; 1 Pet. 3:8) Tingachite bwinonso kupereka ndalama zothandizira pakagwa masoka achilengedwe komanso kuthandiza abale athu kupeza ntchito kwathu komwe kuno. Tikatero tidzawathandiza kuti asalakelake kupita kukagwira ntchito m’mayiko akunja.—Miy. 3:27, 28; 1 Yoh. 3:17.

MUZIKUMBUKIRA KUTI YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI

19, 20. N’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kukayikira zoti Yehova adzawathandiza?

19 Malemba amatiuza kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’” (Aheb. 13:5, 6) Kodi n’zothekadi kukhala ndi maganizo amenewa?

20 M’bale wina yemwe ndi mkulu m’dziko lina losauka anati: “Anthu amakonda kunena zoti a Mboni amakhala osangalala. Amaona kuti a Mboni, ngakhale atakhala osauka, amavala bwino ndipo amaoneka kuti zikuwayendera kusiyana ndi anthu ena.” Izitu n’zogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti zidzachitikira anthu amene amafunafuna Ufumu choyamba. (Mat. 6:28-30, 33) Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, amakukondani ndipo amakufunirani zabwino inuyo ndi ana anu. Pajatu “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mulungu watipatsa malamulo othandiza pa nkhani ya chuma komanso mmene tingasamalirire banja. Tikamatsatira malamulowa timasonyeza kuti timamukonda komanso kumukhulupirira. “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yoh. 5:3.

21, 22. N’chifukwa chiyani inuyo simudzasiya kukhulupirira Yehova?

21 Eduardo anati: “Ndikudziwa kuti nthawi imene ndinachoka n’kusiya banja langa singabwererenso. Panopa ndinangosiya kuziganizira zimenezo. Anthu amene ndinkagwira nawo ntchito, panopa ndi olemera koma sasangalala. Mabanja awo sakuyenda bwino koma lathu likuyenda bwino ndipo tikusangalala. Ndimachita chidwi ndi abale ena kwathu kuno amene ndi osauka koma kulambira Yehova amakuika patsogolo. Zimene Yesu analonjeza zikuchitikadi.”—Werengani Mateyu 6:33.

22 Choncho limbani mtima. Muzimvera Yehova ndiponso kumukhulupirira. Sonyezani kuti mumakonda Mulungu komanso banja lanu. Mungachite zimenezi poyesetsa kukwaniritsa udindo umene Yehova wakupatsani m’banja lanulo. Mukatero, Yehova adzakuthandizani.

^ ndime 1 Mayina asinthidwa.

^ ndime 11 Onani Galamukani! ya September 2011 ya mutu wakuti “Kodi Mungasamale Bwanji Ndalama?”