Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzidziwa Zoona Zake

Muzidziwa Zoona Zake

Vuto Limene Limakhalapo

Ambiri amachitira ena tsankho chifukwa sadziwa zolondola zokhudza anthuwo. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • Anthu ena amene amalemba anzawo ntchito amaganiza kuti akazi sangagwire ntchito zofunika luso lapadera, mphamvu komanso kuganiza kwambiri.

  • M’zaka zapakati pa 500 ndi 1500 AD, ku Europe anthu ankanena kuti Ayuda amathira poizoni m’zitsime komanso kufalitsa matenda. Ndipo pa nthawi ya ulamuliro wachipani cha Nazi ku Germany, Ayuda anakumananso ndi vuto langati lomweli chifukwa anthu ankawanamizira kuti ndi omwe ankayambitsa mavuto azachuma m’dziko la Germany. Zochitika ziwiri zonsezi zinachititsa kuti Ayuda azisalidwa kwambiri ndipo tsankho limeneli likuchitikabe mpaka pano.

  • Ambiri amaganiza kuti munthu aliyense yemwe ndi wolumala sasangalala komanso amangokhala wolusa.

Anthu amene amakhulupirira zinthu zabodza ngati zimenezi, amapereka zitsanzo komanso maumboni awo otsimikizira kuti zimene amaganizazo ndi zoona. Ndipo amaona kuti aliyense amene amaganiza mosiyana ndi iwowo ndi wosazindikira.

Mfundo ya M’Baibulo

“Si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu.”​—MIYAMBO 19:2.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Ngati sitidziwa zolondola, tikhoza kuchita zinthu zolakwika. Tikamangokhulupirira zam’maluwa m’malo mofufuza zoona zake, tingayambe kumaona anthu ena molakwika.

Kodi Kudziwa Zoona Zake N’kothandiza Bwanji?

Kudziwa zolondola zokhudza anthu amtundu winawake kungatithandize kuti tisamangokhulupirira zinthu zabodza zomwe anthu ena amanena zokhudza anthuwo. Komanso tikangozindikira kuti zimene anthu ena amanena zokhudza mtundu winawake wa anthu ndi zabodza, timasiya kumangokhulupirira zinthu zoipa zimene tamva anthu ena akunena zokhudza anthuwo.

Zimene Mungachite

  • Anthu akhoza kumanena kuti anthu a gulu linalake ali ndi khalidwe loipa. Komabe ndi bwino kumakumbukira kuti m’gulu limenelo muli anthu enanso ambirimbiri omwe alibe khalidwe loipalo.

  • Muzikumbukira kuti zikhoza kutheka kuti zimene mukudziwa zokhudza gulu la anthulo ndi zochepa.

  • Muziyesetsa kudziwa zolondola zokhudza anthuwo kuchokera kwa anthu komanso malo odalirika.