NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) January 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa February 26 mpaka April 1, 2018.

ANADZIPEREKA NDI MTIMA WONSE

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Madagascar

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe za anthu amene adzipereka kuti akathandize kufalitsa uthenga wa Ufumu kumadera osiyanasiyana a m’dziko lalikulu la Madagascar.

“Iye Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”

Mapeto akamayandikira tingayembekezere kuti mavuto azichulukirachulukira. Lemba la chaka cha 2018 limatikumbutsa kuti tizidalira Yehova kuti azitipatsa mphamvu.

Chikumbutso Chimatithandiza Kukhala Ogwirizana

Kodi Chikumbutso chimathandiza bwanji kuti anthu a Mulungu azigwirizana? Kodi tidzapanga liti Chikumbutso chomaliza?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupereka kwa Amene Ali ndi Chilichonse?

Njira imodzi imene timasonyezera kuti timakonda Mulungu ndi kumupatsa zinthu zathu. Kodi kupereka zinthu zathu zamtengo wapatali kwa Yehova kumatithandiza bwanji?

Kodi Tiyenera Kukonda Ndani Kuti Tikhale Osangalala?

Kodi kukonda Mulungu kumasiyana bwanji ndi chikondi chofotokozedwa pa 2 Timoteyo 3:​2-4? Yankho la funso limeneli lingatithandize kukhala osangalala.

Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli

Kodi makhalidwe amene anthu ali nawo m’masiku otsirizawa akusiyana bwanji ndi amene anthu a Mulungu ali nawo?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Aisiraeli ankatsatiradi mfundo za Chilamulo cha Mose pothetsa nkhani zawo za tsiku ndi tsiku?