Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pa Nyanja ya Galileya

Pa Nyanja ya Galileya

Pa Nyanja ya Galileya

NKHANI yolembedwa pa Marko 4:35-41 imafotokoza kuti Yesu limodzi ndi ophunzira ake anakwera ngalawa kuti awolokere tsidya lina la Nyanja ya Galileya. Timawerenga kuti: “Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala. Ndipo Iye mwini [Yesu] anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro.”

M’Baibulo lonse, ndi malo okhawa pamene pakupezeka liwu lachigiriki la “mtsamiro.” Choncho, akatswiri a Baibulo sakudziwa kuti Marko potchula liwu limeneli anali kutanthauza chiyani kwenikweni. Mabaibulo ambiri amamasulira liwulo kuti “mtsamiro” kapena “khushoni.” Koma kodi mtsamirowo unali wotani? M’chinenero choyambirira, Marko anatchula za mtsamirowo m’njira yosonyeza kuti unali chipangizo cha m’ngalawamo. Ngalawa ina yotumbidwa pafupi ndi Nyanja ya Galileya mu 1986 yathandiza kuzindikira tanthauzo lothekera la liwu lachigiriki limene Marko anagwiritsa ntchito.

Kafukufuku wasonyeza kuti ngalawayo, yotalika mamita asanu ndi atatu, inali yoyendera matanga ndi nkhafi. Inali ngalawa yophera nsomba ndipo inali ndi malo apansi onyamulira katundu mmene anali kusungiramo khoka lalikulu lolemera. Ngalawa imene anaitumbayo inapezeka kuti ndi ya pakati pa 100 B.C.E. ndi 70 C.E. ndipo ingakhale mtundu wa ngalawa imene Yesu ndi ophunzira ake anagwiritsa ntchito. Shelley Wachsmann, amene anagwira nawo ntchito yotumba ngalawayo, analemba buku lakuti The Sea of Galilee Boat​—An Extraordinary 2000 Year Old Discovery. Iye anaganiza kuti “mtsamiro” umene Yesu anagonera unali thumba la mchenga lothandizira kuti ngalawa ikhazikike pamadzi. Msodzi wina wa ku Jaffa, amene anali katswiri wopha nsomba ndi wodziwa za makoka akuluakulu anati: “Pamene ndinali wamng’ono, ngalawa zimene ndinkagwiramo ntchito panyanja ya Mediterranean nthawi zonse zimakhala ndi thumba la mchenga limodzi kapena awiri. . . . Matumbawo ankakhala m’ngalawamo nthawi zonse, n’cholinga chakuti athandize ngalawayo kukhazikika bwino pamadzi. Koma pamene sitinali kuwagwiritsa ntchito, tinali kuwasunga m’malo apansi osungiramo katundu. Ndiyeno ngati wina watopa amatha kutsikira m’munsimo ndi kutenga thumba la mchengalo n’kugonera ngati mtsamiro.”

Akatswiri a Baibulo ambiri amakhulupirira kuti zimene Marko anafotokoza zikusonyeza kuti Yesu atagona anatsamira pa thumba la mchenga m’munsi mwa ngalawa. Ndiwo anali malo otetezeka kwambiri m’ngalawa kukachita namondwe. Kaya mtundu wake kwenikweni wa mtsamirowo unali wotani, chofunika ndi zimene zinachitika pambuyo pake. Mwa mphamvu ya Mulungu, Yesu anatontholetsa nyanjayo itawinduka ndi namondwe. Ngakhale ophunzirawo anafunsa nati: “Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?”