Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

 Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

“Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka.”​—2 TIMOTEO 2:15.

1. Kodi ndi kusintha kwa zinthu kotani kumene kumabweretsa mavuto pa moyo wathu wauzimu?

DZIKO limene tikukhalali likupitirizabe kusintha. Tikuona kupita patsogolo kochititsa chidwi kwa sayansi ndi luso la zaumisiri zimene zikuyendera limodzi ndi kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino. Monga mmene taonera m’nkhani yapitayi, Akristu ayenera kukaniza mzimu wotsutsana ndi Mulungu wa dzikoli. Komabe, pamene dzikoli likusintha, ifenso zinthu zimasintha pa moyo wathu m’njira zambiri. Timakula kuchoka paubwana kufika pauchikulire. Tingapeze chuma kapena chuma chathu chingathe, tingakhale ndi thanzi labwino kapena tingadwale, tingakhale ndi anthu amene timawakonda kwambiri kapena anthuwo angamwalire. Zambiri mwa zinthu zimene zimasinthazi n’zoti ife sitingachitepo kanthu kuti zisatero, ndipo kusinthako kungabweretse mavuto atsopano ndiponso odetsa nkhaŵa pa moyo wathu wauzimu.

2. Kodi zinthu zinasinthasintha motani pa moyo wa Davide?

2 Ndi anthu ochepa amene zinthu zimasintha kwambiri pa moyo wawo mofanana ndi mmene zinachitikira ndi Davide, mwana wa Jese. Davide anasintha  mofulumira kuchoka pa mbusa wamba wachinyamata n’kukhala munthu wotchuka, ngwazi ya dziko lawo. Kenako zinasintha n’kukhala munthu wothaŵathaŵa, pamene mfumu yansanje inali kumusaka ngati nyama. Zitatha zimenezi, Davide anadzakhala mfumu ndiponso anagonjetsa madera ambiri. Analimbana ndi zotsatirapo zopweteka kwambiri za tchimo lalikulu. Anakumana ndi mavuto komanso banja lake linagaŵikana. Anapeza chuma chambiri, anakalamba, ndipo anaona mavuto a ukalamba. Komabe, ngakhale kuti zinthu zambiri zinasintha motero pa moyo wake, Davide anadalira ndi kukhulupirira Yehova ndi mzimu Wake kwa moyo wake wonse. Anachita changu kudzionetsera “kwa Mulungu wovomerezeka,” ndipo Mulungu anamudalitsa. (2 Timoteo 2:15) Ngakhale kuti mmene zinthu zilili pa moyo wathu n’zosiyana ndi mmene zinalili kwa Davide, tingaphunzirepo kanthu pa mmene anachitira zinthu pa moyo wake. Chitsanzo chake chingatithandize kumvetsa mmene tingachitire kuti mzimu wa Mulungu upitirizebe kutithandiza zinthu zikasintha pa moyo wathu.

Kudzichepetsa kwa Davide Ndi Chitsanzo Chabwino

3, 4. Kodi Davide anasintha bwanji kuchoka pa mbusa wamba wachinyamata n’kukhala munthu wotchuka kwambiri m’dzikolo?

3 Davide ali mnyamata sanali wotchuka ngakhale m’banja lawo limene. Mneneri Samueli atapita ku Betelehemu, bambo a Davide anamuonetsa ana seveni mwa ana aamuna eyiti amene anali nawo. Davide, yemwe anali wamng’ono mwa onsewo, anamusiya akuyang’anira nkhosa. Komabe, Yehova anasankha Davide kuti akhale mfumu yam’tsogolo ya Israyeli. Davide anaitanidwa kuthengo kumene anali. Kenako, nkhani ya m’Baibuloyo imati: “Samueli anatenga nyanga ya mafuta, nam’dzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli.” (1 Samueli 16:12, 13) Davide anadalira mzimu umenewu pamoyo wake wonse.

4 Posakhalitsa mbusa wachinyamata ameneyu anatchuka m’dziko lonselo. Anamuitana kuti azikatumikira mfumu ndi kumaiimbira nyimbo. Anapha Goliati yemwe anali katswiri wa nkhondo, chimphona, komanso woopsa moti ngakhale asilikali odziŵa bwino nkhondo a Israyeli anaopa kulimbana naye. Atamusankha kuti atsogolere asilikaliwo, Davide anagonjetsa Afilisti. Anthu anamukonda kwambiri ndipo anapeka nyimbo zomutamanda. Izi zisanachitike, mlangizi wina wa Mfumu Sauli anafotokoza za Davide kuti anali ‘wanthetemya wodziŵa kuimba’ zeze komanso kuti “wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola.”​—1 Samueli 16:18; 17:23, 24, 45-51; 18:5-7.

5. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanam’chititsa Davide kudzikuza, ndipo tikudziŵa bwanji kuti sanadzikuze?

5 Davide anaoneka kuti anali wachikwanekwane, wotchuka, wokongola, wachinyamata, waluso polankhula, wanthetemya poimba, katswiri pankhondo, ndiponso Mulungu anamuyanja. Chilichonse mwa zinthu zimenezi chikanamuchititsa kudzikuza, koma ayi ndithu, sanadzikuze. Taonani mmene Davide anayankhira Mfumu Sauli, imene inapatsa Davide mwana wake wamkazi kuti amukwatire. Posonyeza kudzichepetsa kwenikweni, Davide anati: “Ine ndine yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani m’Israyeli, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?” (1 Samueli 18:18) Pofotokoza za vesi limeneli, katswiri wina analemba kuti: “Davide ankatanthauza kuti iyeyo payekha, kapena mmene banja lake linalili, ngakhalenso mzere wake wobadwira, sizinali zoti n’kumuyenereza kukhala ndi mwayi waukulu wokhala mkamwini wa mfumu.”

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kukulitsa kudzichepetsa?

6 Davide anatha kudzichepetsa chifukwa chakuti ankazindikira kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri ndipo amaposa anthu opanda ungwiro pa chilichonse. Davide anachita chidwi  kwambiri kuti Mulungu amadziŵa anthu. (Salmo 144:3) Davide ankadziŵanso kuti ulemu ulionse umene angakhale ataupeza, anakhala nawo chifukwa chakuti Yehova anadzichepetsa kuti amuthandize, kumuteteza, ndi kumusamalira. (Salmo 18:35) Ndi phunziro labwinotu kwambiri limeneli kwa ife. Luso lathu, zimene takwanitsa kuchita, ndiponso mwayi wa utumiki uliwonse umene tingakhale nawo usatichititse kudzikuza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” (1 Akorinto 4:7) Kuti tikhale ndi mzimu woyera wa Mulungu ndiponso kuti iye atiyanje, tiyenera kukulitsa ndi kukhalabe odzichepetsa.​—Yakobo 4:6.

“Musabwezere Choipa”

7. Kodi ndi mpata wotani umene Davide anapeza woti akanatha kupha Mfumu Sauli?

7 Ngakhale kuti kutchuka kwa Davide sikunam’chititse kudzitukumula, kunachititsa Mfumu Sauli, yomwe mzimu wa Mulungu unam’chokera, kuyamba kuchitira nsanje Davide mpaka kufuna kumupha. Ngakhale kuti Davide sanalakwe, anathaŵa kuti apulumutse moyo wake ndipo anali kukhala m’chipululu. Ulendo wina, Mfumu Sauli ikufunafuna Davide mosalekeza, inaloŵa m’phanga, osadziŵa kuti Davide ndi anzake anabisala momwemo. Anyamata a Davide anamulimbikitsa Davideyo kuti agwiritse ntchito mpata umenewo umene unaoneka ngati wapereka ndi Mulungu kuti aphe Sauli. Tingawaone m’maganizo pamene akumunong’oneza Davide mumdima kuti: “Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m’dzanja lako, kuti ukam’chitira iye chokukomera.”​—1 Samueli 24:2-6.

8. N’chifukwa chiyani Davide anadziletsa kubwezera choipa?

8 Davide anakana kupha Sauli. Posonyeza chikhulupiriro ndi kuleza mtima, anaganiza zongosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Mfumuyo itachoka m’phangamo, Davide anaifuulira ndi kunena kuti: “Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.” (1 Samueli 24:12) Ngakhale ankadziŵa kuti Sauli anali kulakwitsa, Davide sanabwezere yekha, ndiponso sanalankhule kwa Sauli monyoza kapena kumunyoza pamaso pa anthu ena. Pa maulendo ena angapo, Davide anadziletsa kubwezera yekha choipa. M’malo mwake, anadalira Yehova kuti adzakonza zinthu.​—1 Samueli 25:32-34; 26:10, 11.

9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kubwezera ngati anthu ena akutitsutsa kapena kutizunza?

9 Mofanana ndi Davide, mwina mungakumane ndi mavuto enaake. Mwina ana a sukulu anzanu, antchito anzanu, achibale anu, kapena anthu ena alionse amene chikhulupiriro chawo n’chosiyana ndi chanu, akukutsutsani kapena kukuzunzani. Musabwezere. Dikirani Yehova, m’pempheni kuti akupatseni mzimu wake woyera kuti ukuthandizeni.  Mwina anthu osakhulupirirawo adzachita chidwi ndi khalidwe lanu labwino ndipo adzakhala okhulupirira. (1 Petro 3:1) Mulimonse mmene zingakhalire, khulupirirani kuti Yehova akuona mmene zinthu zilili kwa inu ndipo adzachitapo kanthu panthaŵi imene iye adzaona kuti n’koyenera kuti atero. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.”​—Aroma 12:19.

‘Mverani Mwambo’

10. Kodi zinakhala bwanji kuti Davide achite tchimo, ndipo anayesetsa motani kuliphimba?

10 Patapita zaka, Davide anakhala mfumu yotchuka kwambiri imene anthu anali kuikonda. Kukhulupirika kumene anasonyeza pamoyo wake, pamodzinso ndi masalmo abwino kwambiri amene analemba potamanda Yehova, zikhoza kuchititsa munthu kuganiza kuti Davide anali munthu woti sakanachita tchimo lalikulu. Koma anachitadi tchimo. Tsiku lina mfumuyi ili padenga la nyumba yake inaona mkazi wokongola akusamba. Inafufuza za mkaziyo. Davide atamva kuti mkaziyo anali Bateseba ndipo mwamuna wake, Uriya, anali kunkhondo, anamuitanitsa ndipo anagona naye. Kenako, anamva kuti ali ndi mimba. Nkhaniyi ikanakhala yoopsa kwambiri ngati anthu akanaidziŵa. M’Chilamulo cha Mose, kuchita chigololo unali mlandu womwe chilango chake chinali imfa. Mfumuyo iyenera kuti inaganiza kuti zinali zotheka kuphimba tchimolo. Motero, inatumiza uthenga kwa asilikali, n’kulamula kuti Uriya abwerere ku Yerusalemu. Davide ankayembekezera kuti Uriya adzagona limodzi ndi Bateseba usiku umenewo koma zimenezo sizinachitike. Atagwira njakata, Davide anam’tumiza Uriya kubwerera ku nkhondo atam’patsira kalata yoti akapatse Yoabu, m’tsogoleri wa asilikali. M’kalatamo analemba kuti Uriya amuike kutsogolo kwa nkhondo imene inali itavuta kwambiri zimene zikanachititsa kuti aphedwe. Yoabu anamvera ndipo Uriya anaphedwa. Bateseba atamaliza mwambo wolira mwamuna wake, Davide anamutenga n’kukhala mkazi wake.​—2 Samueli 11:1-27.

11. Kodi Natani anafotokoza nkhani yotani kwa Davide, ndipo Davideyo anatani atamva nkhaniyo?

11 Zimene anachitazo zinaoneka ngati zayenda bwino, ngakhale kuti Davide anayenera kudziŵa kuti zonse zimene zinachitikazo Yehova anali kuziona. (Ahebri 4:13) Panapita miyezi, ndipo mwana anabadwa. Ndiyeno mneneri Natani anapita kwa Davide atauzidwa ndi Mulungu. Mneneriyo anaiuza mfumuyo nkhani yakuti munthu wachuma yemwe anali ndi nkhosa zambiri anatenga n’kupha nkhosa ya munthu wosauka yemwe anali nayo imodzi yokhayo ndipo ankaikonda kwambiri. Nkhaniyo inamukhudza kwambiri Davide ndipo anaona kuti chilungamo chiyenera kutsatidwa pa nkhaniyi koma sanadziŵe kuti inali ndi tanthauzo lobisika. Davide anagamula mwamsanga motsutsa munthu wolemerayo. Atakwiya kwambiri, anauza Natani kuti: “Munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha.”​—2 Samueli 12:1-6.

12. Kodi Yehova anamuweruza bwanji Davide?

12 Mneneriyo anayankha kuti: “Munthuyo ndi inu nomwe.” Davide anadziweruza yekha. Mosakayikira, kukwiya kwa Davide kuja kunasintha n’kukhala manyazi aakulu ndiponso chisoni chachikulu. Iye anamvetsera kukamwa kuli pululu pamene Natani anali kupereka chiweruzo cha Yehova chosathaŵika. Panalibe mawu otonthoza. Davide ananyoza mawu a Yehova pochita zinthu zoipa. Kodi sanaphe Uriya ndi lupanga la adani?  Lupanga silidzachoka panyumba ya Davide. Kodi sanatenge mkazi wa Uriya mwachinsinsi? Zinthu zoipa zofanana ndi zimenezi zinali kudzamuchitikira, osati mwachinsinsi koma moonekera kwa anthu onse.​—2 Samueli 12:7-12.

13. Kodi Davide anachita chiyani ndi chilango cha Yehova?

13 Ubwino wake, Davide sanakane kuti anali wolakwa. Sanamupsere mtima mneneri Natani. Sanaimbe mlandu anthu ena chifukwa cha zimene anachita kapena kupereka zifukwa zoti sakanachitira mwina. Atauzidwa machimo akewo, Davide anavomereza kuti walakwadi, ponena kuti: “Ndinachimwira Yehova.” (2 Samueli 12:13) Salmo 51 likusonyeza mmene anavutikira maganizo chifukwa cha tchimo lake ndiponso mmene anasonyezera kulapa kwake. Iye anapempha Yehova kuti: “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere mzimu wanu woyera.” Anali kukhulupirira kuti Yehova, mwa chifundo chake, sadzapeputsa “mtima wosweka ndi wolapa [“woswanyika, NW]” chifukwa cha tchimo. (Salmo 51:11, 17) Davide anapitiriza kudalira mzimu wa Mulungu. Ngakhale kuti Yehova sanatetezere Davide ku zotsatirapo zopweteka za tchimo lake, anamukhululukira.

14. Kodi tiyenera kuchita motani Yehova akamatilanga?

14 Tonsefe ndife opanda ungwiro, ndipo timachimwa. (Aroma 3:23) Nthaŵi zina tingachite tchimo lalikulu monga mmene anachitira Davide. Monga mmene tate wachikondi amalangira ana ake, Yehova amawongolera anthu amene amafuna kum’tumikira. Ngakhale kuti chilango n’chopindulitsa, n’chovuta kuchilandira. Ndipotu nthaŵi zina chimakhala “chowawa.” (Ahebri 12:6, 11) Komabe, ngati ‘timvera mwambo,’ kapena kuti kumvera malangizo, tingayanjanenso ndi Yehova. (Miyambo 8:33) Kuti tipitirizebe kukhala ndi mzimu wa Yehova, tiyenera kumvera pamene tikuwongoleredwa ndi kuchita zinthu zoti Mulungu atiyanje.

Musadalire Chuma Chimene Sichidziŵika Ngati Chidzakhalitsa

15. (a) Kodi anthu ena amagwiritsa ntchito chuma chawo motani? (b) Kodi Davide anafuna kugwiritsa ntchito chuma chake motani?

15 Palibe chilichonse chimene chikusonyeza kuti Davide anachokera ku banja lotchuka kapena kuti banja lake linali lolemera. Komabe, atakhala mfumu, Davide anapeza chuma chambiri. Monga mukudziŵira, anthu ambiri amadziunjikira chuma, amafuna kuchiwonjezera mwaumbombo, kapena amachigwiritsa ntchito mwadyera. Ena amagwiritsa ntchito chuma chawo mofuna kuti anthu awatame. (Mateyu 6:2) Davide anagwiritsa ntchito chuma chake mosiyana. Anafunitsitsa kulemekeza Yehova. Davide anauza Natani kuti akufuna kumangira Yehova kachisi kuti muzikhala likasa la chipangano, limene panthaŵiyo linali ku Yerusalemu “m’kati mwa nsalu zotchinga.” Yehova anasangalala ndi zimene Davide anafuna kuchita koma anamuuza kudzera mwa Natani kuti mwana wake, Solomo, ndi amene adzamange kachisiyo.​—2 Samueli 7:1, 2, 12, 13.

16. Kodi Davide anakonzeratu chiyani zothandiza pa ntchito yomanga kachisi?

16 Davide anasonkhanitsa zipangizo zoti zidzagwiritsidwe ntchito pa ntchito yaikulu yomanga imeneyi. Davide anauza Solomo kuti: “Ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake,  pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuwonjezereko.” Davide anatenga pa chuma chake matalente 3,000 a golidi ndi matalente 7,000 a siliva n’kupereka. * (1 Mbiri 22:14; 29:3, 4) Kupereka kwa Davide mooloŵa manja sikunali kudzionetsera koma kusonyeza chikhulupiriro ndi kudzipereka kwa Yehova Mulungu. Pozindikira Gwero la chuma chake, iye anauza Yehova kuti: “Zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Mtima wopatsa wa Davide unamulimbikitsa kuchita zonse zimene akanatha pofuna kupititsa patsogolo kulambira koyera.

17. Kodi malangizo amene ali pa 1 Timoteo 6:17-19 akugwira ntchito bwanji kwa anthu osauka ndi olemera omwe?

17 Mofanana ndi Davide, tiyeni tigwiritse ntchito chuma chathu pochita zabwino. M’malo mokhala ndi moyo wokondetsa chuma, ndi bwino kuchita zinthu zoti Mulungu atiyanje, ndipo zimenezi n’zomwe zingatithandize kuti tikhale ndi nzeru ndi chimwemwe chenicheni. Paulo analemba kuti: “Iwo amene ali olemera pazinthu za pansi pano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma adalire Mulungu amene amatipatsa zonse mooloŵa manja kuti tikondwere nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pantchito zokoma, ooloŵa manja, ndiponso okonda kugaŵana zinthu zawo ndi anthu ena. Pakutero adzadziunjikira chuma chimene chidzakhala ngati maziko olimba a nthaŵi yakutsogolo, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.” (1 Timoteo 6:17-19, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Kaya ndife osauka kapena olemera, tiyeni tidalire mzimu wa Mulungu ndi kuchita zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi “chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:21) Palibe chinthu chofunika kwambiri kuposa kuyanjidwa ndi Atate wathu wachikondi wakumwamba.

Dzionetsereni Wovomerezeka kwa Mulungu

18. Kodi Davide anapereka motani chitsanzo chabwino kwa Akristu?

18 Davide pa moyo wake wonse, anachita zinthu zoti Yehova amuyanje. Iye anafuula m’nyimbo kuti: “Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu.” (Salmo 57:1) Kukhulupirira kwake Yehova sikunapite pachabe. Davide anakula, “ndi kuchuluka masiku.” (1 Mbiri 23:1) Ngakhale kuti Davide anachita machimo aakulu, amakumbukiridwa monga m’modzi mwa mboni za Mulungu zimene zinasonyeza chikhulupiriro cholimba.​—Ahebri 11:32.

19. Kodi tingatani kuti tidzionetsere ovomerezeka kwa Mulungu?

19 Pamene zinthu zikusintha pa moyo wanu, kumbukirani kuti monga mmene Yehova anathandizira, kulimbitsa, ndi kuwongolera Davide, adzachitanso chimodzimodzi kwa inu. Moyo wa mtumwi Paulo unasinthanso pa zinthu zambiri monga mmene zinalili ndi Davide. Koma nayenso anakhalabe wokhulupirika mwa kudalira mzimu wa Mulungu. Iye analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:12, 13) Ngati tidalira Yehova, adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Iye amafuna kuti zinthu zitiyendere bwino. Ngati timumvetsera ndi kumuyandikira, adzatipatsa mphamvu zoti tichite chifuniro chake. Ndipo ngati tipitiriza kudalira mzimu wa Mulungu, tidzatha ‘kudzionetsera kwa Mulungu ovomerezeka’ pakalipano komanso mpaka kalekale.​—2 Timoteo 2:15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Masiku ano, mtengo wa zinthu zimene Davide anapereka ndi wokwana madola 1,200,000,000 a ku United States.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingapeŵe bwanji kudzikuza?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kubwezera choipa?

• Kodi chilango tiyenera kuchiona motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Mulungu osati chuma?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Davide anadalira mzimu wa Mulungu ndipo anachita zinthu zoti Mulungu amuyanje. Kodi inu mukuchitanso chimodzimodzi?

[Chithunzi patsamba 18]

“Zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu”