Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana

Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana

Vuto Limene Limakhalapo

Tikamapewa anthu amene timawaganizira zolakwika, tsankho limakula kwambiri mumtima mwathu. Tikamangocheza ndi anthu amene timaona kuti timafanana nawo, tikhoza kumaganiza kuti zimene ifeyo timaganiza, mmene timamvera mumtima mwathu, komanso mmene timachitira zinthu ndi zokhazo zimene zili zabwino.

Mfundo ya M’Baibulo

“Futukulani mtima wanu.”—2 AKORINTO 6:13.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Mawu akuti “mtima” angatanthauze mmene timamvera komanso zimene timakonda. Tikamangokonda anthu okhawo amene timafanana nawo, sitingathe kufutukula mtima wathu. Kuti tipewe vuto limeneli, tiyenera kumachezanso ndi anthu amene timasiyana nawo zinthu zina.

Kodi Kucheza ndi Anthu Osiyanasiyana N’kothandiza Bwanji?

Tikayamba kudziwana ndi anthu ena, timamvetsa chifukwa chake amachita zinthu mosiyana ndi ifeyo. Ndiyeno tikamagwirizana nawo kwambiri, timaiwala kuti ndi ochokera mumtundu wina. Timayamba kuwalemekeza kwambiri ndipo nafenso timayamba kusangalala ndi zimene iwo amasangalala nazo komanso kumva chisoni ndi zimene zikuwamvetsa chisoni.

Taganizirani chitsanzo cha Nazaré. Pa nthawi ina anali ndi maganizo atsankho kwa anthu ochokera m’mayiko ena. Pofotokoza zimene zinamuthandiza kuti asinthe, iye anati: “Ndinkacheza nawo komanso kugwira nawo ntchito. Ndinaona kuti zimene anthu am’dera lathu ankanena zokhudza anthuwa zinali zosiyana kwambiri ndi mmene iwo alili. Ukayamba kugwirizana ndi anthu a zikhalidwe zina, umaphunzira kuti si onse amachita zinthu mofanana ndipo umayamba kuwakonda komanso kuwalemekeza.”

Zimene Mungachite

Muziyesetsa kupeza mpata wolankhulana ndi anthu ochokera m’mayiko ena, m’mitundu ina kapena omwe amalankhula chinenero china. Mukhoza

  • Kuwafunsa kuti akuuzeni mbiri yawo.

  • Kuwaitana kuti mukadye nawo chakudya.

  • Kumvetsera nkhani zawo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene amaona kuti ndi zofunika.

Mukamayesetsa kumvetsa mmene zimene akumana nazo zasinthira moyo wawo mukhoza kuyamba kuona moyenera anthu amtundu umenewo.