Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Aisiraeli ankatsatiradi mfundo za Chilamulo cha Mose pothetsa nkhani zawo za tsiku ndi tsiku?

INDE, nthawi zina. Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi pa nkhaniyi. Lemba la Deuteronomo 24:14, 15 limanena kuti: “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu, amene ali m’mizinda yanu. . . . Angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira, iwe n’kupezeka kuti wachimwa.”

Phale limene analembapo dandaulo la waganyu

Cha m’ma 600 B.C.E. paphale linalake panalembedwa nkhani yokhudza mfundo yapalembali. Phaleli linapezeka pafupi ndi ku Asidodi ndipo zikuoneka kuti analemba zimene waganyu winawake amene akuti analephera kukolola mbewu zokwanira ananena. Analembapo kuti: “Mtumiki wanu [wopempha thandizo] anamaliza kuika zokolola munkhokwe masiku apitawo ndipo Hoshayahu mwana wa Shobay anabwera n’kudzalanda chovala cha mtumiki wanu. . . . Anzanga amene ndinkagwira nawo ntchito masana onse akhoza kuvomereza . . . kuti zimene ndikunenazi ndi zoona. Ine sindinalakwe chilichonse. . . . Mwina mungaone kuti si udindo wanu kumuuza kuti andibwezere chovalachi, koma chonde ndithandizeni mwa chifundo chanu. Musangokhala chete chifukwa chovala changa chapita.”

Katswiri wina wa mbiri yakale dzina lake Simon Schama ananena kuti zimene zinalembedwa paphaleli “sikuti zimangosonyeza kuti waganyuyo ankayesetsa kuti apeze chovala chake. Koma zikusonyezanso kuti iye ankadziwa malamulo a m’Baibulo, makamaka a mu Levitiko ndi Deuteronomo, oletsa kuchitira nkhanza anthu osauka.”