Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chodzimana Zinthu Zochepa

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chodzimana Zinthu Zochepa

 Mbiri ya Moyo Wanga

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chodzimana Zinthu Zochepa

YOSIMBIDWA NDI GEORGE NDI ANN ALJIAN

Ine ndi mkazi wanga sitinkaganiza m’pang’ono pomwe kuti tsiku lina tidzasokoneza mawu akuti “mphunzitsi” ndi mawu akuti “mbeŵa.” Sitinalingalirepo kuti tidzakhala tikuganizira zilembo zachilendo pofuna kulankhulana ndi anthu a kumayiko a ku Asia tili ndi zaka za m’ma 60. Koma zimenezi n’zimene ine ndi Ann tinachita chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980. Talekani tikuuzeni mmene tapezera madalitso ambiri chifukwa chodzimana zinthu zochepa m’zaka zapitazo.

NDINABADWIRA m’banja lochokera ku Armenia ndipo ndinali wachipembedzo cha Armenian Church. Ann anali wa Roma Katolika. Tinakambirana za zikhulupiriro zathu zachipembedzo n’kugwirizana chimodzi pamene tinakwatirana mu 1950. Ine ndinali ndi zaka 27 pamene Ann anali ndi zaka 24. Tinkakhala m’nyumba ina imene inali pamwamba pa nyumba imene ndinkachitiramo bizinesi yanga yochapa zovala ku Jersey City, New Jersey, m’dziko la United States of America. Panthaŵi imeneyo, ndinali nditachita bizinesi yangayi kwa zaka pafupifupi zinayi.

Mu 1955 tinagula nyumba yokongola ya zipinda zitatu ku Middletown, ku New Jersey. Nyumbayo inali pa mtunda wa makilomita 60 kuchokera kumene kunali bizinesi yangayo, kumene ndinali kugwira ntchito masiku asanu ndi limodzi pa mlungu. Nthaŵi zonse ndinkafika usiku kunyumba. Nthaŵi imene ndinkalankhula ndi Mboni za Yehova ndi pamene zinkabwera nthaŵi zina ku bizinesi yanga n’kumandipatsa mabuku ophunzirira Baibulo. Ndinkaŵerenga mabukuwo mwachidwi kwambri. Ngakhale kuti bizinesi yangayo inkandidyera nthaŵi yambiri ndiponso ndinkaiganizira  kwambiri, ndinayamba kulemekeza kwambiri Baibulo.

Pasanapite nthaŵi yaitali ndinadzatulukira kuti wailesi ya Watchtower, ya WBBR, inkaulutsa nkhani zofotokoza Baibulo panthaŵi imene ndinali kuyenda pagalimoto popita ndiponso pobwerako ku bizinesi yangayo. Ndinkamvetsera mwatcheru nkhani zimenezo, ndipo chidwi changa chinakula n’kufika poti ndinapempha Mboni kuti zidzandichezere. Mu November 1957, George Blanton anafika kunyumba kwanga ndipo anayamba kuphunzira nane Baibulo.

Banja Lathu Lonse Linayamba Kulambira Koona

Kodi Ann anamva bwanji ndi zimenezi? Lekani akuuzeni.

“Poyamba ndinkatsutsa kwambiri. Ndinkasokoneza kwambiri a George akamaphunzira Baibulo moti anaganiza zomakaphunzira ku malo ena, ndipo anachita zimenezo kwa miyezi isanu ndi itatu. M’nthaŵi imeneyo, a George anayamba kumapezeka pamisonkhano Lamlungu ku Nyumba ya Ufumu. Ndinazindikira kuti anaikirapo mtima kwambiri pankhani yophunzira Baibulo chifukwa limeneli ndi tsiku lokhalo limene sankagwira ntchito. Koma anapitirizabe kukhala mwamuna komanso tate wabwino, motinso anali wabwino kuposa poyamba, ndipo ndinayamba kusintha maganizo. Nthaŵi zina ndikamapukuta pa tebulo, pakakhala kuti palibe amene akundiona, ndinkatenga magazini ya Galamukani! imene a George ankayika patebulopo nthaŵi zonse, n’kumaŵerenga. Nthaŵi zina a George ankandiŵerengera nkhani za mu Galamukani! zimene sizinkafotokoza mwachindunji ziphunzitso zachipembedzo koma zimene nthaŵi zonse zinkafotokoza za Mlengi.

“Tsiku lina madzulo a George atapita kukachita phunziro lawo la Baibulo ndi Mbale Blanton, ndinatenga buku limene mwana wathu wa zaka ziŵiri, dzina lake George, anaika patebulo pambali pa bedi langa. Linali lofotokoza za chiyembekezo cha anthu akufa. Ngakhale kuti ndinali nditatopa, ndinayamba kuliŵerenga chifukwa chakuti agogo anga aakazi anali atangomwalira kumene, ndipo ndinataya mtima kwambiri. Ndinaona ndiponso kumvetsa mwamsanga choonadi cha m’Baibulo chakuti anthu akufa sakuvutika kwinakwake ndiponso kuti adzakhalanso ndi moyo akadzaukitsidwa m’tsogolo. Nthaŵi yomweyo ndinakhala tsonga papedipo, n’kumaŵerenga mwachidwi komanso kudula mzere kunsi kwa mfundo zimene ndinafuna kuti ndidzawasonyeze a George akabwera kuchokera kophunzira Baibulo.

“Amuna angawa sanakhulupirire kuti ndine ndemwe amene ndinali wotsutsa uja. Pamene ankachoka panyumba, ndinatsutsa kwambiri, koma tsopano ndinali wosangalala ndi choona cha m’Baibulo chimene ndinaphunzira. Tinakhala maso usiku wonse mpaka chakum’maŵa tikukambirana za m’Baibulo. A George anafotokoza cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi. Ndinawapempha usiku womwewo kuti azichitira phunziro lawo la Baibulolo panyumba pomwepo kuti ndizichita nawo.

“Mbale Blanton ananena kuti zingakhale bwino kuti ana athu azichita nawonso phunzirolo. Tinaganiza kuti anali aang’ono kwambiri, popeza wina  anali ndi zaka ziŵiri pamene winayo anali ndi zaka zinayi zokha. Komabe, Mbale Blanton anatisonyeza lemba la Deuteronomo 31:12 limene limati: ‘Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, . . . kuti amve, ndi kuti aphunzire.’ Tinayamikira kwambiri langizo limenelo ndipo tinakonza zoti ana athuwo aziyankha pa phunziro la Baibulolo. Tinkakonzekera pamodzi ndemanga, koma sitinkawauza zoti adzanene. Tikuganiza kuti zimenezi zinathandiza kuti ana athuwo achitenge choonadi kukhala chawochawo. Tidzayamikira mpaka kalekale langizo limene Mbale Blanton anatipatsa lothandiza kuti banja lathu likule mwauzimu.”

Mavuto Amene Anachititsa Kuti Tidzimane

Tsopano popeza tonse tinali kuphunzira Baibulo, panali mavuto atsopano amene tinafunikira kuwathetsa. Popeza bizinesi yanga inali kutali, nthaŵi zambiri ndinkafika panyumba cha m’ma naini koloko usiku. Chifukwa cha zimenezi, sindinkatha kupezeka pa misonkhano ya pakati pa mlungu, ngakhale kuti ndinkapitako Lamlungu lokha. Panthaŵi imeneyi n’kuti Ann akuchita nawo misonkhano yonse ndipo anali kupita patsogolo mofulumira kwambiri. Inenso ndinkafuna kumapezeka pa misonkhano yonse komanso kuchititsa phunziro la banja lopindulitsa. Ndinaona kuti ndinafunika kudzimana zinthu zina. Motero, ndinaganiza zochepetsa nthaŵi imene ndinali kuchita bizinesi yangayo, ngakhale kuti zimenezo zinachititsa makasitomala anga ena kusiya kubwera ku bizinesi yanga.

Zimenezi zinathandiza kwambiri. Phunziro la banja tinkaliona kukhala lofunika kwambiri monga mmene tinali kuonera misonkhano isanu ya mlungu ndi mlungu ya ku Nyumba ya Ufumu. Phunziro la banjali tinalitcha msonkhano wathu wachisanu ndi chimodzi. Zimenezo zinatanthauza kulipezera tsiku ndi nthaŵi yapadera. Tinakonza kuti tizichita Lachitatu mlungu uliwonse nthaŵi ya 8:00 madzulo. Nthaŵi zina tikatha kudya chakudya chamadzulo n’kumaliza kutsuka mbale ku kitchini, wina wa ife ankanena kuti, “Nthaŵi ya ‘msonkhano’ yatsala pang’ono kukwana!” Ann ankayambapo kutsogolera phunzirolo ndikachedwa, ndipo ndinkamulandira ndikangofika.

Chinthu china chimene chinatithandiza kukhala olimba ndiponso ogwirizana monga banja chinali kuŵerenga pamodzi lemba la tsiku m’maŵa. Komabe, panali vuto pokonza zimenezi. Aliyense ankadzuka panthaŵi yosiyana ndi ena. Tinakambirana zimenezi ndipo tinaganiza kuti tonse tizidzuka panthaŵi yofanana, kudya chakudya cha m’maŵa pa 6:30, ndi kukambirana lemba la tsiku pamodzi. Zimenezi zinatipindulitsa kwambiri. Ana athu atakula, anasankha kukatumikira pa Beteli. Tinaona kuti kukambirana lemba la tsiku ndi tsiku kumeneku kunathandiza pa moyo wawo wauzimu.

Mwayi Wotumikira Titabatizidwa Unachititsa Kuti Tidzimane Kwambiri

Ndinabatizidwa m’chaka cha 1962, ndipo panthaŵiyi n’kuti nditachita bizinesi yanga ija kwa zaka 21. Ndinaigulitsa ndipo ndinayamba kugwira ntchito yolembedwa kudera lomwe tinali kukhalalo kuti ndizikhala pafupi ndi mkazi ndi ana anga kuti tithe kutumikira Yehova pamodzi. Zimenezi zinachititsa kuti tipeze madalitso ambiri. Tinakhala ndi cholinga chakuti tonse tidzachite utumiki wa nthaŵi zonse. Zimenezo zinayamba kuchitika kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970 pamene mwana wathu wamkulu, Edward, anakhala mtumiki wa nthaŵi zonse, kapena kuti mpainiya wokhazikika, atangomaliza kumene sukulu ku sekondale. Patapita nthaŵi yochepa, mwana wathu George anayambanso upainiya ndipo posakhalitsa, Ann anayambanso. Ndinkalimbikitsidwa kwambiri ndi anthu atatu onseŵa, chifukwa ankandiuza zimene akumana nazo muutumiki wa kumunda. Monga banja, tinkakambirana mmene tingafeŵetsere moyo wathu kuti tonse tithe kuchita utumiki wa nthaŵi zonse. Tinaganiza zogulitsa nyumba yathu. Tinali titakhala m’nyumbayo kwa zaka 18 ndipo ana anthu tinawalerera mnyumba imeneyo. Tinkaikonda kwambiri nyumba yathuyo, koma Yehova anadalitsa zimene tinasankha kuchita zogulitsa nyumbayo.

Edward anaitanidwa kukatumikira ku Beteli mu 1972, ndipo nayenso George anaitanidwa mu 1974. Ngakhale kuti ine ndi Ann tinawasoŵa kwambiri  anyamataŵa, sitinkalimbana ndi kuganizira mmene zinthu zikanakhalira bwino akanakhala kuti anali nafe pafupi, kukwatira, ndi kukhala ndi ana. M’malo mwake, tinkasangalala kuti ana athu anali kutumikira Yehova pa Beteli. * Tikugwirizana ndi zimene lemba la Miyambo 23:15 limanena pamene limati: “Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa.”

Kuyamba Upainiya Wapadera

Ana athu onse atapita ku Beteli, tinapitiriza upainiya. Ndiyeno tsiku lina mu 1975, tinalandira kalata yotipempha kuti tikayambe ntchito ya upainiya wapadera m’gawo losagaŵiridwa ku Clinton County, ku Illinois. Zinali zodabwitsatu zimenezo! Zimenezi zinatanthauza kuti tinafunika kuchoka ku New Jersey, kumene tinali pafupi ndi ana athu omwe anali ku New York, ndiponso kumene tinali ndi anzathu ndi achibale. Komabe, tinaiona kuti ndi ntchito imene Yehova watipatsa ndipo tinadzimana zinthu zimenezi, zimene zinachititsa kuti tipeze madalitso ena atsopano.

Patapita miyezi ingapo tikugwira ntchito m’gawo losagaŵiridwa, tinayamba kukhala ndi misonkhano mu holo ina ya mderalo ku Carlyle, Illinois. Koma tinkafuna malo okhazikika oti tizisonkhanirapo. Mbale wina wa mderalo ndi mkazi wake anapeza malo amene anali ndi kanyumba kakang’ono amene tinachita lendi. Tinayeretsa malo onsewo kuphatikizapo kanyumbako ndi zimbuzi, ndipo tinawasintha n’kukhala malo aang’ono ochitirapo misonkhano. Tikukumbukira bwinobwino hatchi ina imene inkachita nafe chidwi kwambiri. Nthaŵi zambiri inkasuzumira pa zenera kuti ione zimene zinkachitika pa misonkhanoyo.

Patapita nthaŵi, mpingo wa Carlyle unakhazikitsidwa, ndipo tinasangalala kuti tinathandiza nawo kuti mpingowu upangike. Tinkathandizidwa ndi banja lina lachinyamata, Steve ndi Karil Thompson, apainiya amene nawonso anabwera kudzatumikira m’gawo losagaŵiridwa. Banjali linakhala m’derali kwa zaka zingapo ndipo kenako anakaphunzira ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo ndipo anapita kukachita umishonale ku East Africa, kumene akutumikira m’ntchito yoyendayenda.

Posakhalitsa, malo aang’ono amene tinali kusonkhanirawo anayamba kudzaza kwambiri, ndipo tinkafunikira nyumba yaikulu. Mbale ndi mkazi wake omwe anatithandiza poyamba aja anatithandizanso ndipo tinagula malo amene anali oyenerera kumangapo Nyumba ya Ufumu. Patapita zaka zingapo tinasangalala kwambiri pamene anatiitana pa mwambo wopatulira Nyumba ya Ufumu imene inangomangidwa kumene ku Carlyle. Ndinapatsidwa mwayi wokamba nkhani yopatulira nyumbayo. Kutumikira kudera limeneli chinali chinthu chabwino kwambiri kwa ife, dalitso lochokera kwa Yehova.

Tinatumizidwa ku Gawo Latsopano

Mu 1979 tinatumizidwa ku gawo lina, ku tauni ya Harrison, ku New Jersey. Tinatumikira kumeneko  kwa zaka pafupifupi 12. M’kati mwa nthaŵi imeneyo tinayamba kuphunzira Baibulo ndi mkazi wina wachitchaina, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tiyambe kuphunzira ndi Matchaina ambiri. Pamene tinali kutero, tinadzazindikira kuti m’dera lathulo munali ana asukulu ndi mabanja achitchaina ambirimbiri. Zimenezi zinatilimbikitsa kuphunzira chinenero cha Chitchaina. Ngakhale kuti zimenezi zinafuna kuti tipatule nthaŵi tsiku lililonse yophunzira chinenerochi, zinachititsa kuti tikhale ndi maphunziro a Baibulo ambiri osangalatsa ndi Matchaina ambiri a m’dera lathulo.

M’zaka zimenezo, tinakumana ndi zochitika zoseketsa zambiri, makamaka poyesera kulankhula Chitchaina. Tsiku lina Ann anauza mwininyumba kuti iye anali “mbeŵa” ya Baibulo m’malo monena kuti “mphunzitsi” wa Baibulo. Mawu aŵiriŵa ndi ofanana kwambiri m’Chitchaina. Mwininyumbayo anamwetulira n’kunena kuti: “Loŵani. Sindinalankhulanepo ndi mbeŵa ya Baibulo chibadwire.” Tikuvutikabe kulankhula chinenerochi.

Ndiyeno anatitumiza kudera lina ku New Jersey kumene tinapitirizabe kugwira ntchito m’gawo la anthu olankhula Chitchaina. Kenako anatipempha kuti tisamukire ku Boston, Massachusetts, kumene gulu la Chitchaina linali likupangika kwa zaka pafupifupi zitatu. Takhala ndi mwayi wothandizira gulu limeneli kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazi ndipo tinasangalala kuona gululi likukhala mpingo pa January 1, 2003.

Kudalitsidwa Chifukwa Chodzimana

Pa Malaki 3:10 timaŵerengapo za pempho la Yehova kwa anthu ake loti abweretse zopereka zawo ndi nsembe zawo kuti iye awatsanulire madalitso oti adzasoŵa malo akuwalandirira. Tinasiya bizinesi imene ndinali kuikonda kwambiri. Tinagulitsa nyumba yathu, imene tinali kuikonda kwambiri. Ndiponso tinadzimana zinthu zina. Komabe, tikayerekezera ndi madalitso amene tapeza, kudzimana kumene tinachitako n’kochepa.

Inde, Yehova watidalitsadi kwambiri. Tasangalala kuona ana anthu akutsatira choonadi, tasangalala kuchita utumiki wa nthaŵi zonse wopulumutsa miyoyo, ndipo taona Yehova akutisamalira pa zimene timafunikira pa moyo wathu. Inde, tadalitsidwa chifukwa chodzimana zinthu zochepa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Ana awoŵa akupitirizabe kutumikira pa Beteli, Edward ndi mkazi wake, Connie, akutumikira ku Patterson ndipo George ndi mkazi wake, Grace, akutumikira ku Brooklyn.

[Chithunzi patsamba 25]

Louise ndi George Blanton ali ndi Ann, mu 1991

[Chithunzi patsamba 26]

Nyumba ya Ufumu ku Carlyle, yomwe inapatuliridwa pa June 4, 1983

[Chithunzi patsamba 27]

Tili ndi mpingo umene wangoyambika kumene wa Chitchaina wa Boston

[Chithunzi patsamba 28]

Tili ndi Edward, Connie, George, ndi Grace