Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzizindikira Kuti Ena Amakuposani

Muzizindikira Kuti Ena Amakuposani

Vuto Limene Limakhalapo

Kudzikonda kungachititse munthu kukhala watsankho. Munthu wodzikonda amadziona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa anthu ena komanso amaona anthu osiyana ndi iyeyo kuti ndi otsalira. Aliyense akhoza kuyamba kukhala ndi maganizo amenewa. Buku lina linati: “Ngakhale kuti zimasiyanasiyana, koma anthu azikhalidwe zambiri amaona kuti moyo umene amakhala, zakudya zawo, zovala, zinthu zimene amakonda kuchita, zikhulupiriro zawo, mfundo zimene amayendera komanso zinthu zina, ndi zapamwamba kwambiri kuposa za anthu a zikhalidwe zina.” (Encyclopædia Britannica) Kodi tingatani kuti tichotse maganizo amenewa?

Mfundo ya M’Baibulo

Muzichita zinthu “modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”​—AFILIPI 2:3.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Kuti tipewe mtima wodzikuza, tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa. Tikakhala odzichepetsa timazindikira kuti pali zinthu zina zimene anthu azikhalidwe zina amachita bwino kuposa ifeyo. Si zoona kuti anthu achikhalidwe chinachake amachita bwino pa zinthu zonse.

Taganizirani chitsanzo cha Stefan. Iye anakulira m’dziko la Chikomyunizimu koma anasiya kuchitira tsankho anthu omwe amachokera m’mayiko amene satsatira Chikomyunizimu. Iye anati: “Zimene ndaona ndi zakuti kuona ena kukhala okuposa kumathandiza kuthetsa mtima watsankho. Ndimazindikira kuti sindingadziwe zonse, ndiye ndimaona kuti ndikhoza kuphunzira zinazake kwa munthu wina aliyense.”

Zimene Mungachite

Muziona zinthu moyenera komanso muzivomereza kuti nthawi zina mumalakwitsa. Muzivomerezanso kuti anthu ena amachita bwino kwambiri zinthu zimene inuyo mumalephera. Musamaganize kuti anthu onse a mtundu winawake ali ndi vuto lofanana.

M’malo mongothamangira kuganizira zolakwika zokhudza munthu wa mtundu winawake, mungachite bwino kudzifunsa kuti:

Muzivomereza kuti anthu ena amachita bwino kwambiri zinthu zimene inuyo mumalephera

  • ‘Kodi khalidwe limene silindisangalatsa mwa munthu ameneyu ndi loipadi kapena tangokhala kuti anthufe timachita zinthu mosiyana?’

  • ‘Kodi munthu ameneyu akhozanso kuona kuti ndili ndi makhalidwe enaake oipa?’

  • ‘Kodi munthu ameneyu amachita bwino zinthu ziti kuposa ineyo?’

Ngati mutayankha mafunso amenewa moona mtima, mukhoza kuthetsa mtima watsankho komanso mungayambe kuona makhalidwe abwino amene munthuyo ali nawo.