NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) February 2014

Magaziniyi ikufotokoza nkhani yosangalatsa ya mu Salimo 45. Itithandizanso kuti tiziona kuti Yehova Mulungu amatipatsa zofunika, amatiteteza komanso ndi Mnzathu weniweni.

Tamandani Khristu, Mfumu ya Ulemerero

Kodi nkhani yosangalatsa imene yafotokozedwa mu Salimo 45 ikutikhudza bwanji?

Sangalalani Chifukwa cha Ukwati wa Mwanawankhosa

Kodi mkwatibwi ndi ndani? Kodi Khristu wakhala akumukonzekeretsa bwanji? Ndani adzasangalalanso chifukwa cha ukwatiwu?

Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Chikhulupiriro cha mkazi wamasiye chinalimba kwambiri mwana wake ataukitsidwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi?

Yehova Amatipatsa Zinthu Zofunika Ndipo Amatiteteza

Tiziona kuti Yehova Mulungu ndi Atate wathu wakumwamba. Nkhaniyi ingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu yemwe amatipatsa zinthu zofunika ndiponso amatiteteza.

Yehova Ndi Mnzathu Weniweni

Nkhaniyi ikusonyeza kuti Abulahamu ndi Gidiyoni anali mabwenzi a Yehova Mulungu. Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale mabwenzi a Yehova?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani Ayuda a m’nthawi ya Yohane Mbatizi “anali kuyembekezera” Mesiya?

‘Tiziona Ubwino wa Yehova’

Davide ankayamikira zimene Mulungu anakonza kuti anthu azimulambira. Kodi ifeyo tingatani kuti tizisangalala polambira Mulungu woona?

KALE LATHU

Padutsa Zaka 100 Tsopano

Padutsa zaka 100 tsopano kuchokera pamene filimu ya chilengedwe inayamba kuonetsedwa pofuna kuthandiza anthu kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.