Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 3 2018 | Kodi Mulungu Zimam’khudza Mukamavutika?

KODI MULUNGU ZIMAM’KHUDZA MUKAMAVUTIKA?

Pakachitika ngozi komanso anthu akamavutika ndiponso kufa, ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amaona zimene zikuchitikazi?’ Baibulo limanena kuti:

“Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”​—1 Petulo 3:12.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mmene Mulungu amatithandizira komanso zimene akuchita kuti athetse mavuto onse.

 

“Kodi Mulungu Anali Kuti?”

Kodi pa nthawi ina patachitika ngozi munayamba mwakayikirapo ngati mulungu amakukondani inuyo panokha?

Kodi Mulungu Amachita Chidwi ndi Zimene Zimakuchitikirani?

Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu amachita chidwi ndi zimene zimachitika pa moyo wathu?

Kodi Mulungu Amakumvetsani?

Mulungu amadziwa mavuto amene takumana nawo ndiponso zimene zachititsa kuti tikhale ndi khalidwe linalake.

Kodi Mulungu Amadziwa Mmene Mumamvera?

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amachita nafe chidwi, amatimvetsa komanso amadziwa mmene timamvera.

Kodi Mavuto Amene Timakumana Nawo Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

Kodi Mulungu amagwiritsa ntchito matenda kapena mavuto polanga anthu pa zolakwa zimene anachita?

Kodi N’chifukwa Chiyani Timavutika?

Baibulo limatchula zifukwa zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika.

Posachedwapa Mulungu Athetsa Mavuto Onse

Kodi tikudziwa bwanji kuti posachedwapa Mulungu athetsa mavuto onse komanso zinthu zopanda chilungamo?

Kodi Kudziwa Zoti Mulungu Amatiganizira Kungatithandize Bwanji?

Malemba amatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzakwaniritsa zimene watilonjeza.

Kodi Mulungu Amamva Bwanji Akamakuonani Mukuvutika?

Mavesi awa a m’Baibulo angakuthandizeni kudziwa mmene Mulungu amamvera anthu akamavutika.