Zimene Zili M’magaziniyi: Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri
Buku Lakale Lokhala ndi Mfundo Zothandiza Masiku Ano
Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa nkhani zachipembedzo. Lilinso ndi malangizo othandiza pa mbali zonse za moyo wathu monga:
Kukhala ndi moyo wathanzi
Kukhala ndi mtendere wa m’maganizo
Kukhala ndi banja labwino komanso mabwenzi abwino
Kugwiritsa ntchito bwino ndalama
Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu
Buku Lothandiza Kuposa Lililonse
Kwa zaka zambiri, Baibulo lakhala likuthandiza anthu kukhala ndi moyo wabwino. Panopa, Baibulo likupezeka m’zinenero zambiri. Werengani magaziniyi kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni.