GALAMUKANI! August 2013 | Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Wautali?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti asayansi komanso azachipatala akhoza kuthandiza kuti anthu akhale ndi moyo wautali. Koma kodi asayansi angathandizedi anthu kuti adzakhale ndi moyo wosatha?

Zochitika Padzikoli

Muli nkhani monga: Malungo ayambiranso ku Greece, ku China kuli azimayi ambiri osakwatiwa, anthu ambiri amene anali asilikali ku United States akumadzipha, ndi nkhani zina.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala

Achinyamata ena amadzivulaza mwadala. N’chiyani chimawachititsa kuti azichita zimenezi? Kodi mungamuthandize bwanji mwana wanu ngati amadzivulaza mwadala?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Wautali?

Kumvetsa bwino chimene chimapangitsa kuti anthufe tizikalamba kenako n’kumwalira kungatithandize kudziwa kuti n’zotheka kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

KUCHEZA NDI ANTHU

Dokotala wa Mafupa Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Dr. Irène Hof Laurenceau akufotokoza chifukwa chake anakhala wa Mboni za Yehova.

Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?

Kodi kutchalitchi kwanu amaphunzitsa za Utatu? Kodi mfundo zimene anagwirizana pa msonkhano wa ku Nicaea zimakhudza zimene mumakhulupirira?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mowa

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena zomwe zingakuthandizeni kuti mudziwe kuipa kwa mowa ndi ubwino wake.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mbalame ya Albatross Yosatopa ndi Kuuluka

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chomwe chimathandiza mbalame zina kumauluka m’mwamba kwambiri komanso kwa nthawi yaitali koma osakupiza mapiko ake olo kamodzi.

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?

Achinyamata ena ali ndi vuto lodzivulaza mwadala. Ngati muli ndi khalidwe limeneli, kodi mungatani kuti mulisiye?

Anthu Otchulidwa M’Baibulo Amene Akufanana ndi Yosefe

Koperani ndi kusindikiza nkhaniyi ndiyeno lembani kufanana pakati pa Yosefe ndi anthu ena asanu otchulidwa m’Baibulo.