Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli

Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli

“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa.”—MAL. 3:18.

NYIMBO: 127, 101

1, 2. Kodi anthu a Mulungu ayenera kukhala osamala pa nkhani iti masiku ano? (Onani zithunzi zoyambirira.)

ANTHU ambiri ogwira ntchito kuchipatala amasamalira anthu amene akudwala matenda opatsirana. Iwo amasamalira anthuwo chifukwa chofuna kuwathandiza. Koma pochita zimenezi, amayenera kudziteteza kuti asatengere matenda amene anthuwo akudwala. Chimodzimodzinso ndi ifeyo. Timakhala komanso kugwira ntchito ndi anthu amene ali ndi maganizo ndiponso makhalidwe oipa. Choncho tiyenera kukhala osamala kwambiri.

2 M’masiku otsiriza ano makhalidwe a anthu aipa kwambiri. M’kalata yake yachiwiri yopita kwa Timoteyo, Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu omwe satumikira Mulungu adzakhale nawo m’masiku otsiriza, ndipo anati makhalidwewa adzaipa kwambiri. (Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, 13.) Mwina Akhristufe timakhumudwa ndi makhalidwe oipa amene anthu ambiri ali nawo. Komabe tikhoza kutengera mosavuta maganizo ndiponso zochita za anthu omwe ali ndi makhalidwewo. (Miy. 13:20) Munkhaniyi tikambirana makhalidwe amene anthu a m’dzikoli amasonyeza komanso makhalidwe abwino amene anthu a Mulungu amakhala nawo. Tionanso zimene tingachite kuti tisamatengere makhalidwe oipawo komanso kuti tizithandiza anthu ena kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

3. Kodi ndi ndani amasonyeza makhalidwe otchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5?

 3 Mtumwi Paulo analemba kuti ‘masiku otsiriza adzakhala nthawi yovuta’ ndipo anatchula makhalidwe oipa okwana 19 amene anthu adzakhala nawo pa nthawiyo. Makhalidwe amene anatchulawo ndi ofanana ndi amene anatchulidwa pa Aroma 1:29-31. Koma pa 2 Timoteyo 3:2-5 Paulo anagwiritsa ntchito mawu amene sanatchulidwenso pena paliponse m’Malemba Achigiriki. Iye asanatchule makhalidwe oipawa, anayamba ndi mawu akuti “anthu adzakhala . . . “ Ponena kuti “anthu,” Paulo ankasonyeza kuti anthu ambiri, kaya amuna kapena akazi, adzasonyeza makhalidwe oipa. Koma sikuti munthu aliyense amakhala ndi makhalidwe oipawa. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino.​—Werengani Malaki 3:18.

TIZIDZIONA MOYENERA

4. Kodi mungafotokoze bwanji anthu odzitukumula ndiponso onyada?

4 Paulo atanena kuti anthu ambiri adzakhala odzikonda komanso okonda ndalama, analembanso kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Munthu amasonyeza makhalidwe amenewa chifukwa choganiza kuti ndi wapamwamba kuposa ena potengera luso lake, maonekedwe ake, chuma chake kapena udindo wake. Anthu amakhalidwe amenewa amalakalaka kuti ena aziwatama kapena kuwasirira. Katswiri wina analemba kuti munthu wonyada kwambiri amadziona kuti ndi wapadera moti tingati amadzilambira yekha. Anthu ena amanena kuti khalidwe lonyada ndi lonyansa kwambiri moti ngakhale anthu onyadawo amanyansidwa ndi anthu ena amene ali ndi khalidweli.

5. Kodi atumiki ena okhulupirika a Mulungu anasonyeza bwanji khalidwe lonyada?

5 Yehova amadana ndi khalidwe la kunyada. Paja Baibulo limanena kuti iye amanyansidwa ndi “maso odzikweza.” (Miy. 6:16, 17) Munthu wonyada sangakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Sal. 10:4) Mdyerekezi ndi wonyada. (1 Tim. 3:6) Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale atumiki ena a Yehova anayamba kusonyeza khalidweli. Mwachitsanzo Uziya, yemwe anali mfumu ya ku Yuda, anakhala wokhulupirika kwa zaka zambiri, koma Baibulo limanena kuti: “Atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.” Pa nthawi ina, nayenso Mfumu Hezekiya anayamba mtima wonyada koma kenako anasiya.​—2 Mbiri 26:16; 32:25, 26.

6. Kodi n’chiyani chikanachititsa kuti Davide akhale wonyada, koma n’chiyani chinamuthandiza kuti akhale wodzichepetsa?

6 Anthu ena amayamba kunyada chifukwa cha zinthu monga kuoneka bwino, kutchuka, luso loimba kapena udindo wapamwamba. Davide anali ndi zinthu zonsezi koma anakhala wodzichepetsa kwa moyo wake wonse. Iye atapha Goliyati, Mfumu Sauli anamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire. Koma Davide ananena kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?” (1 Sam. 18:18) N’chiyani chinathandiza Davide kuti akhalebe wodzichepetsa? Iye ankadziwa kuti anali ndi makhalidwe abwino, maluso komanso udindo chifukwa choti Mulungu ‘anatsika m’munsi,’ kapena kuti anadzichepetsa, kuti amuthandize. (Sal. 113:5-8) Davide ankadziwanso kuti zinthu zonse zabwino zimene anali nazo anachita kuzilandira kuchokera kwa Yehova.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:7.

7. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale odzichepetsa?

7 Masiku ano, anthu a Yehova amayesetsa kukhala odzichepetsa ngati mmene ankachitira  Davide. Timatsanzira Yehova, yemwe ndi Munthu wamkulu m’chilengedwe chonse, koma amadzichepetsa. (Sal. 18:35) Timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Timadziwanso kuti chikondi ‘sichidzitama ndiponso sichidzikuza.’ (1 Akor. 13:4) Ndipo tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, anthu ena angafune kuyamba kuphunzira za Yehova ngati mmene amuna angakopekere ndi khalidwe labwino la akazi awo.​—1 Pet. 3:1.

TIZIGWIRIZANA NDI ANTHU ENA

8. (a) Kodi masiku ano anthu ena amaona bwanji nkhani yosamvera makolo? (b) Kodi Malemba amalangiza ana kuti azichita chiyani?

8 Paulo anafotokozanso mmene anthu a m’masiku otsiriza azidzachitira zinthu ndi anthu ena. Iye analemba kuti ana adzakhala osamvera makolo. N’zoona kuti anthu ambiri amaona kuti zimenezi si vuto ndipo mabuku, mafilimu ndiponso mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa ana kukhala osamvera. Koma khalidweli ndi limene limasokoneza mabanja ambiri. Anthu akhala akudziwa mfundo imeneyi kuyambira kalekale. Mwachitsanzo, kale ku Greece munthu akamenya makolo ake ankamulanda ufulu wake. Komanso ku Rome, munthu akamenya bambo ake ankalangidwa mofanana ndi amene wapha munthu. Malemba Achiheberi komanso Malemba Achigiriki amalangizanso ana kuti azilemekeza makolo awo.​—Eks. 20:12; Aef. 6:1-3.

9. N’chiyani chingathandize ana kuti azimvera makolo awo?

9 Ana angapewe kutengera khalidwe la kusamvera akamaganizira zinthu zabwino zimene makolo awo awachitira. Angachitenso bwino kukumbukira kuti Mulungu, yemwe ndi Atate wa tonsefe, amatilamula kuti tikhale omvera. Ana akamalankhula zinthu zabwino zokhudza makolo awo, angathandize ana anzawo kuti azilemekezanso makolo awo. Koma ana akaona kuti makolo awo sakuwakonda kwenikweni zingakhale zovuta kuti aziwamvera kuchokera pansi pa mtima. Mosiyana ndi zimenezi, ana akaona kuti makolo awo amawakonda ndi mtima wonse, amafuna kuchita zinthu zowasangalatsa ngakhale zitakhala zovuta kwambiri kwa anawo. Mnyamata wina dzina lake Austin ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkafuna kuchita zosiyana ndi zimene makolo anga ankafuna. Koma iwo ankaika malamulo omveka, ankafotokoza chifukwa chimene akuikira malamulowo komanso ankakambirana nane momasuka. Izi zinandithandiza kuti ndiziwamvera. Ndinkaona kuti amandikonda ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndiziyesetsa kuwasangalatsa.”

10, 11. (a) Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene anthu osakonda anzawo amasonyeza? (b) Kodi Akhristu oona amasonyeza chikondi kwa ndani?

10 Paulo anatchula makhalidwe ena oipa amene anthu amasonyeza chifukwa chosakonda anzawo. Iye atatchula anthu “osamvera makolo” anatchula anthu osayamika, ndipo m’pomveka chifukwa anthu otere sayamikira zinthu zabwino zimene ena awachitira. Ananena kuti anthu adzakhala osakhulupirika komanso osafuna kugwirizana ndi anzawo. Ananenanso kuti anthu adzakhala achiwembu komanso onyoza, omwe amanena zinthu zonyoza anzawo ngakhalenso Mulungu. Anatinso anthu adzakhala onenera anzawo zoipa, kapena kuti anthu amene amafalitsa miseche n’cholinga choti awononge mbiri ya anthu ena. *

11 Mosiyana ndi anthu amene sakonda anzawo masiku ano, anthu amene amalambira Yehova amasonyeza anzawo chikondi ndipo sichikhala champeni kumphasa. Anthu a Yehova akhala akuchita zimenezi kuyambira kalekale. Tikutero chifukwa Yesu atanena kuti lamulo lalikulu  m’Chilamulo cha Mose ndi kukonda Mulungu, ananena kuti lachiwiri lake ndi kukonda anzathu ndipo chikondi chake ndi cha a·gaʹpe. (Mat. 22:38, 39) Iye ananenanso kuti kukondana ndi khalidwe limene Akhristu oona ayenera kudziwika nalo. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Akhristu amasonyezanso chikondi ngakhale kwa adani awo.​—Mat. 5:43, 44.

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda anthu?

12 Yesu ankasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. Iye ankayenda kumzinda ndi mzinda kukauza anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ankachiritsa anthu osaona, olumala, akhate, osamva ndiponso kuukitsa akufa. (Luka 7:22) Yesu anafikanso popereka moyo wake kuti awombole anthu ngakhale kuti ambiri ankadana naye. Yesu ankatsanzira Atate wake ndendende posonyeza chikondi. Padziko lonse, a Mboni za Yehova amasonyezanso chikondi chenicheni kwa anthu anzawo.

13. Kodi chikondi chimene timasonyeza anthu chingawathandize bwanji kuti aphunzire za Yehova?

13 Tikamasonyeza anthu chikondi, ena amafuna kuphunzira za Atate wathu wakumwamba. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mwamuna wina wa ku Thailand. Iye anakhudzidwa kwambiri ndi chikondi chimene abale ankasonyezana kumsonkhano wachigawo. Atabwerera kwawo, anapempha kuti aziphunzira Baibulo kawiri pa mlungu ndipo anayamba kulalikira kwa achibale ake. Patangopita miyezi 6 kuchokera nthawi ya msonkhano, anapatsidwa mbali ya kuwerenga Baibulo pamisonkhano yampingo. Kuti tidziwe ngati tikuchita bwino pa nkhani yosonyeza chikondi, tingadzifunse mafunso awa: ‘Kodi ndimayesetsa kuti ndizithandiza anthu m’banja langa, mumpingo komanso mu utumiki? Nanga kodi ndimayesetsa kuona anthu ena mmene Yehova amawaonera?’

MIMBULU NDIPONSO NKHOSA

14, 15. Kodi anthu ambiri amasonyeza makhalidwe oipa ati, nanga anthu ena asintha bwanji?

14 Palinso makhalidwe ena amene anthu a m’dzikoli amasonyeza omwe Akhristu ayenera kuwapewa. Baibulo linaneneratu kuti anthu amene salambira Mulungu adzakhala osakonda zabwino. Mabaibulo ena anamasulira mawu  akuti “osakonda zabwino” kuti “odana ndi zabwino zonse.” Baibulo linaneneratunso kuti anthu adzakhala osadziletsa ndiponso oopsa. Komanso anthu ena ndi osamva za ena ndipo amachita zinthu mopupuluma popanda kuganizira zotsatirapo zake.

15 Koma anthu ambiri amene poyamba anali ndi makhalidwe oipawa anasintha n’kukhala anthu abwino. M’Baibulo muli ulosi wofotokoza za kusintha kumeneku. (Werengani Yesaya 11:6, 7.) Ulosiwu umanena kuti nyama zakutchire monga mimbulu ndi mikango zizidzakhala mwamtendere ndi nyama zimene anthu amaweta monga nkhosa ndi ng’ombe. Umanenanso kuti nyamazi zidzakhala mwamtendere chifukwa “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yes. 11:9) Popeza nyama sizingaphunzire za Yehova, ndiye kuti ulosiwu ukunenanso za kusintha kwa anthu.

Anthu akamatsatira mfundo za m’Baibulo amasintha kwambiri (Onani ndime 16)

16. Kodi Baibulo lathandiza bwanji anthu kuti asinthe makhalidwe awo?

16 Pali anthu ambiri omwe anali oopsa ngati mimbulu koma tsopano amakhala mwamtendere ndi ena. Mungawerenge za ena mwa anthuwa munkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” zomwe zimapezeka pa jw.org. Anthu amene amadziwa Yehova komanso kumutumikira amasiyana ndi anthu ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe. Anthu ongooneka ngati odzipereka kwa Mulungu amachita zinthu ngati amalambira Mulungu koma khalidwe lawo limakhala losiyana ndi zimene iye amafuna. Koma anthu ena amene poyamba anali oopsa anavala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:23, 24) Anthu akamaphunzira zokhudza Mulungu, amayesetsa kuti moyo wawo ugwirizane ndi zimene Mulungu amafuna. Choncho amasintha zimene amakhulupirira, zimene amaganiza komanso khalidwe lawo. Zinthu zimenezi n’zovuta kusintha koma zimatheka chifukwa mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene akufunitsitsa kuchita zimene Mulunguyo amafuna.

“ANTHU AMENEWA UWAPEWE”

17. Kodi tingapewe bwanji kutengera makhalidwe a anthu oipa?

17 Masiku ano anthu amene amatumikira Mulungu amasiyana kwambiri ndi amene samutumikira. Atumiki a Yehovafe timafunika kusamala kwambiri kuti tisatengere maganizo a anthu osalungama. Tiziyesetsa kumvera malangizo akuti tizipewa anthu amene atchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5. N’zoona kuti sitingapeweretu anthu amakhalidwe oipa chifukwa timakhala moyandikana nawo, timagwira nawo ntchito kapena timapita nawo kusukulu. Koma n’zotheka kupewa kutengera maganizo komanso makhalidwe awo oipa. Zimenezi zingatheke tikamapitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova pophunzira Baibulo komanso kugwirizana kwambiri ndi anthu amene amamutumikira ndi mtima wonse.

18. Kodi zolankhula ndi zochita zathu zingathandize bwanji anthu ena?

18 Tiyenera kuyesetsa kuthandiza anthu ena kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Tiziyesetsa kupeza mpata wolalikira ndipo tizipempha Mulungu kuti atithandize kulankhula zinthu zoyenera pa nthawi yoyenera. Tiyenera kuuza anthu kuti ndife a Mboni za Yehova. Ndiye anthuwo akamaona makhalidwe athu abwino, adzalemekeza Mulungu osati ifeyo. Taphunzitsidwa “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:11-14) Tikamakhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu, anthu adzaona ndipo ena akhoza kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zek. 8:23.

^ ndime 10 Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “wonenera anzawo zoipa” ndi di·aʹbo·los, ndipo m’Baibulo mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za Satana, yemwe amanenera Mulungu zoipa.