Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhulupirira Ulosi wa M’Baibulo Kumapulumutsa

Kukhulupirira Ulosi wa M’Baibulo Kumapulumutsa

 Kukhulupirira Ulosi wa M’Baibulo Kumapulumutsa

YESU ali paulendo womaliza wochoka ku kachisi ku Yerusalemu, ndipo wophunzira wake wina akumuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera.” Mtundu wa Ayuda umanyadira kwambiri kachisiyu. Komano Yesu akuyankha kuti: “Kodi ukuona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”​—Maliko 13:1, 2.

Izitu n’zovuta kwambiri kumvetsa! Miyala ina ya kachisiyu n’njaikulu kwadzaoneni. Komanso mawu a Yesu okhudza kachisiyu, yemwe ali chimake cha kulambira, akusonyezanso kuti Yerusalemu ndipo mwinanso mtundu wonse wa Ayuda, udzawonongedwa. Motero ophunzira a Yesu akum’funsitsa: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zayandikira mapeto ake n’chiyani?”​—Maliko 13:3, 4.

Yesu akuwauza kuti: “Mapeto sanafikebe.” Choyamba ophunzirawo adzamva za nkhondo, zivomezi, njala, ndi miliri m’malo osiyanasiyana. Kenaka kudzachitika zinthu zomwe zidzaike mtundu wa Ayudawo m’mavuto aakulu zedi. Inde, mtunduwo udzakhala pa “chisautso chachikulu.” Koma Mulungu adzachitapo kanthu kuti apulumutse “osankhikawo,” omwe ndi Akhristu okhulupirika. Kodi adzachita motani zimenezi?​—Maliko 13:7; Mateyo 24:7, 21, 22; Luka 21:10, 11.

Kugalukira Ufumu wa Aroma

Tsopano patha zaka 28 ndipo Akhristu a ku Yerusalemu akudikirabe mapeto. M’madera osiyanasiyana a ufumu wa Aroma mukuchitika nkhondo, zivomezi, njala, ndi miliri. (Onani bokosi lomwe lili pa tsamba 9.) Ku Yudeya kukuchitika nkhondo zambirimbiri za pachiweniweni. Komabe mumzinda wa Yerusalemu muli mtendere ndithu. Anthu akudya bwinobwino, kugwira ntchito, kulowa m’banja, ndi kubereka ana, monga mwa nthawi zonse. Anthu akuona kuti mzindawo ukhalabe wa bata chifukwa cha ulemerero wa kachisi wamkuluyo.

Cha m’ma 61 C.E. Akhristu a ku Yerusalemu akulandira kalata yochokera kwa mtumwi Paulo. Iye akuwayamikira chifukwa cha kupirira kwawo koma akuda nkhawa kuti Akhristu ena mumpingo ayamba kutayirira. Ena akupatuka pa njira yachikhristu  kapena sakukula mwauzimu. (Aheberi 2:1; 5:11, 12) Paulo akuwalimbikitsa kuti: “Chotero, musataye ufulu wanu wa kulankhula . . . Pakuti ‘kwatsala kanthawi kochepa kwambiri,’ ndipo ‘iye amene akubwerayo adzafika, mosachedwa.’ ‘Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake,’ ndipo, ‘ngati abwerera m’mbuyo, moyo wanga ulibe chikondwerero mwa iye.’” (Aheberi 10:35-38) Awatu ndi malangizo a panthawi yake. Koma kodi Akhristuwo akhalabe okhulupirika ndi kudikirirabe mwatcheru kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu? Kodi Yerusalemu watsaladi pang’ono kuwonongedwa?

Pa zaka zisanu zotsatira, ku Yerusalemu zinthu zikuipiraipirabe. Ndiyeno mu 66 C.E. bwanamkubwa wachiroma, yemwenso anali tambwali, dzina lake Florus anasowetsa ndalama zokwana matalente 17 “za misonkho” zochokera m’thumba la kachisi wopatulika. Zimenezi zikupsetsa mtima kwambiri Ayuda ndipo akugalukira boma la Aroma. Ayudawo akukhamukira ku Yerusalemu ndi kupha asilikali achiroma omwe anali kumeneko. Kenaka akulengeza kuti Yudeya salinso muulamuliro wa Aroma. Zimenezi zikuyambitsa nkhondo pakati pa Yudeya ndi Roma.

Patangotha miyezi itatu, kazembe wachiroma wa ku Suriya, dzina lake Seshasi Galasi, akulowera kum’mwera ndi asilikali okwana 30,000 kuti akathetse kugalukirako. Gulu lakeli likufika ku Yerusalemu pa Madyerero a Misasa ndipo mwamsanga likulowerera m’madera ozungulira mzindawo. Ayuda ogalukirawo alipo ochepa motero akuthawira mu mpanda wa kachisi uja. Posakhalitsa asilikali achiroma akuyamba kugumula mpandawo. Zimenezi zikuwanyansa kwambiri Ayudawo. Akuipidwa kwambiri kuona asilikali achikunja akuipitsa malo opatulika kwambiri a chipembedzo cha Chiyuda. Koma Akhristu a mumzindawu akukumbukira mawu a Yesu akuti: ‘Mukadzaona chonyansa chosakaza chitaimirira m’malo oyera, pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira ku mapiri.’ (Mateyo 24:15, 16) Kodi Akhristuwa akhulupirira mawu a Yesu amenewa n’kuwamveradi? Zimene zichitike patsogolo pake zisonyeza kuti ayenera kumvera mawuwo kuti apulumuke. Koma kodi athawa bwanji?

Mosayembekezereka ndiponso pachifukwa chosadziwika bwino, Seshasi Galasi anabwerera ndi asilikali ake n’kuthawira cha kunyanja, Ayudawo ali pambuyo kum’thamangitsa. M’njira yodabwitsayi, mzindawu unayamba wapuma kaye pang’ono kumavuto ake. Pokhulupirira chenjezo la ulosi wa Yesu, Akhristu akuthawa ku Yerusalemu n’kupita ku mzinda wa Pela. Mzindawu unali kumapiri a kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano ndipo sunakhudzidwe ndi nkhondoyi. Anathawa pa nthawi yake. Posakhalitsa Ayuda ogalukira aja akubwerera ku Yerusalemu ndipo akuyamba kukakamiza aliyense kulowa gulu lawo logalukiralo. * Apa n’kuti Akhristu  ali phee ku Pela kudikirira kuti zinthu zitha bwanji.

Zinafika Poipa Zedi

Patatha miyezi yochepa chabe, asilikali ena achiroma akubwera ku Yerusalemu. M’chaka cha 67 C.E., bwanamkubwa wina, dzina lake Vasipashani ndi mwana wake Tito akusonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali okwana 60,000. Pa zaka ziwiri zotsatira gulu la asilikali oopsali, likulowera ku Yerusalemu ndipo m’njiramo likuseseratu aliyense woyesa kulimbana nalo. Panthawiyi, n’kuti mu Yerusalemu muli nkhondo yoopsa ya pachiweniweni pakati pa Ayuda okhaokha. Iwo akuwononga nkhokwe za chakudya mumzindawu ndiponso nyumba zonse za m’dera lozungulira kachisi, ndipo Ayuda oposa 20,000 akuphedwa pa nkhondoyi. Vasipashani akuzengereza pang’ono kulowa mumzinda wa Yerusalemu. Iye akuti: ‘Mulungu wathu ndiye mkulu wa asilikali achiroma wodziwa nkhondo kuposa ine, chifukwatu adani athu akuphana okhaokha.’

Atamwalira Nero, yemwe anali mfumu ya Roma, Vasipashani akupita ku Roma kuti akatenge mpando wa ufumuwo, ndipo anasiya Tito kuti amalizitse ntchito yogonjetsa Yudeya. Tito akufika ku Yerusalemu patangotsala pang’ono kuti phwando la Pasaka la mu 70 C.E. lichitike, motero anatsekereza anthu amene anali mumzindawu ndiponso amene anabwera kudzachita phwando limeneli. Asilikali ake anagwetsa mitengo yambirimbiri m’madera a kumidzi a ku Yudeya kuti amange mpanda waukulu makilomita 7 kuzungulira mzinda umene anauzingawu. Mitengo yampandawo anaisongola kumapeto kwake. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Adani ako adzamanga mpanda wa zisonga kukuzungulira, nadzakutsekereza ndi kukusautsa kuchokera kumbali zonse.”​—Luka 19:43.

Posakhalitsa chilala chinalowa mumzindawo. Magulu a zigawenga anayamba kulanda zinthu m’makomo mwa anthu amene anafa kapena amene akudwala mwakayakaya. Chifukwa chosowa pogwira mayi wina akufika popha ndi kudya mwana wake wakhanda, ndipo n’kutheka kuti si yekhayu anachita zimenezi, n’kukwaniritsa ulosi wakuti: “Mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene . . . pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.”​—Deuteronomo 28:53-57.

Potsiriza, Aroma atazinga Yerusalemu kwa miyezi isanu, mzindawo akuugonjetsa. Akufunkha ndi kuwotcha mzinda ndi kachisi wake waulemerero  uja ndipo kenaka akuonetsetsa kuti agumula chilichonse n’kungotsala miyala yokhayokha. (Danieli 9:26) Anthu amene ophedwa akukwana 1,100,000; ndipo anthu ena 97,000 akugulitsidwa kukhala akapolo. * (Deuteronomo 28:68) Pafupifupi m’Yudeya monse simunatsalenso Myuda aliyense. N’zoona kuti mtunduwu sunaonepo zoopsa zoterezi, ndipo zinasinthiratu ndale, chipembedzo ndiponso chikhalidwe cha Ayuda. *

Panthawiyo, Akhristu omwe anathawira ku Pela anathokoza Mulungu ndi mtima wonse chifukwa chowapulumutsa. Kukhulupirira ulosi wa m’Baibulo kunawapulumutsa.

Tikaganizira nkhani imene inachitikayi, tonsefe masiku ano tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndili ndi chikhulupiriro choti chingathe kudzandipulumutsa pa chisautso chachikulu chimene chayandikirachi? Kodi ndili mu “mtundu wa anthu okhala ndi chikhulupiriro chosunga moyo”?’​—Aheberi 10:39; Chivumbulutso 7:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Wolemba mbiri wina wachiyuda, dzina lake Josephus, ananena kuti Ayuda ogalukirawo anathamangitsa Aromawo kwa masiku 7 kenaka anabwerera ku Yerusalemu.

^ ndime 15 Buku lina limati pafupifupi Myuda mmodzi pa Ayuda 7 aliwonse a mu Ufumu wa Aroma anaphedwa.

^ ndime 15 Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo, yemwe ndi Myuda, dzina lake Alfred Edersheim anati: “Aisiraeli anali asanaonepo zoopsa zoterezi n’kale lonse, ndipo ngakhale patsogolo pake sanadzaonepo zoopsa zochita kufika pamenepa.”

[Tchati patsamba 9]

Mbali za Chizindikiro Zimene Zinakwaniritsidwa M’nthawiyi

NKHONDO:

Gau (39-40 C.E.)

Kumpoto kwa Africa (41 C.E.)

Britain (43, 60 C.E.)

Armenia (58-62 C.E.)

Nkhondo zapachiweniweni ku Yudeya (50-66 C.E.)

ZIVOMEZI:

Roma (54 C.E.)

Pompeyi (62 C.E.)

Asiya Mina (53, 62 C.E.)

Krete (62 C.E.)

NJALA:

Roma, Girisi, Igupto (cha m’ma 42 C.E.)

Yudeya (cha m’ma 46 C.E.)

MILIRI:

Babulo (40 C.E.)

Roma (60, 65 C.E.)

ANENERI ONYENGA:

Yudeya (cha m’ma 56 C.E.)

[Mapu/​Chithunzi patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nkhondo ya Aroma ku Palestina kuyambira mu 67 mpaka mu 70 C.E.

Tolemayi

Nyanja ya Galileya

Pela

PEREYA

SAMARIYA

Yerusalemu

Nyanja ya Mchere

YUDEYA

Kaisareya

[Mawu a Chithunzi]

Map only: Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel​

[Chithunzi patsamba 11]

‘Adani athu akuphana okhaokha.’​—Anatero Vasipashani

[Zithunzi patsamba 11]

Mu 70 C.E. asilikali ankhondo achiroma anawononga mzinda wa Yerusalemu

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Relief: Soprintendenza Archeologica di Roma; Vespasian: Bildarchiv Preussischer Kulturbesitz/​Art Resource, NY