GALAMUKANI! March 2015 | Kodi Kukhulupirira Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’zochititsa chidwi kwambiri.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Anthu ambiri amaona kuti yankho la funso loti Mulungu aliko ndi lovuta ndipo ena saganizira n’komwe nkhaniyi. Kodi kudziwa yankho lake kungatithandize bwanji?

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku Africa

Kuchita ziphuphu komanso kupha zipembere popanda chilolezo ndi kuphwanya malamulo.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mungatani Kuti Muzigwirizana Ndi Apongozi Anu?

Mfundo zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti nkhani zokhudza apongozi zisasokoneze banja lanu.

TIONE ZAKALE

Malamulo Omwe Anagawanitsa Dziko

Pa mayiko onse a ku America, n’chifukwa chiyani Brazil ndi dziko lomwe anthu ambiri amalankhula Chipwitikizi?

Kamphepo Kayaziyazi Komanso Dzuwa Ndi Mankhwala

Asayansi a makono apeza kuti zimene asayansi a m’zaka za 1800 anapeza n’zoona.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kutchova Juga

Kodi ndi masewera osangalatsa chabe?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Akadziwotche Omwe Amamva Kwambiri

Akadziwotchewa ali ndi timakutu tating’ono koma amamva kwambiri kuposa nyama ina iliyonse.

Zina zimene zili pawebusaiti

Zimene Achinyamata Amanena pa Nkhani ya Nkhanza Zokhudza Kugonana

Onani zimene achinyamata 5 ananena pa nkhani yochitiridwa nkhanza zokhudza kugonana komanso zimene mungachite wina akakuchitirani nkhanzazo.

Uzikhala Waukhondo

Yehova amaika chilichonse pamalo oyenera. Onani zimene nanunso mungachite kuti muzikhala aukhondo