Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatipatsa Zinthu Zofunika Ndipo Amatiteteza

Yehova Amatipatsa Zinthu Zofunika Ndipo Amatiteteza

“Popeza wasonyeza kuti amandikonda, inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.”—SAL. 91:14.

1, 2. Kodi anthufe timasiyana bwanji pa nkhani ya makolo komanso mmene tinaphunzirira choonadi?

YEHOVA ndi amene anayambitsa banja. (Aef. 3:14, 15) Komabe, ngakhale anthu a m’banja limodzi amakhala osiyana. Mwina munakhala ndi makolo anu kuyambira muli mwana. Ena makolo awo anamwalira, mwina chifukwa cha matenda kapena ngozi. Ndipo pali ena amene makolo awo sakuwadziwa.

2 Ifeyo monga atumiki a Yehova, tinaphunzira choonadi m’njira zosiyanasiyana. N’kutheka kuti munakulira m’choonadi ndipo makolo anu anakuphunzitsani mfundo za m’Malemba. (Deut. 6:6, 7) Kapena muli m’gulu la anthu masauzande ambirimbiri amene anaphunzira choonadi kuchokera kwa atumiki ena a Yehova amene ankalalikira.—Aroma 10:13-15; 1 Tim. 2:3, 4.

3. Kodi tonse ndife ofanana m’njira ziti?

3 Ngakhale kuti ndife osiyana chonchi, timafanana m’njira zina. Tonsefe timakumana ndi mavuto chifukwa cha uchimo wa Adamu ndipo timafa. (Aroma 5:12) Komabe, popeza kuti tikulambira Mulungu woona, tinganene kuti Yehova ndi “Atate wathu.” Ponena za anthu akale amene Mulungu anawasankha, lemba la Yesaya 64:8 limati: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu.” Komanso  pamene Yesu ankaphunzitsa ophunzira ake kupemphera, anayamba ndi mawu akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mat. 6:9.

4, 5. Kodi tikamakambirana za Atate wathu Yehova, tiziganiziranso za chiyani?

4 Atate wathu wakumwamba amatisamalira komanso kutiteteza chifukwa timamukhulupirira ndipo timaitanira pa dzina lake. Pa Salimo 91:14, Yehova ananena kuti: “Popeza [munthu wolambira Mulungu woona] wasonyeza kuti amandikonda, inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.” Izi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu amapulumutsa anthu ake m’manja mwa adani awo ndipo amawateteza kuti asafafanizidwe.

5 Kuti tizikonda kwambiri Atate wathu wakumwamba, tiyeni tikambirane mfundo zitatu izi: (1) Iye amatipatsa zinthu zofunika. (2) Amatiteteza. (3) Ndi Mnzathu weniweni. Tikamakambirana mfundo zimenezi, tiziganizira mozama za ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi kuona zimene tingachite pomulemekeza monga Atate wathu. Komanso tiziganizira madalitso amene Yehova adzapereke kwa anthu amene akumuyandikira.—Yak. 4:8.

YEHOVA AMATIPATSA ZINTHU ZOFUNIKA

6. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino”?

6 Yakobo analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo.” (Yak. 1:17) Moyo umene tili nawowu ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. (Sal. 36:9) Tikamachita chifuniro cha Mulungu pa moyo wathu, timadalitsidwa kwambiri komanso timayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. (Miy. 10:22; 2 Pet. 3:13) Koma popeza tonse tinatengera uchimo wa Adamu, kodi zimenezi zingatheke bwanji?

7. Kodi Yehova anakonza bwanji njira yoti tigwirizanenso naye?

7 Yehova amatipatsadi zinthu zambirimbiri zofunika. Mwachitsanzo, iye amatisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Pajatu tonsefe tinatengera uchimo kwa Adamu, yemwe ndi kholo lathu. (Aroma 3:23) Koma chifukwa cha chikondi chake, Yehova anakonza njira yoti tigwirizanenso naye. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.”—1 Yoh. 4:9, 10.

8, 9. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amapereka zinthu zofunika m’nthawi ya Abulahamu ndi Isaki? (Onani chithunzi patsamba 16.)

8 Cha m’ma 1893 B.C.E., panachitika zinthu zina zomwe zinasonyeza chikondi chachikulu cha Yehova pokonza njira yothandizira anthu omvera kuti apeze moyo wosatha. Lemba la Aheberi 11:17-19 limati: “Mwa chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa, zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe. Choncho munthu ameneyu, amene analandira malonjezo mokondwera, anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake wobadwa yekha. Anali wokonzeka kuchita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: ‘Amene adzatchedwa “mbewu yako” adzachokera mwa Isaki.’ Koma anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa. Ndipo iye anamulandiradi kuchokera kwa akufa m’njira ya fanizo.” Mofanana ndi Abulahamu, Yehova anapereka Mwana wake Yesu Khristu chifukwa cha anthu.—Werengani Yohane 3:16, 36.

9 Isaki ayenera kuti anasangalala kwambiri Mulungu atamulanditsa kuti asaperekedwe nsembe. Mosakayikira, iye anayamikira  kwambiri pamene Mulungu anapereka nkhosa yamphongo, yomwe inakodwa m’ziyangoyango, kuti iphedwe m’malo mwa iyeyo. (Gen. 22:10-13) M’pake kuti malowa anawatcha kuti “Yehova-yire,” kutanthauza kuti “Yehova Adzapereka Zinthu Zofunikira.”—Gen. 22:14; mawu a m’munsi.

WATIPATSA MWAYI WOTI TIGWIRIZANENSO NAYE

10, 11. Kodi ndani akhala akutsogolera pa “utumiki wokhazikitsanso mtendere” ndipo achita bwanji zimenezi?

10 Pamene tikuganizira zimene Yehova watipatsa, timayamikiranso kwambiri zimene Yesu Khristu wachita. Pa nkhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “Tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse, chifukwatu onsewo anali atafa kale. Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.”—2 Akor. 5:14, 15.

11 Akhristu oyambirira ankakonda kwambiri Mulungu ndipo ankaona kuti kumutumikira ndi mwayi waukulu. Choncho analandira ndi mtima wonse “utumiki wokhazikitsanso mtendere.” Ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa inathandiza anthu amtima wabwino kuti akhale pa mtendere ndi Mulungu. Inathandizanso kuti anthuwo akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndipo kenako n’kukhala ana ake auzimu. Masiku ano, odzozedwa amagwiranso ntchito yomweyi ndipo ali ngati akazembe a Mulungu ndi Khristu. Iwo amathandiza kuti anthu amene ali ndi maganizo abwino akokedwe ndi Mulungu komanso akhale naye pa ubwenzi wabwino.—Werengani 2 Akorinto 5:18-20; Yoh. 6:44; Mac. 13:48.

12, 13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa zinthu zambiri zofunika?

12 Akhristu onse amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli amathandiza odzozedwa pa ntchito yolalikira Ufumu chifukwa choyamikiranso zimene Yehova wawapatsa. Tonsefe tikamagwira ntchito imeneyi, timagwiritsa ntchito Baibulo, lomwenso ndi mphatso yapadera yochokera kwa Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17) Tikamaligwiritsa ntchito mwaluso mu utumiki, timathandiza anthu ena kuti nawonso apeze moyo wosatha. Kuti tigwire bwino ntchitoyi, timadalira kwambiri mzimu woyera. Mzimuwu ndi mphatso inanso imene Yehova watipatsa. (Zek. 4:6; Luka 11:13) Tikawerenga Buku Lapachaka la Mboni za Yehova, timaona kuti anthu ambiri akuthandizidwa chifukwa cha ntchitoyi. Ndi mwayi waukulu kugwira ntchito imeneyi yomwe imalemekeza kwambiri Atate wathu wowolowa manjayu.

13 Ndiye poti Mulungu watipatsa zonsezi, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimachita zonse zimene ndingathe mu utumiki posonyeza kuti ndimayamikira kwambiri zimene Yehova wandipatsa? Kodi ndingatani kuti ndizilalikira uthenga wabwino mogwira mtima?’ Tikamaika zinthu za Ufumu patsogolo nthawi zonse, timasonyeza kuti timayamikira kwambiri mphatso zamtengo wapatali zimene Mulungu watipatsa. Ndiyeno tikatero, Yehova amaonetsetsa kuti tikupeza zinthu zofunika pa moyo wathu. (Mat. 6:25-33) Popeza Mulungu amatikonda, tiyeni tiziyesetsa kukondweretsa mtima wake.—Miy. 27:11.

14. Kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake?

14 Davide anaimba kuti: “Ine ndasautsika ndipo ndasauka.Yehova amandiwerengera. Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.” (Sal. 40:17) Yehova wateteza gulu la anthu ake mobwerezabwereza makamaka pamene akuzunzidwa moopsa ndi adani awo. Timayamikira kwambiri kuti Mulungu amatithandiza pa nthawi ngati zimenezi  komanso kuti amatipatsa zinthu zambiri zauzimu nthawi zonse.

YEHOVA AMATITETEZA

15. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene bambo wachikondi angatetezere mwana wake.

15 Bambo wachikondi amapereka zinthu zofunika kwa ana ake komanso amayesetsa kuwateteza. Amayesetsa kwambiri kuwapulumutsa ngati ali pa ngozi. M’bale wina amakumbukira zimene zinamuchitikira ali mwana. Iye ndi bambo ake akuchokera mu utumiki ankayenera kuwoloka mtsinje. Koma m’mawa wa tsikulo kunagwa mvula yambiri ndipo mtsinjewo unasefukira. Powoloka, anafunika kuponda miyala ikuluikulu. Mwanayu ndi amene anali patsogolo ndipo poponda mwala wina anaterereka n’kugwera m’madzi n’kumira. Kenako mwamwayi bambo ake anamugwira n’kumuvuula. Atate wathu wakumwamba amatipulumutsanso ku zinthu zoipa za m’dzikoli ndiponso kwa Satana, yemwe akulilamulira. Yehova amatiteteza bwino kuposa wina aliyense.—Mat. 6:13; 1 Yoh. 5:19.

16, 17. Kodi Yehova anathandiza ndiponso kuteteza bwanji Aisiraeli pamene ankamenyana ndi Aamaleki?

16 Zimene Yehova anachita mu 1513 B.C.E. populumutsa Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo ndiponso kuwateteza powoloka Nyanja Yofiira zimasonyeza bwino mmene iye amatetezera anthu ake. Aisiraeli atadutsa m’chipululu kulowera kuphiri la Sinai, anafika ku Refidimu.

17 Malinga ndi ulosi wa pa Genesis 3:15, Satana ayenera kuti ankafunitsitsa kuukira Aisiraeli omwe ankaoneka ngati osatetezeka. Mwachitsanzo, anachita zimenezi pogwiritsa ntchito Aamaleki, omwe anali adani a anthu a Mulungu. (Num. 24:20) Yehova anateteza anthu ake pogwiritsa ntchito anthu anayi okhulupirika omwe ndi Yoswa, Mose, Aroni  ndi Hura. Pomenyana ndi Aamalekiwo, Aisiraeli ankapambana Mose akakweza manja ake. Mikono yake ikayamba kutopa, Aroni ndi Hura ankaichirikiza. Choncho “Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yawo” chifukwa chothandizidwa ndiponso kutetezedwa ndi Yehova. (Eks. 17:8-13) Mose anamanga guwa lansembe pamalowa n’kulitcha kuti Yehova-nisi. Dzinali limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Chizindikiro Changa.”—Werengani Ekisodo 17:14, 15; mawu a m’munsi.

AMATITETEZA KU MISAMPHA YA SATANA

18, 19. Kodi Mulungu amateteza bwanji atumiki ake masiku ano?

18 Yehova amateteza anthu amene amamukonda ndi kumumvera. Adani akamatiukira, timadalira Mulungu kuti atiteteze ngati mmene Aisiraeli anachitira ku Refidimu. Yehova wakhala akuteteza gulu la anthu ake ndipo amatithandiza kuti tisagwere m’misampha ya Mdyerekezi. Iye wateteza kambirimbiri abale athu amene sanafune kulowerera ndale. Mwachitsanzo, anachita zimenezi pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany komanso m’mayiko ena m’ma 1930 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940. Tingachite bwino kuwerenga ndiponso kuganizira mbiri za moyo wa abale ndi alongo athu komanso nkhani za mu Buku Lapachaka zofotokoza mmene Mulungu watetezera anthu ake pamene ankazunzidwa. Zimenezi zidzatithandiza kuti tizidalira kwambiri Yehova monga malo athu othawirako.—Sal. 91:2.

Yehova angagwiritse ntchito Akhristu anzathu potithandiza kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mavuto (Onani ndime 18 mpaka 20)

19 Mwachikondi, Yehova amatipatsa malangizo amene amatiteteza ndipo amachita zimenezi kudzera m’gulu lake komanso mabuku amene gululi limafalitsa. Taganizirani malangizo ena othandiza amene talandira posachedwapa. Anthu ambiri m’dzikoli ali ndi makhalidwe oipa komanso amaonera zolaula, koma Yehova watipatsa malangizo othandiza kwambiri. Mwachitsanzo, watipatsa malangizo othandiza kuti tisamacheze ndi anthu olakwika pa Intaneti. *1 Akor. 15:33.

20. Kodi timatetezedwa bwanji mumpingo wachikhristu?

20 Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tikuphunzitsidwadi ndi Yehova’? Tingachite zimenezi pomvera malamulo ake. (Yes. 54:13) Mpingo wathu ndi malo otetezeka chifukwa muli akulu okhulupirika omwe amagwiritsa ntchito Malemba potipatsa malangizo othandiza. (Agal. 6:1) Yehova akutisamalira kwambiri kudzera mwa “mphatso za amuna” zimenezi. (Aef. 4:7, 8) Kodi tizitani akamatipatsa malangizo? Tiziwagonjera ndiponso kuwamvera ndi mtima wonse. Tikatero, Mulungu adzatidalitsa.—Aheb. 13:17.

21. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

21 Tiyeni tiziyesetsa kutsatira malangizo a Atate wathu wakumwamba n’kulola kuti mzimu wake woyera uzititsogolera. Tiyeneranso kuganizira mozama chitsanzo cha Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kuyesetsa kumutsanzira. Yesu analandira mphoto yaikulu chifukwa anamvera Mulungu mpaka imfa. (Afil. 2:5-11) Ifenso tidzadalitsidwa tikamadalira Yehova ndi mtima wathu wonse. (Miy. 3:5, 6) Choncho nthawi zonse tizidalira Yehova kuti azitipatsa zinthu zofunika komanso azititeteza. N’zosangalatsa ndiponso ndi mwayi waukulu kwambiri kumutumikira. Komanso tikamaganizira mfundo yakuti Mulungu ndi mnzathu weniweni, tidzayamba kumukonda kwambiri. M’nkhani yotsatira tidzakambirana chifukwa chake tikunena kuti Yehova ndi mnzathu weniweni.

^ ndime 19 Malangizo oterewa tingawapeze m’nkhani yakuti, “Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011, tsamba 3 mpaka 5. Malangizo ena ali m’nkhani yakuti, “Samalani ndi Misampha ya Mdyerekezi” komanso yakuti, “Musasunthike Popewa Misampha ya Satana” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2012, tsamba 20 mpaka 29.