Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lamulo la Chikondi Lolembedwa M’mitima

Lamulo la Chikondi Lolembedwa M’mitima

 Lamulo la Chikondi Lolembedwa M’mitima

“Ndidzaika chilamulo changa m’kati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba.”​—YEREMIYA 31:33.

1, 2. (a) Kodi tsopano tikambirana chiyani? (b) Kodi Yehova anadzionetsera motani pa phiri la Sinai?

M’NKHANI ziwiri zapitazo, tinaphunzira kuti pamene Mose anatsika kuchokera m’phiri la Sinai, nkhope yake inanyezimira ndi ulemerero wa Yehova. Tinakambirananso za chophimba nkhope chimene Mose anadziphimba nacho. Tsopano tiyeni tikambirane nkhani ina yofananako, koma yokhudza Akristu a masiku ano.

2 Pamene Mose anali m’phirimo, analandira malangizo kwa Yehova. Atasonkhana m’munsi mwa phiri la Sinai, Aisrayeliwo anaona ndi maso awo mphamvu zodabwitsa kwambiri zimene Mulungu anadzionetsera nazo. “Panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liwu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. . . . Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m’moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m’ng’anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.”​—Eksodo 19:16-18.

3. Kodi Yehova anawapereka motani Malamulo Khumi kwa Israyeli, ndipo n’chiyani chimene mtunduwo unazindikira panthawiyo?

3 Yehova analankhula kwa anthuwo kupyolera mwa mngelo, powapatsa Malamulo Khumi aja. (Eksodo 20:1-17) Choncho, zinali zosakayikitsa kuti malamulo amenewo anali ochokera kwa Wamphamvuyonse. Yehova ndiye analemba malamulowo pamagome a miyala​—inde, magome amene Mose anawaswa poona Aisrayeli akulambira mwana wa ng’ombe wagolide. Yehova analembanso kachiwiri malamulowo pamiyala. Panthawiyi, pamene Mose anali kutsika m’phirimo atanyamula magomewo, nkhope yake inali kunyezimira. Pamenepo, onse anazindikira kuti malamulowo anali ofunika kwambiri.​—Eksodo 32:15-19; 34:1, 4, 29, 30.

4. N’chifukwa chiyani Malamulo Khumi anali ofunika kwambiri?

4 Magome awiri a Malamulo Khumiwo anaikidwa m’likasa la chipangano m’Chipinda Chopatulikitsa m’chihema, ndipo pambuyo pake anaikidwa m’kachisi. Malamulowo anapereka mfundo zimene zinali maziko a Chilamulo cha Mose. Anakhalanso maziko oyendetsera boma laumulungu la mtundu wa Israyeli. Malamulo amenewo anali umboni wakuti Yehova anali ndi mtundu wapadera, mtundu wosankhika, umene anali kuutsogolera.

5. Kodi malamulo a Mulungu kwa Israyeli anasonyeza chikondi chake n’njira zotani?

5 Malamulo amenewo anasonyeza zambiri  za Yehova, makamaka mmene ankawakondera anthu ake. Inde, malamulowo anakhalatu mphatso yamtengo wapatali kwa amene anawamvera! Katswiri wina analemba kuti: “Chikhalire, palibe malamulo alionse okhazikitsidwa ndi anthu . . . amene anaposa, kapena kufanana, ngakhale kuyandikirako ku mawu khumi a Mulungu amenewa.” Ponena za Chilamulo chonse cha Mose, Yehova anati: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.”​—Eksodo 19:5, 6.

Lamulo Lolembedwa mu Mtima

6. Kodi ndi lamulo liti limene lakhala loposa malamulo olembedwa pamiyala?

6 Inde, malamulo a Mulungu amenewo anali opindulitsa kwambiri. Komabe, kodi mukudziwa kuti Akristu odzozedwa ali ndi lamulo lamtengo wapatali kuposa malamulo olembedwa pamiyala aja? Yehova ananeneratu za kuchita pangano latsopano losiyana ndi pangano la Chilamulo limene anapangana ndi mtundu wa Israyeli. Iye anati: “Ndidzaika chilamulo changa m’kati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba.” (Yeremiya 31:31-34) Yesu, amene ndiye Nkhoswe ya chipanganocho, sanapatse otsatira ake mndandanda wa malamulo olembedwa. Iye anakhomereza lamulo la Yehova m’maganizo ndi m’mitima ya ophunzira ake mwa zinthu zimene ananena ndi kuchita.

7. Kodi “lamulo la Kristu” choyamba linapatsidwa kwa yani, ndipo analilandira pambuyo pake ndani?

7 Lamulo limeneli limatchedwa “lamulo la Kristu.” Choyamba linapatsidwa ku mtundu wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” osati kwa mtundu wakuthupi wa Israyeli, amene anali mbadwa za Yakobo. (Agalatiya 6:2, 16; Aroma 2:28, 29) Akristu odzozedwa ndi mzimu ndiwo Israyeli wa Mulungu. M’kupita kwa nthawi, “khamu lalikulu” linagwirizana nawo. Khamu limeneli ndilo anthu ochokera m’mitundu yonse amene nawonso akufuna kupembedza Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 10; Zekariya 8:23) Monga “gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi,” magulu onse awiriwo amasunga “lamulo la Kristu,” mwa kulola kuti liwatsogolere pa zonse zimene amachita.​—Yohane 10:16.

8. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Chilamulo cha Mose ndi lamulo la Kristu?

8 Mosiyana ndi Aisrayeli akuthupi, amene anakakamizika kusunga Chilamulo cha Mose chifukwa chobadwira mu mtundu wa Israyeli, Akristu amasunga lamulo la Kristu mwa kusankha kwawo. Pachifukwa chimenechi, mtundu wa munthu komanso malo kumene anabadwira si zinthu zofunikira ayi. Iwo amaphunzira za Yehova ndi njira zake, ndipo ndi ofunitsitsa kuchita chifuniro chake. Popeza lamulo la Mulungu lili “m’kati mwawo,” lolembedwa “m’mtima mwawo,” titero kunena kwake, chachikulu chimene Akristu odzozedwa amakhalira omvera Mulungu si kuopa kuti iye adzalanga anthu osamvera ayi. Komanso sikuti amamumvera chifukwa chokhala okakamizidwa  kutero, ayi. Amamumvera makamaka chifukwa cha chinthu china chofunika kwambiri ndi champhamvu zedi; ndicho lamulo la Mulungu limene lili m’mitima mwawo. A nkhosa zinanso n’chimodzimodzi.

Malamulo Ozikidwa pa Chikondi

9. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti chikondi ndicho mfundo yaikulu ya malamulo a Yehova?

9 Mfundo yaikulu ya malamulo a Yehova ndi malangizo ake onse tikhoza kuitchula ndi liwu limodzi: chikondi. N’chimene chakhala maziko a kupembedza koyera, ndipo chidzapitiriza kutero. Pamene Yesu anafunsidwa za lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo, anayankha kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” Lachiwiri linali lakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” Kenako anati: “Pa malamulo awa awiri m’pokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.” (Mateyu 22:35-40) Mwa mawuwa, Yesu anasonyeza kuti, si Chilamulo chokha chophatikizapo Malamulo Khumi chimene chinazikidwa pa chikondi, komanso ngakhale Malemba Achihebri onse.

10. Kodi timadziwa bwanji kuti chikondi ndicho maziko a lamulo la Kristu?

10 Kodi kukonda kwathu Mulungu ndi mnansi n’kumenenso kuli maziko a lamulo lolembedwa m’mitima ya Akristu? Zili choncho kumene! Lamulo la Kristu limaphatikizapo kukonda Mulungu ndi mtima wonse, ndipo limaphatikizaponso lamulo latsopano lakuti, Akristu ayenera kukhala ndi chikondi chodzipereka kwa wina ndi mnzake. Inde, ayenera kukhala ndi chikondi chimene Yesu anali nacho. Mwa mtima wonse, iye anataya moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. Anaphunzitsa ophunzira ake kukonda Mulungu ndi kukondana wina ndi mnzake, ngati  mmene iye anawakondera. Chikondi chapadera chimene amakhala nacho kwa wina ndi mnzake ndicho khalidwe lalikulu limene anthu amawadziwira Akristu oona. (Yohane 13:34, 35; 15:12, 13) Yesu analangiza ophunzira ake kuti azikonda ngakhale adani awo.​—Mateyu 5:44.

11. Kodi Yesu anasonyeza motani chikondi chake kwa Mulungu ndi anthu?

11 Yesu anapereka chitsanzo chabwino koposa cha kusonyeza chikondi. Pamene anali mzimu wamphamvu kumwamba, anavomereza mwayi wakuti adzachite chifuniro cha Atate wake pa dziko lapansi. Kuwonjezera pa kupereka moyo wake kuti anthu ena akakhale ndi moyo wosatha, iye anaphunzitsa anthu mmene angakhalire ndi moyo waphindu. Anali wodzichepetsa, wokoma mtima, ndi woganizira ena, pothandiza awo amene anali opsinjika ndi oponderezedwa. Anagawiranso anthu “mawu a moyo wosatha,” mwa kuwathandiza mosatopa kuti adziwe Yehova.​—Yohane 6:68.

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kukonda kwathu Mulungu ndi kukonda kwathu mnansi n’zosalekanitsika?

12 Kwenikweni, kukonda kwathu Mulungu ndi kukonda kwathu mnansi n’zosalekanitsika. Mtumwi Yohane ananena kuti: “Chikondi chichokera kwa Mulungu, . . . Munthu akati, kuti, ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:7, 20) Yehova ndiye gwero la chikondi, komanso ndiye chitsanzo changwiro pa kusonyeza chikondi. Chilichonse chimene amachita, amachita chifukwa cha chikondi. Ifeyo timatha kukonda anthu ena chifukwa chakuti anatipanga m’chifanizo chake. (Genesis 1:27) Mwa kusonyeza chikondi kwa anansi athu, timasonyeza chikondi kwa Mulungu.

Kukonda Mulungu Ndiko Kumumvera

13. Ngati tikufuna kuti tim’konde Mulungu, kodi tiyenera kuchita chiyani choyamba?

13 Kodi tingathe bwanji kum’konda Mulungu amene sitimuona? Chofunika choyambirira ndicho kum’dziwa kaye. N’zosatheka kum’konda ndi mtima wonse munthu amene sitim’dziwa. Ndiye chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tim’dziwe Mulungu mwa kuwerenga Baibulo, mwa kupemphera, ndi mwa kuyanjana ndi anthu amene amam’dziwa kale ndi kum’konda. (Salmo 1:1, 2; Afilipi 4:6; Ahebri 10:25) Makamaka Mauthenga Abwino anayi ndi othandiza kwambiri. Amalongosola makhalidwe a Yehova amene Yesu Kristu anawasonyeza m’moyo wake ndi utumiki wake. Chikhumbo chathu chofuna kukhala omvera kwa Mulungu ndi otengera makhalidwe ake, chimakhala champhamvu mowirikiza, pamene tim’dziwa ndi kuzindikira chikondi chimene anasonyeza kwa ife. Inde, kukonda Mulungu kumafuna kukhala omumvera.

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malamulo a Mulungu si olemetsa?

14 Pamene tikonda anthu ena, timakhala tikudziwa zimene amakonda ndi zimene sakonda, ndipo timachita nawo zinthu motsatira zimenezo. Sitifuna kukhumudwitsa anthu amene timawakonda. “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu,” anatero mtumwi Yohane, “kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Malamulowo si olemetsa, ndipo si ambirimbiri. Chikondi n’chimene chimatitsogolera. Sitili ndi mndandanda wa malamulo ambirimbiri ofunika kuti tiwaloweze pamtima kuti azititsogolera pofuna kuchita chilichonse ayi; chikondi chathu kwa Mulungu n’chimene chimatitsogolera. Ngati tikonda Mulungu, timasangalala kuchita chifuniro chake. Tikatero, timasangalatsa Mulungu, ndiponso ife eni timapindula. Malangizo ake amakhala ndi ubwino kwa ife nthawi zonse.​—Yesaya 48:17.

15. Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kutsanzira Yehova? Fotokozani.

15 Chikondi chathu kwa Mulungu chimatilimbikitsa kutengera makhalidwe ake. Pamene tikonda munthu wina, timasirira makhalidwe ake ndipo timayesetsa kuti tifanane naye. Taganizirani ubale wa pakati pa Yehova ndi Yesu. Iwo anali limodzi kumwamba mwinamwake kwa zaka mabiliyoni ambirimbiri. Pakati pawo panali chikondi chenicheni chozama. Yesu anafanana kwambiri ndi Atate wake wakumwamba moti anatha  kuuza ophunzira ake kuti: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Pamene tidziwa zambiri za Yehova ndi Mwana wake ndi kuwamvetsa, timafuna kuti tifanane nawo. Chifukwa cha chikondi chathu kwa Yehova, limodzi ndi chithandizo cha mzimu wake woyera, tidzatha ‘kuvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo tidzavala watsopano.’​—Akolose 3:9, 10; Agalatiya 5:22, 23.

Chikondi Chionekere

16. Kodi ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa ena imasonyeza motani chikondi chathu kwa Mulungu ndi mnansi?

16 Monga Akristu, chikondi chathu kwa Mulungu ndi mnansi chimatilimbikitsa kutenga mbali pantchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Mwakutero, timakondweretsa Yehova Mulungu, “amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:3, 4) Chotero, timatha kumakhala achimwemwe pothandiza ena kuti lamulo la Yesu lilembedwe m’mitima yawo. Ndipo timakondwera poona miyoyo yawo ikusintha ndi kuyamba kusonyeza makhalidwe ofanana ndi a Yehova. (2 Akorinto 3:18) Kunena zoona, kuthandiza anthu ena kuti adziwe Mulungu ndi mphatso yamtengo wapatali yoposa iliyonse imene tingawapatse. Awo amene amalola kupalana ubwenzi ndi Yehova angathe kukhala naye paubwenzi wabwino wotero kwamuyaya.

17. N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kukulitsa chikondi chathu kwa Mulungu ndi mnansi, m’malo mongofuna chuma?

17 Tikukhala m’dziko limene anthu ochuluka amaika patsogolo chuma ndi kuchikonda kwambiri. Komabe, chuma sichikhalitsa. Chitha kubedwa kapena kuwonongeka ndi dzimbiri. (Mateyu 6:19) Baibulo limatichenjeza kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku  nthawi yonse.” (1 Yohane 2:16, 17) Inde, Yehova adzakhala ku nthawi zonse, ndipo amene amam’konda ndi kum’tumikira adzateronso. Chotero, kodi si chinthu chanzeru kuti tikulitse chikondi chathu kwa Mulungu ndi anthu anzathu, m’malo mongofuna zinthu za dzikoli, zimene kwenikweni n’zosakhalitsa?

18. Kodi mmishonale wina anasonyeza motani chikondi chodzipereka ndi mtima wonse?

18 Awo amene amakulitsa chikondi amabweretsa chitamando kwa Yehova. Taganizirani za Sonia, amene ndi mmishonale m’dziko la Senegal. Iye anali kuphunzira Baibulo ndi mayi wina dzina lake Heidi, amene anatenga matenda a Edzi kwa mwamuna wake wosakhulupirira. Mwamuna wakeyo atamwalira, Heidi anabatizidwa, koma posakhalitsa anayamba kudwala kwambiri, mpaka anagonekedwa m’chipatala. Sonia anati: “A chipatala anayesetsa kuthandiza, koma anali ochepa. Abale ndi alongo ku mpingo anapemphedwa kuti azim’samalira kuchipatalako. Tsiku lachiwiri usiku, ndinakhala pamphasa pafupi ndi bedi lake. Ndinathandiza kum’samalira usikuwo mpaka pamene anamwalira. Dokotala amene anali kum’yang’anira anati: ‘Vuto lathu lalikulu n’lakuti ngakhale achibale enieni a wodwala, kawirikawiri amangom’siya yekha akaona kuti akudwala matenda a Edzi. Tsono zikutheka bwanji kuti iweyo, amene si mbale wake, amenenso umachokera ku dziko lina, komanso mzungu, n’kulolera kuika moyo wako pachiswe kusamalira matenda ngati amenewa?’ Ndinafotokoza kuti kwa ine, Heidi anali mbale wanga weniweni, ngati kuti anali wa bere limodzi. Chifukwa chakuti ndinapeza mbale wanga watsopano ameneyu, ndinali wosangalala kumusamalira.” Ubwino wakenso ndi wakuti, matenda a Heidi sanam’khudze Sonia pamene anali kum’samalira mwachikondi.

19. Pokhala ndi lamulo la Mulungu m’mitima mwathu, kodi tiyenera kusalekerera mwayi wochita chiyani?

19 Timapeza zitsanzo zambiri za atumiki a Yehova amene anasonyeza chikondi chodzipereka ndi mtima wonse. Palibe mndandanda wokhazikitsidwa wa malamulo amene anthu amadziwira anthu a Mulungu masiku ano. M’malo mwake, timaona kukwaniritsidwa kwa zimene zinalembedwa pa Ahebri 8:10 kuti: “Ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m’nzeru zawo, ndipo pamtima pawo ndidzawalemba iwo; ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu.” Tiyenitu nthawi zonse tizikonda lamulo la chikondi limene Yehova analemba m’mitima yathu. Tiyeni tigwiritse ntchito mpata uliwonse kusonyeza chikondicho.

20. N’chifukwa chiyani lamulo la Kristu lili chuma chamtengo wapatali?

20 N’zosangalatsatu kutumikira Mulungu limodzi ndi gulu la abale la padziko lonse, limene limasonyeza chikondi choterocho! Awo amene ali ndi lamulo la Kristu m’mitima mwawo, amasangalala ndi chuma chamtengo wapatali chimenecho m’dziko lino lopanda chikondi. Sikuti amasangalala ndi chikondi cha Yehova chokha, komanso amasangalala ndi chikondi champhamvu chimene chili pakati pa abale. “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimakhala m’mayiko osiyanasiyana, zimalankhula zinenero zosiyanasiyana, komanso ndi amafuko osiyanasiyana, zimasangalala ndi umodzi wa chipembedzo umene palibe wina wofanana nawo. Umodzi umenewu umabweretsa dalitso la Yehova. Wamasalmo analemba kuti: “Pamenepo [pakati pa anthu ogwirizana m’chikondi] Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.”​—Salmo 133:1-3.

Kodi Mungayankhe?

• Kodi n’chifukwa chiyani Malamulo Khumi anali ofunika kwambiri?

• Kodi lamulo lolembedwa m’mitima n’chiyani?

• Kodi chikondi chili ndi mbali yanji pa “lamulo la Kristu”?

• Kodi tingasonyeze chikondi chathu kwa Mulungu ndi mnansi m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 25]

Aisrayeli anali ndi malamulo olembedwa pa magome a miyala

[Zithunzi patsamba 26]

Akristu ali ndi lamulo la Mulungu lolembedwa m’mitima mwawo

[Chithunzi patsamba 28]

Sonia limodzi ndi mtsikana wa ku Senegal pa msonkhano wachigawo wa mu 2004