Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupereka Nsembe Zokondweretsa Mulungu

Kupereka Nsembe Zokondweretsa Mulungu

 Kupereka Nsembe Zokondweretsa Mulungu

BUKU lina lonena za anthu a mtundu wa Aaziteki limati: “Aaziteki ankakhulupirira kuti moyo unachokera ku imfa. Iwo anapereka nsembe anthu ambiri kuposa mitundu ina yonse yakale ku America.” Bukuli limanenanso kuti: “Pamene ufumu wawo unkakula, anthuwo ankaona kuti kupereka nsembe anthu ambiri n’kumene kungalimbitse ufumuwo.” Malinga ndi zimene buku linanso limanena, chiwerengero cha anthu omwe Aaziteki ankapereka nsembe pachaka chinafika pa 20,000.

Chifukwa cha mantha ndiponso nkhawa, kapena chifukwa chodziimba mlandu ndi kudzimvera chisoni, anthu akhala akupereka nsembe zosiyanasiyana kwa milungu yawo kuyambira kalekale. Komanso, Baibulo limasonyeza kuti pali nsembe zina zimene Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, ndiye analamula kuti ziziperekedwa. Motero, sikulakwa kufunsa kuti: Kodi Mulungu amakondwera ndi nsembe zotani? Ndipo kodi nsembe n’zofunika pa kulambira masiku ano?

Nsembe Zimene Olambira Oona Ankapereka

Yehova atakhazikitsa mtundu wa Isiraeli, iye anaupatsa malangizo omveka bwino a mmene anafunira kuti Aisiraeliwo azimulambira. Ndipo pa kulambirapo anafunikanso kupereka nsembe. (Numeri, machaputala 28 ndi 29) Zina mwa nsembezo zinali zambewu; zina zinali za ng’ombe, nkhosa, mbuzi, njiwa, ndi maunda. (Levitiko 1:3, 5, 10, 14; 23:10-18; Numeri 15:1-7; 28:7) Panali nsembe zopsereza zomwe ankafunika kuzinyeketsa pamoto. (Eksodo 29:38-42) Panalinso nsembe zoyamika, zimene woperekayo ankadyako nyama yomwe yaperekedwa nsembe kwa Mulungu.​—Levitiko 19:5-8.

Nsembe zonse zimene anthu ankapereka potsatira Chilamulo cha Mose zinali mbali ya kulambira Mulungu. Komanso popereka nsembezo, anthuwo ankasonyeza kuti akuzindikira kuti iye ndiye Wolamulira Wamkulu m’chilengedwe chonse. Kudzera m’nsembezo, Aisiraeli ankasonyeza kuti akuyamikira Yehova chifukwa cha madalitso ake ndiponso chifukwa chowateteza. Komanso ankapereka nsembe kuti akhululukidwe machimo awo. Iwo ankadalitsidwa kwambiri akamatsatira bwinobwino zimene Yehova ankafuna pa kulambira.​—Miyambo 3:9, 10.

Kwa Yehova, chinthu chofunika kwambiri chinali mtima wa munthu wopereka nsembeyo. Kudzera mwa mneneri wake Hoseya, Yehova anati: “Ndikondwera nacho chifundo, si  nsembe ayi; ndi kum’dziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.” (Hoseya 6:6) Choncho, anthuwo akasiya kulambira koona n’kuyamba makhalidwe otayirira ndiponso kupha anthu osalakwa, nsembe zimene ankapereka paguwa lansembe la Yehova zinali zopanda ntchito. N’chifukwa chake, kudzera mwa Yesaya, Yehova anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? . . . ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng’ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.”​—Yesaya 1:11.

“Chimene Sindinauza Iwo”

Mosiyana kwambiri ndi Aisiraeli, anthu a m’dziko la Kanani ankapereka ana awo nsembe kwa milungu yawo, kuphatikizapo mulungu wa Aamoni wotchedwa Moleki, amene ankatchedwanso Milikomu kapena Moloki. (1 Mafumu 11:5, 7, 33; Machitidwe 7:43) Buku lina lonena za Baibulo limati: “Monga mwambo wa kulambira kwawo, Akanani ankachita zachiwerewere pamaso pa milungu yawo; ndipo kenako, ankapereka nsembe ana awo oyamba kubadwa kwa milungu yawoyo.”​—Halley’s Bible Handbook.

Kodi Yehova Mulungu ankakondwera ndi zinthu ngati zimenezi? Ayi. Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’dziko la Kanani, Yehova anawapatsa lamulo lomwe lili pa Levitiko 20:2, 3, lakuti: “Unenenso kwa ana a Israyeli ndi kuti, Aliyense wa ana a Israyeli, kapena wa alendo akukhala m’Israyeli, amene apereka mbewu zake kwa Moleke, azimupha ndithu; anthu a m’dziko am’ponye miyala. Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kum’sadza kum’chotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbewu zake kwa Moleke, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.”

Ngakhale kuti zikuoneka ngati sizingachitike, Aisiraeli ena amene anasiya kulambira koona, anayamba kuchita nawo mchitidwe wauchiwanda umenewu, wopereka ana nsembe kwa milungu yonama. Pankhaniyi, lemba la Salmo 106:35-38 limati: “Anasokonekerana nawo amitundu, naphunzira ntchito zawo: Ndipo anatumikira mafano awo, amene anawakhalira msampha: Ndipo anapereka ana awo aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda, nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana awo aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe [kwa] mafano a Kanani; M’mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.”

Pofotokoza mmene ankanyansidwira ndi mchitidwewu, kudzera mwa mneneri wake Yeremiya, Yehova anafotokoza za ana a Yuda kuti: ‘Aika zonyansa zawo m’nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse. Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m’chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m’moto ana awo aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa mumtima mwanga.’​—Yeremiya 7:30, 31.

Chifukwa cha mchitidwe  wonyansawu, m’kupita kwa nthawi Mulungu anasiya kuyanja mtundu wa Isiraeli. Mapeto ake, Yerusalemu, amene anali likulu la dziko lawo, anawonongedwa, ndipo anthuwo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. (Yeremiya 7:32-34) Motero, n’zoonekeratu kuti si Mulungu woona amene anayambitsa kupereka anthu nsembe, ndipo mchitidwewu si mbali ya kulambira koona. Kupereka anthu nsembe kwamtundu uliwonse ndi mchitidwe wauchiwanda, ndipo olambira oona a Mulungu ayenera kupewa chilichonse chokhudzana nawo.

Nsembe Yadipo ya Khristu Yesu

Komabe, ena angafunse kuti, ‘Ndiye n’chifukwa chiyani Chilamulo cha Yehova kwa Aisiraeli chinkafuna kuti azipereka nsembe zanyama?’ Mtumwi Paulo anafunsanso funso lomweli pamene anati: “Nanga tsopano Chilamulo chinakhaliraponji?” Ndiyeno anapereka yankho lakuti: “Anachiwonjezapo kuti machimo aonekere, mpaka amene ali mbewuyo atafika, amene anapatsidwa lonjezolo . . . Ndiye chifukwa chake Chilamulo chakhala namkungwi wotitsogolera kwa Khristu.” (Agalatiya 3:19-24) Nsembe zanyama zimene zinkaperekedwa potsatira Chilamulo cha Mose zinaimira nsembe yaikulu imene Yehova Mulungu anadzaperekera anthu. Nsembeyi ndi ya Mwana wake, Yesu Khristu. Yesu anafotokoza za nsembe imeneyi, yomwe Yehova anapereka chifukwa cha chikondi chake, pamene anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Chifukwa chokonda Mulungu ndiponso anthu, Yesu sananyinyirike kupereka moyo wake wangwiro womwe anali nawo padziko lapansi, kuti ukhale dipo lowombolera mbadwa za Adamu. (Aroma 5:12, 15) Yesu anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Padziko lapansi panalibe munthu aliyense amene akanatha kuwombola anthu mu ukapolo wa uchimo ndi imfa umene Adamu anawalowetsamo chifukwa cha kuchimwa kwake. (Salmo 49:7, 8) Chotero Paulo ananena kuti Yesu “analowa ndi magazi a iye mwini, osati ndi magazi a mbuzi ndi a ana ang’ombe amphongo ayi. Analowa kamodzi kwatha m’malo oyera am’katikati, natipezera chilanditso chosatha.” (Aheberi 9:12) Mwa kulandira magazi ansembe a Yesu, Mulungu ‘anafafaniza chikalata cholemba pamanja . . . chimene chinali kutitsutsa.’ Izi zikutanthauza kuti, Yehova anachotsa pangano la Chilamulo, limodzi ndi nsembe zimene Chilamulocho chinkafuna, n’kubweretsa ‘mphatso ya moyo wosatha.’​—Akolose 2:14; Aroma 6:23.

Nsembe Zauzimu

Popeza kuti nsembe zanyama ndi zambewu sizifunikanso pa kulambira koona, kodi masiku ano pali nsembe zilizonse zofunika kuti tizipereka? Inde zilipo. Yesu Khristu anapereka nsembe mwa kukhala ndi moyo wodzimana pamene ankatumikira Mulungu, ndipo pomalizira pake anapereka moyo wake nsembe kaamba a anthu. Motero, iye anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsate mosalekeza.” (Mateyo 16:24) Izi zikutanthauza kuti aliyense amene akufuna kukhala wotsatira wa Yesu, ayenera kupereka nsembe. Kodi nsembe zake ndi zotani?

Imodzi mwa nsembezi n’njakuti, munthu amene amatsatiradi Khristu amatsogoza chifuniro cha Mulungu pamoyo wake. Taonani  mmene mtumwi Paulo anafotokozera zimenezi. Iye anati: “Ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu, abale, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira. Ndipo musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.”​—Aroma 12:1, 2.

Kuwonjezera pamenepo, Baibulo limasonyeza kuti mawu athu otamanda Yehova nawonso ndi nsembe. Mneneri Hoseya anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘kupereka mawu a milomo yathu ngati ng’ombe,’ posonyeza kuti Mulungu amaona kuti mawu athu omutamanda ndi nsembe zabwino kwambiri. (Hoseya 14:2) Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Heberi kuti: “Tipereke kwa Mulungu nsembe ya chitamando, ndiyo chipatso cha milomo yathu, inde, milomo imene imalengeza dzina lake poyera.” (Aheberi 13:15) Masiku ano, a Mboni za Yehova ali pakalikiliki kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira m’mitundu yonse. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Iwo akupereka nsembe zotamanda Mulungu padziko lonse, usana ndi usiku.​—Chivumbulutso 7:15.

Kuwonjezera pa kulalikira, kuchitira ena zabwino nakonso ndi nsembe zimene zimakondweretsa Mulungu. Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:16) Ndipotu, kuti Mulungu akondwere ndi nsembe zomutamanda, munthu wopereka nsembeyo afunika kukhala ndi khalidwe labwino. Paulo anati: ‘Makhalidwe anu akhale oyenera uthenga wabwino wa Khristu.’​—Afilipi 1:27; Yesaya 52:11.

Mofanana ndi mmene zinalili kale, nsembe zonse zoperekedwa pa kulambira koona zimabweretsa chimwemwe chachikulu ndiponso madalitso a Yehova. Choncho, tiyeni tiziyesetsa kupereka nsembe zimene zimakondweretsadi Mulungu.

[Chithunzi patsamba 18]

‘Ana awo aamuna ndi aakazi . . . anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani’

[Zithunzi patsamba 20]

Mwa kulalikira uthenga wabwino ndiponso kuthandiza anthu m’njira zina, Akhristu oona amapereka nsembe zimene Mulungu amakondwera nazo