Posachedwapa Mulungu Athetsa Mavuto Onse
“Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti? Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti?” (Habakuku 1:2, 3) Amenewa ndi mawu a Habakuku yemwe anali munthu wabwino ndipo Mulungu ankasangalala naye. Kodi zimene anafunsazi zikusonyeza kuti analibe chikhulupiriro? Ayi si choncho. Mulungu anamutsimikizira Habakuku kuti adzathetsa zinthu zoipazi pa nthawi yake.—Habakuku 2:2, 3.
Inuyo kapena wachibale wanu akamavutika, zimakhala zosavuta kuyamba kuona kuti Mulungu akuchedwa kuthetsa mavuto. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Petulo 3:9.
KODI MULUNGU ADZATHETSA LITI MAVUTOWA?
Athetsa posachedwapa! Yesu ananena za m’badwo umene udzaone zizindikiro zosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza “a nthawi ino.” (Mateyu 24:3-42) Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesuwu ndi chizindikiro chakuti posachedwapa Mulungu athetsa mavutowa. *
Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavutowa? Pamene Yesu anali padzikoli anasonyeza mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake pothetsa mavuto. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
Ngozi Zadzidzidzi: Pamene Yesu ndi atumwi ake ankawoloka Nyanja ya Galileya, anakumana ndi chimphepo champhamvu chamkuntho chimene chinkafuna kumiza ngalawa yawo. Zimene Yesu anachita pamenepa, zinasonyeza kuti iye komanso Atate wake ali ndi mphamvu zotha kulamulira zinthu zam’chilengedwe. (Akolose 1:15, 16) Iye anangoti: “Leka! Khala bata!” Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? Baibulo limati: “Mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.”—Maliko 4:35-39.
Matenda: Yesu anachiritsa anthu osaona, olumala ngakhalenso anthu ena omwe ankadwala matenda osiyanasiyana monga akugwa komanso khate. “Onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawachiritsa.”—Mateyu 4:23, 24; 8:16; 11:2-5.
Njala: Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Atate wake anamupatsa pochulukitsa chakudya chochepa. Baibulo limanena kuti Yesu anadyetsa anthu masauzande ambiri maulendo awiri.—Mateyu 14:14-21; 15:32-38.
Imfa: Baibulo limanena kuti Yesu anaukitsa anthu atatu ndipo zimenezi zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu yothetsa imfa. Mmodzi mwa anthu amene Yesu anaukitsa anali atakhala m’manda kwa masiku 4.—Maliko 5:35-42; Luka 7:11-16; Yohane 11:3-44.
^ ndime 5 Kuti mumve zambiri zokhudza masiku otsiriza, onani mutu 9 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungapangenso dawunilodi bukuli pa www.jw.org/ny.