Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziwa Zoti Mulungu Amatiganizira Kungatithandize Bwanji?

Kodi Kudziwa Zoti Mulungu Amatiganizira Kungatithandize Bwanji?

Mulungu analenga thupi lathu m’njira yoti lizitha kudzichiritsa lokha. Tikavulala thupi limachita zinthu zina zochititsa chidwi kuti mabala, kaya akuluakulu kapena ang’onoang’ono, apole. (Johns Hopkins Medicine) Munthu akangovulala, nthawi yomweyo thupi limayamba kutseka pabalapo kuti magazi asiye kutuluka, limakulitsa mitsempha ya magazi n’kukonza maselo amene awonongeka komanso kulimbitsa pabalapo kuti pagwirane.

TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: Ngati Mulungu analenga thupi lathu kuti lizitha kudzichiritsa lokha, ayeneranso kuti adzakwaniritsa zimene amatilonjeza kuti adzachiritsa mabala a mumtima mwathu obwera chifukwa cha mavuto omwe timakumana nawo. Munthu wina amene analemba nawo Masalimo anati, “Iye amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Salimo 147:3) Ngati panopo muli ndi mabala mumtima chifukwa cha mavuto amene mumakumana nawo pa moyo wanu, kodi mungatsimikize bwanji kuti Mulungu adzamanga mabala anu kuti muchire?

BAIBULO LIMASONYEZA KUTI MULUNGU NDI WACHIKONDI

Mulungu amatilonjeza kuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yesaya 41:10) Munthu amene amadziwa kuti Mulungu amamukonda amakhala ndi mtendere wa m’maganizo ndiponso mphamvu zotha kupirira mavuto amene akukumana nawo. Mtumwi Paulo ananena kuti mtendere wa m’maganizo umenewu ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Iye ananenanso kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afilipi 4:4-7, 9, 13.

Malemba amatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro choti Yehova adzakwaniritsa zimene watilonjeza. Mwachitsanzo, lemba la Chivumbulutso 21:4, 5 limafotokoza zimene adzachite komanso chifukwa chake tiyenera kumukhulupirira:

  • “Iye adzapukuta misozi yonse” ya anthu. Yehova adzachotsa mavuto komanso nkhawa zathu zonse ngakhale zimene anthu ena saziona.

  • “Wokhala pampando wachifumu” waulemerero kumwamba, yemwe ndi Wamphamvuyonse, adzagwiritsa ntchito udindo komanso mphamvu zake kuteteza ndi kuthandiza anthu.

  • Yehova amatitsimikizira kuti malonjezo ake ndi “odalirika ndi oona.” Choncho, zili ngati Yehova akulumbira kuti iyeyo monga Mulungu woona, adzakwaniritsa zonse zimene walonjeza.

“‘Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’ Ndipo wokhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.’”—Chivumbulutso 21:4, 5.

Chilengedwe komanso Baibulo zimatithandiza kudziwa makhalidwe a Atate wathu wakumwamba. Ngakhale kuti chilengedwe sichimachita kutiuza kuti tikhale paubwenzi ndi Yehova, Baibulo limanena zimenezi ndipo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Komanso lemba la Machitidwe 17:27 limati: “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”

Mukamayesetsa kuphunzira za Mulungu, m’pamene mumayamba kukhulupirira kwambiri kuti iye “amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Ndiye kodi timapindula bwanji tikayamba kukhulupirira Yehova?

Taganizirani za Toru wa ku Japan. Iye analeredwa ndi mayi ake omwe anali Mkhristu, koma kenako analowa m’gulu lina la zigawenga lotchedwa Yakuza. Iye anati, “Ndinkaona kuti Mulungu samandikonda. Ndinkaonanso kuti m’bale wanga kapenanso munthu wina yemwe ndimam’konda akamwalira, ndiye kuti Mulungu akundilanga.” Toru anafotokoza kuti maganizo amenewa anachititsa kuti akhale munthu “wouma mtima komanso wopanda chisoni.” Pofotokoza zimene ankafuna kudzachita pa moyo wake iye anati: “Ndinkafunitsitsa kuti ndidzangopha munthu wina wake wodziwika n’cholinga choti nditchuke, kenako ndidzadziphe.”

Komabe atayamba kuphunzira Baibulo pamodzi ndi mkazi wake Hannah, Toru anasintha kwambiri moyo wake komanso mmene ankaonera zinthu. Hannah anati: “Titangoyamba kuphunzira ndinaona kuti mwamuna wanga akusintha khalidwe lake.” Nayenso Toru anati: “Panopo ndatsimikiza kuti Mulungu amaganizira wina aliyense. Samafuna kuti anthu azifa ndipo amatikhululukira machimo athu ngati talapa kuchokera pansi pa mtima. Yehova amamvetsera zinthu zimene sitingauze munthu aliyense ngakhale zimene anthu ena sangazimvetse. Posachedwapa Mulungu achotsa mavuto onse amene anthu amakumana nawo. Ndipotu ngakhale panopa, Iye amatithandiza m’njira zimene sitingaziganizire. Amatisamalira komanso kutilimbikitsa tikakhala pa mavuto.”​—Salimo 136:23.

Monga mmene taonera m’chitsanzo cha Toru, kudziwa kuti posachedwapa Mulungu athetsa mavuto onse komanso kupukuta misozi yonse ya anthu, kumatithandiza kuona kuti tikuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo ndiponso kumatithandiza kukhala ndi moyo wabwino panopo. Ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene ladzadza ndi mavuto, tikhoza kumakhalabe osangalala podziwa kuti Mulungu amatikonda.