Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yopanga Ophunzira Yakhudza Kwambiri Zochita Pamoyo Wanga

Ntchito Yopanga Ophunzira Yakhudza Kwambiri Zochita Pamoyo Wanga

Mbiri ya Moyo Wanga

Ntchito Yopanga Ophunzira Yakhudza Kwambiri Zochita Pamoyo Wanga

Yosimbidwa ndi Lynette Peters

Lamlungu lina m’mawa, asilikali apanyanja a ku America anabwera kudzatisamutsa. Msilikali wina wodziwa kutetekera mfuti anaimirira padenga. Asilikali ena anali gonegone pakapinga, atatcheratchera mfuti zawo. Pamene timathamanga kupita pamene panali helikopita yomwe inali kutidikira, ine ndi amishonale anzanga tinayesetsa kuika mitima m’malo. Patangotha nthawi pang’ono ndegeyo inanyamuka. Pakutha mphindi khumi tinali titakwera sitima ya panyanja yomwe inali itaima kufupi ndi gombe.

M’MAWA mwa tsiku lotsatira, tinamva kuti zigawenga zawononga ndi mabomba hotela imene tinabisalamo usiku wapitawo. Zipwirikiti zomwe zinapitirira kwa zaka zingapo ku Sierra Leone, tsopano zinafika pa nkhondo yeniyeni. Anthu onse a kumayiko ena, kuphatikizapo ifeyo, tinauzidwa kuti tiyambe kuchoka m’dzikoli nthawi yomweyo. Kuti mudziwe mmene ndinapezekera m’mavuto amenewa, dikirani ndifotokoze kuyambira pachiyambi penipeni.

Ndinakulira ku British Guiana, komwe kuyambira mu 1966 kunayamba kudziwika ndi dzina loti Guyana. Ndili wamng’ono m’ma 1950, ndinkakhala mosangalala, mopanda nkhawa zilizonse. Makolo ochuluka ankaikira mtima kwambiri pa maphunziro a ana awo, ndipo ankafuna kuti anawo azikhoza bwino kusukulu. Ndimakumbukira nthawi ina pamene kalaliki wina wa ku banki anafunsa bambo anga kuti, “N’chifukwa chiyani mumawononga ndalama zambiri chonchi kulipirira maphunziro a ana anu?” Bambo anamuyankha kuti, “Kuti anawa adzakhaledi pabwino m’tsogolo akufunika kuphunzira bwino basi.” Nthawi imeneyo, iwo ankaganiza kuti sukulu zapamwamba kwambiri ndi zimene zingakhale ndi maphunziro abwino kwambiri. Koma maganizo oterewa sanakhale nawo nthawi yaitali.

Pamene ndinali ndi zaka 11, mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zinachitika n’zakuti, tsiku lina anapita ku Nyumba ya Ufumu limodzi ndi mnzawo. Malinga ndi zimene anakamva kumeneko, sanakayikire n’komwe kuti apeza choonadi. Kenako, mayi anafotokozera mnzawo wina zimene anakamva ku Nyumba ya Ufumu kuja. Sipanapite nthawi yaitali, onse atatu anayamba kuphunzira ndi Daphne Harry (yemwe anadzadziwika ndi dzina lakuti Baird) ndi Rose Cuffie. Onse awiriwa anali amishonale. Pasanathe n’chaka chomwe, mayi ndi anzawo awiri aja anabatizidwa. Patatha zaka zisanu, bambo anga anachoka m’tchalitchi cha Seventh-Day Adventist, ndipo anabatizidwa n’kukhala Mboni.

Tili ang’onoang’ono, ana atatu oyambirirafe pa ana 10 a m’banja mwathu, tinkakonda kukacheza ku nyumba ya amishonale kumene Daphne ndi Rose ankakhala. Tikapita kumeneko, iwo ankatisimbira nkhani zokhudza utumiki wawo wa kumunda. Amishonale amenewa ankasangalala kwambiri posamalira mwakhama zosowa zauzimu za anthu ena. Chitsanzo chawo n’chimene chinandilimbikitsa kukhala ndi mtima wofuna kudzakhala mmishonale.

Komano, kodi n’chiyani chinandithandiza kukhalabe ndi cholinga chodzachita utumiki wa nthawi zonse, pamene maganizo a achibale anga ndiponso anzanga onse kusukulu anali ofuna kuphunzira kwambiri ndi kudzakhala pantchito zabwino? Panali zinthu zambiri zimene ndikanatha kukopeka nazo. Mwachitsanzo, ndikanatha kuthera nthawi yanga kuphunzira zamalamulo, zoimbaimba, ndi zachipatala. Chitsanzo chabwino cha makolo anga chinandithandiza kwambiri. Ankagwiritsa ntchito mfundo za choonadi pamoyo wawo, anali akhama pophunzira Baibulo, anaikira mtima kwambiri pothandiza anthu kuphunzira za Yehova. * Kuwonjezera apo, iwo nthawi ndi nthawi ankaitana atumiki a nthawi zonse kuti adzacheze kunyumba kwathu. Chimwemwe chimene anthu amenewa anali nacho chinandithandiza kuona ntchito yopanga ophunzira kukhala yofunika kwambiri pamoyo wanga.

Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 15. Kenako nditangomaliza maphunziro a kusekondale, ndinayamba upainiya wa nthawi zonse. Munthu woyamba amene ndinam’thandiza kupita patsogolo mpaka kufika podzipereka ndi kubatizidwa anali Philomena. Mtsikana ameneyu ankagwira ntchito pachipatala. Zinandilimbikitsa kupitiriza utumiki wa nthawi zonse poona kuti akukonda Yehova kwambiri. Pasanapite nthawi, m’boma momwe ndinkagwira ntchito yausekilitale, anafuna kundipatsa ntchito ina yabwino. Koma ndinaikana ntchitoyo, kuti ndipitirize upainiya.

Ndinkakhalabe ndi makolo anga, ndipo amishonale anapitiriza kudzacheza kunyumba kwathu. Ndinkasangalala kwambiri akamasimba nkhani zokhudza utumiki wawo. Zonsezi zinalimbikitsa kwambiri cholinga changa chodzakhala mmishonale, ngakhale kuti zinkaoneka zokayikitsa kuti zingatheke. Nthawi imeneyo, amishonale ankatumizidwa ku Guyana, ndipo amatumizidwabe mpaka pano. Tsiku lina mu 1969, ndinadabwa kwambiri komanso ndinali ndi chisangalalo chachikulu nditalandira kalata yondiitana ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Sukuluyi inali ku Brooklyn, mumzinda wa New York.

Ndinatumizidwa ku Dziko Limene Sindinkaliyembekezera

Kalasi yathu ya nambala 48 ya Sukulu ya Gileadi inali ndi ophunzira 54 ochokera ku mayiko 21. Mwa ophunzira amenewa, alongo 17 tinali osakwatiwa. Ngakhale kuti patha zaka 37 tsopano, ndikukumbukirabe bwinobwino zinthu zimene zinachitika miyezi isanu ya sukuluyo. Panali zambiri zoti tiphunzire. Kuwonjezera pa mfundo za choonadi za m’Malemba, panalinso malangizo ndi uphungu womwe ungatithandize tikadzakhala amishonale. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kutsatira malangizo, kukhala wosatengeka kwambiri ndi mafashoni, ndiponso kuchitabe khama ngakhale panthawi zovuta.

Makolo anga nthawi zonse ankatilimbikitsa kufika pamisonkhano yonse. Panalibe aliyense amene ankanamizira kudwala moti n’kuphonya misonkhano, chifukwa ankadziwiratu kuti saloledwa kuchita nawo ngakhale zinthu zina zosangalatsa. Komabe, panthawi ina pamene ndinali ku Sukulu ya Gileadi ndinayamba kukhala ndi vuto losafika pamisonkhano yonse. Lachisanu lina madzulo, ndinayesa kufotokozera Don ndi Dolores Adams zifukwa zimene sindikanapitira ku misonkhano tsikulo. Banja limeneli linkatumikira pa Beteli ndipo ndi limene linkanditenga pagalimoto yawo kupita kumisonkhano. Poyesa kufotokoza zifukwazo, ndinatchula zinthu ngati kuchuluka kwa homuweki, malipoti ofunika kukonzekera, ndi zina zotero. Ndinaona kuti sindingakwanitse kupita ku Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Titakambirana kwa kanthawi ndithu, M’bale Adams anandiuza kuti: “Chita zimene chikumbumtima chako chikukuuza.” Ndinamvera malangizo ake ndipo sindinaphonye misonkhano tsikulo. Kuchokera pamenepo, sindinalole chilichonse kundilepheretsa kupita kumisonkhano yachikhristu, pokhapokha ngati zinthu zavutitsitsa.

Chapakati pa nyengo ya maphunzirowo panayamba kumveka mphekesera yonena za mayiko amene tidzatumizidwako. Ineyo, m’mbuyo monsemo ndinkaganiza kuti ndidzatumizidwa ku Guyana, kumene kunkafunika thandizo lalikulu pantchito yolalikira. Taganizirani mmene ndinadabwira nditadziwa kuti sindidzatumizidwa kwathu. M’malo mwake, ndinatumizidwa ku Sierra Leone, kumadzulo kwa Africa. Ndinam’thokoza kwambiri Yehova chifukwa chakuti tsopano cholinga changa chokakhala mmishonale kudziko lakutali ndi kwathu chinakwaniritsidwa.

Panali Zambiri Zoti Ndiphunzire

N’tangofika ku Sierra Leone ndinaona kuti ndi dziko lokongola mochititsa kaso. Lili ndi mapiri ambiri ndiponso magombe okongola. Koma kukongola kwenikweni kwa dzikoli kwagona pa anthu ake. Anthuwo ndi achikondi ndiponso okoma mtima, zomwe zimachititsa ngakhale anthu ochokera m’mayiko ena kukhala momasuka. Izi zimathandiza kwambiri kuti amishonale atsopano aiwale kwawo. Anthu a ku Sierra Leone amakonda kucheza za miyambo ndi chikhalidwe chawo ndipo makamaka kuthandiza alendo kuphunzira Chikiliyo, chinenero chimene anthu a zinenero zosiyanasiyana m’dzikoli amamva.

Anthu olankhula Chikiliyo ali ndi miyambi yambiri yochititsa chidwi. Mwachitsanzo, mwambi wakuti Ntchito n’nja pusi, kudya n’kwa nyani, umatanthauza kuti sinthawi zonse pamene munthu wodzala mbewu ndiye amakolola. Mwambi umenewu umasonyeza bwino lomwe kusoweka kwa chilungamo komwe kwafala padziko lonse.​—Yesaya 65:22.

Ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira inali yosangalatsa kwambiri. Sikawirikawiri pamene tinkapeza munthu wosafuna kukambirana naye za m’Baibulo. Kwa zaka zambiri tsopano, amishonale ndiponso anthu ena amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali athandiza anthu a mitundu yosiyanasiyana, akulu ndi ana omwe, kuphunzira choonadi.

Erla St. Hill, munthu woyambirira kuchita naye umishonale, anali wakhama pantchito. Ankagwira ntchito za panyumba yathu ya amishonale mwakhama kwambiri ngati mmenenso ankachitira mu utumiki wa kumunda. Anandithandiza kuzindikira zinthu zambiri zimene zinali zofunika, monga kudziwana ndi anthu oyandikana nafe nyumba, kukaona Mboni zomwe zikudwala ndiponso anthu achidwi, komanso kuyesetsa kuthandiza nawo pamaliro ngati n’zotheka. Anandithandizanso kumvetsa kuti ndikatha utumiki wa kumunda, ndisamachoke m’gawo popanda kupita m’makomo mwa abale kapena alongo m’deralo n’cholinga chokawapatsa moni, ngakhale kwa nthawi yochepa chabe. Chifukwa chochita zimenezi, sizinanditengere nthawi yaitali kuti ndipeze amayi, alongo, abale, ndiponso anzanga. Komanso dziko la Sierra Leone linakhala ngati kwathu.​—Maliko 10:29, 30.

Ndinagwirizananso kwambiri ndi amishonale ena amene ndinkatumikira nawo. Mmodzi mwa iwo anali Adna Byrd, yemwe ndinkagona naye chipinda chimodzi. Iye anatumikira ku Sierra Leone cha m’ma 1978 mpaka 1981. Wina anali Cheryl Ferguson, amene ndakhala ndikugona naye m’chipinda chimodzi kwa zaka 24 zapitazi.

Nkhondo Yapachiweniweni Inabweretsa Mavuto

Mu 1997, pasanathe mwezi kuchokera pamene ofesi yatsopano ya nthambi ya ku Sierra Leone inaperekedwa kwa Mulungu, tinakakamizika kuthawa m’dzikoli chifukwa cha nkhondo, monga momwe ndatchulira poyamba paja. Zaka 6 nkhondoyi isayambe, tinakhudzidwa mtima ndi chikhulupiriro cha Mboni za ku Liberia zomwe zinathawira ku Sierra Leone chifukwa cha nkhondo kwawoko. Ena mwa iwo analibe chilichonse pamene ankafika. Ngakhale kuti anali m’mavuto oterewa, iwo ankachita utumiki wa kumunda tsiku lililonse. Zinali zokhudza mtima kwambiri kuona mmene iwo amakondera Yehova ndiponso anthu.

Popeza tsopano ifeyo ndiye tinali othawa kwawo m’dziko la Guinea, tinatsatira chitsanzo cha abale a ku Liberia. Tinapitiriza kudalira Yehova ndiponso kuika patsogolo zinthu za Ufumu. Patatha chaka chimodzi, tinabwerera ku Sierra Leone, koma pasanathe miyezi 7 nkhondo inayambanso, ndipo tinathawiranso ku Guinea.

Posapita nthawi yaitali, tinamva kuti gulu lina la zigawenga lalanda nyumba yathu ya amishonale ku Kissy, moti katundu wathu anatengedwa ndipo wina anawonongedwa. M’malo motaya mtima, tinangoyamikira kuti tili moyo. Tinali titatsala ndi katundu wochepa, komabe zochepa zomwezo zinatikwanira.

Titasamutsidwa kachiwiri ku Sierra Leone, ine ndi Cheryl, amene ndinkagona naye chipinda chimodzi, tinatsalira ku Guinea. Choncho tinafunika kuti tiphunzire Chifalansa. Ena mwa amishonale anzanga sanachedwe kuyamba kulankhula Chifalansa chomwe tinkaphunzira, osasamala ndi zimene akulakwitsa. Koma ineyo ndinkadana ndi kuti ndizilakwitsa polankhula, choncho ndinkalankhula Chifalansa pokhapokha ndikaona kuti sindingachitirenso mwina. Zimenezi zinali zondiwawa kwambiri. Tsiku ndi tsiku ndinkafunika kukumbukira kuti ndili ku Guinea, n’cholinga choti ndithandize anthu kudziwa Yehova.

Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuzolowera chinenerochi. Izi zinatheka chifukwa cha kuphunzira m’mabuku, kumva mmene ena ochidziwa bwino akulankhulira, komanso kupempha ana kumpingo, omwe samangika polankhula. Kenako, mwadzidzidzi tinalandira thandizo kuchokera ku gulu la Yehova. Kuyambira mu September 2001, Utumiki Wathu wa Ufumu wakhala ukupereka malangizo a zimene munthu anganene pogawira magazini. Malangizo amenewa ndi owonjezera pa malangizo ena amene amaperekedwa a zimene munthu anganene pogawira mabuku ndi timabuku kwa anthu a zipembedzo zosiyanasiyana. Tsopano sindidzikayikira ndikakhala mu utumiki wa kumunda, ngakhale kuti sindingathe kufotokoza zinthu bwinobwino m’Chifalansa ngati mmene ndingachitire m’chinenero changa.

Kuleredwa m’banja lalikulu kunandithandiza kwambiri kuti ndisavutike kukhala ndi anthu ambiri, moti nthawi ina tinkakhalira limodzi anthu 17. Pazaka 37 zaumishonale wanga, ndakhala limodzi ndi amishonale osiyanasiyana oposa 100. Ndi mwayi waukulu kwambiri kudziwana ndi anthu ochuluka chonchi, amakhalidwe osiyanasiyana koma onse ogwira ntchito ndi cholinga chimodzi. Ndipo ndine wosangalala kwambiri kukhala wantchito mnzake wa Mulungu komanso kutenga nawo mbali pantchito yothandiza anthu kuphunzira choonadi cha m’Baibulo.​—1 Akorinto 3:9.

Pazaka zonsezi, ndaphonya zochitika zikuluzikulu pamoyo wa azibale anga, monga maukwati ambiri a abale ndi alonga anga. Ndipo ana awo sindipita kukawaona kawirikawiri ngati mmene ndingafunire. Ndatha kuchita zimenezi chifukwa chokhala ndi mtima wodzimana. Kudzimana komweko n’kumenenso kwathandiza azibale anga kundilola kuchita utumiki waumishonale, moti nthawi zonse akhala akundilimbikitsa kuti ndipitirizebe utumikiwu.

Komabe, kunoko ndakhala ndi mwayi wokhala ndi zinthu zosiyanasiyana zimene ndinaphonya kwathu. Ngakhale kuti ndinasankha kukhala wosakwatiwa, ndili ndi ana ambiri auzimu. Ena a anawa ndi amene ndinaphunzira nawo Baibulo. Koma palinso ena amene akhalanso ana anga chifukwa choti ndi anzanga kwambiri. Ndakhalanso wosangalala kwambiri kuona ana awo akukula, kulowa m’banja, ndiponso kulera ana awo m’choonadi. Ena mwa iwo akuona ntchito yopanga ophunzira kukhala yofunika kwambiri pamoyo wawo, ngati mmene ineyo ndachitira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mayi anga anachita upainiya zaka zoposa 25, ndipo bambo anga atapuma pantchito anayamba upainiya wothandiza.

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ndinatumizidwa ku Sierra Leone, kumadzulo kwa Africa

GUINEA

SIERRA LEONE

[Chithunzi patsamba 13]

Ine ndi abale anga awiriwa tinkakonda kukacheza ndi amishonale m’ma 1950

[Chithunzi patsamba 14]

Ndili ndi anzanga a m’kalasi la nambala 48 la Sukulu ya Gileadi

[Chithunzi patsamba 16]

Mwambo wopereka kwa Mulungu ofesi ya nthambi ya ku Sierra Leone