Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani Ayuda a m’nthawi ya Yohane Mbatizi “anali kuyembekezera” Mesiya?

M’masiku a Yohane M’batizi, “anthu anali kuyembekezera Khristu, ndipo onse anali kuganiza m’mitima yawo za Yohane kuti: ‘Kodi Khristu uja si ameneyu?’” (Luka 3:15) N’chifukwa chiyani anthu ankayembekezera Khristu pa nthawi imeneyoyo? Pali zifukwa zingapo.

Yesu atabadwa, mngelo wa Yehova anaonekera kwa abusa amene ankaweta nkhosa zawo pafupi ndi Betelehemu. (1) Mngeloyo anawauza kuti: “Lero wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye, mumzinda wa Davide.” (Luka 2:8-11) Kenako panaoneka “khamu lalikulu lakumwamba pamodzi ndi mngeloyo likutamanda Mulungu kuti: * ‘Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.’”—Luka 2:13, 14.

Abusa odzichepetsawa anakhudzidwa kwambiri ndi mawu amenewa. Nthawi yomweyo iwo anapita ku Betelehemu ndipo atapeza Yosefe ndi Mariya komanso Yesu, “anafotokoza zimene anauzidwa zokhudza mwana ameneyu.” Ndipo “onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anali kuwauza.” (Luka 2:17, 18) Mawu akuti “onse amene anamva” akusonyeza kuti abusawa ananenanso mawuwa kwa anthu ena osati kwa Yosefe ndi Mariya okha. Kenako abusawo anabwerera kwawo “akulemekeza ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anamva ndi kuziona, ndendende mmene anawauzira muja.” (Luka 2:20) Choncho abusawa analengeza zinthu zabwino zokhudza Khristu zimene anamva.

Mariya atapita ku Yerusalemu kukapereka mwana wake woyambayu kwa Yehova mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, mneneri wamkazi dzina lake Anna “anafika pafupi ndi kuyamba kuyamika Mulungu. Komanso analankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.” (Luka 2:36-38; Eks. 13:12) Apatu uthenga wonena za Mesiya unkafalikirabe.

Kenako “okhulupirira nyenyezi ochokera kumadera a kum’mawa anabwera ku Yerusalemu. Iwo ananena kuti: ‘Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa? Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzaigwadira.’” (Mat. 2:1, 2) “Mfumu Herode itamva zimenezi, inavutika mumtima limodzi ndi Yerusalemu yense. Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe onse aakulu  ndi alembi a anthu, ndipo anayamba kuwafunsa za kumene Khristu adzabadwire.” (Mat. 2:3, 4) Choncho izi zinachititsa kuti anthu ambirimbiri adziwe kuti munthu amene adzakhale Mesiya, wabadwa. *

Lemba la Luka 3:15, limene taligwira mawu koyambirira kuja, limanena kuti Ayuda ena ankaganiza kuti mwina Yohane M’batizi ndi Khristu. Koma maganizo amenewa sanapitirire chifukwa Yohane ananena kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake. Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso ndi moto.” (Mat. 3:11) Mawu amene Yohane ananena modzichepetsawa ayenera kuti anachititsa anthu kuyembekezera kwambiri Mesiya.

Kodi Ayuda pa nthawiyo akanatha kudziwa nthawi yoti Mesiya afike chifukwa cha ulosi wa pa Danieli 9:24-27 wonena za masabata 70? Kaya mwina, koma palibe umboni wosonyeza zimenezi. Chomwe tikudziwa n’chakuti pa nthawiyo anthu anali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya masabata 70 ndipo maganizo onse anali osiyana kwambiri ndi zimene tikudziwa panopa pa nkhaniyi. *

Aesene, omwe ambiri amaganiza kuti anali kagulu kopatuka kuchiyuda, ankaphunzitsa kuti padzaoneka Amesiya awiri chakumapeto kwa zaka 490 koma sitikudziwa ngati ankanena izi potanthauzira ulosi wa Danieli umenewu. Ngakhale zikanakhala choncho, n’zokayikitsa kuti Ayuda ambiri akanamva komanso kuyendera maganizo a kagulu kodzipatulaka.

M’zaka za m’ma 100 C.E., Ayuda ena ankakhulupirira kuti masabata 70 anayamba pamene kachisi woyamba anawonongedwa mu 607 B.C.E. kufika nthawi imene kachisi wachiwiri anawonongedwa mu 70 C.E. Koma ena ankaganiza kuti ulosiwu unakwaniritsidwa pa nthawi ya Amakabeo m’zaka za m’ma 100 B.C.E. Choncho anthu ankasiyana maganizo pa nkhani ya masabata 70.

Ngati anthu akanamvetsa tanthauzo la ulosi wonena za masabata 70 pa nthawiyo, atumwi kapena Akhristu ena oyambirira akanatchula zimenezi popereka umboni wakuti Yesu Khristu ndi Mesiya chifukwa waonekera pa nthawi yake. Koma palibe umboni wosonyeza kuti Akhristu oyambirira anatchulapo zimenezi.

Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira. Anthu amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino ankakonda kutchula maulosi a m’Malemba Achiheberi amene anakwaniritsidwa mwa Yesu. (Mat. 1:22, 23; 2:13-15; 4:13-16) Koma palibe amene anatchula ulosi wa masabata 70 ponena za nthawi imene Yesu anaonekera padzikoli.

Pomaliza, tinganene kuti palibe umboni wotsimikizira kuti m’nthawi ya Yesu anthu ankadziwa zolondola pa ulosi wa masabata 70. Koma mabuku a Uthenga Wabwino amapereka zifukwa zina zomwe zinkachititsa anthu “kuyembekezera” Mesiya.

^ ndime 4 Apa Baibulo langonena kuti angelowa ankatamanda Mulungu koma silinena kuti “ankaimba.”

^ ndime 7 Mwina tingafunse kuti, Kodi okhulupirira nyenyeziwo anagwirizanitsa bwanji kuoneka kwa “nyenyezi” kum’mawa ndi kubadwa kwa “mfumu ya Ayuda”? Kodi mwina anamva za kubadwa kwa Yesu pamene ankadutsa ku Isiraeli?

^ ndime 9 Kuti muone zimene tikudziwa panopa pa ulosi wa masabata 70, werengani mutu 11 wa buku lakuti, Samalani Ulosi wa Danieli!