Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Kugwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Mfundo za m’Baibulo zathandiza anthu ambiri kupewa mavuto a zachuma.

MUZILINGANIZA BWINO ZINTHU

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”​—Miyambo 21:5.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Kuti zinthu zizikuyenderani bwino muyenera kukhala ndi zolinga n’kuyesetsa kumazikwaniritsa. Choncho musanayambe kugwiritsa ntchito ndalama muzikonza bajeti. Musamaiwale kuti n’zosatheka kugula chilichonse chimene mukufuna. Ndiye muzigwiritsa ntchito mwanzeru ndalama zanu.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzitsatira bajeti yanu. Muzilemba zinthu zonse zimene mukufunikira ndipo muzizigawa m’magulu monga zakudya, zovala komanso ndalama ya lendi. Kenako lembani ndalama zimene zingafunike pagulu lililonse. Ngati mwagwiritsa ntchito ndalama zambiri pagulu lina kuposa zimene munalemba, mungagwiritse ntchito ndalama za pagulu lina. Mwachitsanzo, ngati mwawononga ndalama zambiri pogula mafuta a galimoto, mungagwiritse ntchito ndalama zomwe munasungira zinthu zosafunika kwenikweni monga kupita kunyanja.

  • Muzipewa ngongole zosafunikira. Ngati n’zotheka muziyesetsa kupewa ngongole. Mungachite bwino kusungira ndalama zoti mudzagulire chinthu chimene mukufuna m’malo motenga pangongole. Ngati mumagwiritsa ntchito khadi la ngongole, mungachite bwino kupereka ngongole yonse kuti musalipire chiwongoladzanja chochuluka. Mukakhala ndi ngongole, muzikonza mmene mungadzabwezere ngongoleyo ndipo yesetsani kutsatira zimene mwakonzazo.

    Kafukufuku wina anasonyeza kuti munthu akamagula zinthu pogwiritsa ntchito khadi la ngongole, amawononga ndalama zambiri. Choncho ngati muli ndi khadi la ngongole muzikhala wodziletsa kwambiri.

MUZIPEWA MAKHALIDWE OIPA

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chifukwa cha kuzizira, waulesi salima. Iye azidzapemphapempha nthawi yokolola koma sadzapatsidwa kanthu.”​—Miyambo 20:4.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Ulesi umachititsa munthu kukhala pa umphawi. Choncho muziyesetsa kugwira ntchito mwakhama komanso kugwiritsa ntchito bwino ndalama zanu kuti musadzavutike m’tsogolo.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzigwira ntchito mwakhama. Muzisamala ntchito yanu pokhala a khama komanso odalirika. Mabwana amafuna munthu wolimbikira ntchito.

  • Muzichita zinthu moona mtima. Musamabere abwana anu. Kusakhulupirika kukhoza kuipitsa mbiri yanu zomwe zingachititse kuti muvutike kupeza ntchito ina.

  • Musakhale adyera. Munthu amene amangokhalira kusakasaka ndalama akhoza kuwononga thanzi lake, banja lake, komanso sangakhale ndi anzake.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO

Mukhoza kuwerenga Baibulo pa intaneti. Baibuloli likupezeka m’zinenero zoposa 260 pa jw.org

MUSAMAWONONGE NTHAWI KOMANSO NDALAMA ZANU POCHITA ZINTHU ZOSATHANDIZA.

“Chidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka, ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.”​—MIYAMBO 23:21.

MUSAMADERE NKHAWA ZINTHU ZOMWE SIZINACHITIKE.

“Lekani kudera nkhawa moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.”​—MATEYU 6:25.

MUZIPEWA MTIMA WANSANJE.

“Munthu wanjiru amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali, koma sadziwa kuti umphawi udzamugwera.”​—MIYAMBO 28:22.