Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Wautali?

Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Wautali?

HARRIET anamwalira mu 2006, ali ndi zaka 175. Komatu Harriet anali kamba wa pachilumba cha Galapagos ndipo ankakhala kumalo osungira nyama a ku Australia. Kambayu anakhala ndi moyo kwa zaka zochuluka poyerekeza ndi zaka zimene anthu amakhala ndi moyo. Komabe pali zinthu zina zomwenso zimakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali. Taonani zitsanzo izi:

  • Akatswiri ena a ku Finland ananena kuti nkhono ina yam’madzi yotchedwa Margaritifera margaritifera, imatha kukhala ndi moyo kwa zaka 200.

  • Pali nkhono inanso yam’madzi yotchedwa Ocean quahog, yomwe nthawi zambiri imakhala ndi moyo kwa zaka zoposa 100 ndipo ena amati imatha kukhala zaka zoposa 400.

  • Mitengo ina monga mtengo wa paini wotchedwa Britstlecone umatha kukhala zaka masauzande ambiri.

Koma anthu, omwe ndi zolengedwa za nzeru kwambiri, nthawi zambiri amangokhala ndi moyo zaka 80 kapena 90 basi, ngakhale kuti amakhala atayesetsa kuchita zosiyanasiyana kuti akhale ndi moyo wautali.

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani timangokhala zaka zochepa choncho? Kodi pangapezeke njira ina yotithandiza kuti tizikhala ndi moyo kwa zaka zambiri? Anthu ambiri amakhulupirira kuti asayansi komanso achipatala akhoza kuwathandiza.

 Kodi Asayansi Angapeze Njira Yotalikitsira Moyo?

Asayansi athandiza kwambiri pa nkhani ya zachipatala. Mwachitsanzo, magazini ina inanena kuti: “[Ku United States] chiwerengero cha anthu amene amamwalira chifukwa cha matenda opatsirana komanso chifukwa cha mavuto amene amabwera pobereka, chatsika kwambiri. Imfa za ana zachepa ndi 75 peresenti kuyambira m’chaka cha 1960.” Komabe ngakhale zili choncho, asayansi alephera kutalikitsa moyo wa munthu. Magazini ija inanenanso kuti: “Kwa zaka zambiri, asayansi akhala akufufuza chimene chimapangitsa kuti munthu azikalamba, koma sanapezebe yankho. Komabe pali umboni wosonyeza kuti munthu amakalamba chinachake chakasokonekera m’maselo a mu DNA. Ngati munthu amakalamba chifukwa cha zimenezi, ndiye kuti pakhoza kupezekadi njira yopewera kuti maselo a DNA asasokonekere komanso kuti anthu asamakalambe.”—Scientific American.

“Kwa zaka zambiri, asayansi akhala akufufuza chimene chimapangitsa kuti munthu azikalamba, koma sanapezebe yankho”

Asayansi atulukira njira yatsopano yofufuzira DNA yotchedwa epigenetics. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, iwo amafufuza DNA n’cholinga choti adziwe chimene chimachititsa kuti munthu azikalamba.

Selo lililonse limakhala ndi malangizo omwe amathandiza popanga maselo ena atsopano. Ambiri mwa malangizo amenewa amapezeka mkati mwa DNA. DNA imaoneka ngati makwerero opiringizana ndipo pamwamba pake pamapezeka tinthu totchedwa epigenome. Asayansi akuyesetsa kufufuza kuti adziwe mmene tinthu timeneti timagwirira ntchito.

Tinthu timeneti timapereka uthenga ku maselo a mu DNA ndipo uthengawo umatsogolera mmene malangizo a mu DNA angapangidwire. Mwachitsanzo, munthu akapanikizika maganizo, tinthuti timapereka uthengawu ku maselo a DNA omwe amapangitsa kuti munthu asinthe mmene amaonekera komanso mmene amachitira zinthu. Zimene asayansi atulukira chaposachedwapa zokhudza epigenome, zapangitsa kuti aziona kuti akhoza kupeza chimene chimayambitsa matenda osiyanasiyana komanso chimene chimachititsa kuti anthu azikalamba.

Wasayansi wina, dzina lake Nessa Carey, ananena kuti: “Asayansi akhala akugwiritsa ntchito njira imeneyi pofuna kudziwa chimene chimayambitsa matenda ngati nyamakazi ya m’mafupa, matenda a maganizo komanso khansa. Njira imeneyi ingatithandizenso kudziwa chimene chimachititsa kuti munthu azikalamba.” Choncho, asayansi atati afufuza zambiri zokhudza epigenome akhoza kupeza njira zochizira matenda osiyanasiyana monga khansa, komanso akhoza kupeza njira yotalikitsira moyo. Pakalipano, asayansi sanatulukirebe chimene chimachititsa kuti anthu azikalamba. Carey ananena kuti: “Panopa tikuyenderabe mfundo yomwe takhala tikulimbikitsa m’mbuyo monsemu, yoti anthu azidya masamba ambiri komanso azichita zinthu zolimbitsa thupi [kuti asakalambe].”

Kodi n’chifukwa chiyani anthu amayesetsa kutalikitsa moyo? N’chifukwa chiyani anthufe timafuna kukhala ndi moyo wautali? Nyuzipepala ina ya ku Britain, yotchedwa The Times, inanena kuti: “Anthu ambiri amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana zosonyeza kuti safuna kufa. Mwachitsanzo, ena amakhulupirira kuti mzimu suufa, ena amati adzaukitsidwa kapena kuti akadzafa adzabadwanso kwinakwake.” Tiyeni tione chimene chimapangitsa anthu kuti azilakalaka kutalikitsa moyo wawo. Zimenezi zingatithandizenso kudziwa chimene chimapangitsa kuti anthu azikalamba.

N’chifukwa Chiyani Anthufe Timafuna Kukhala Ndi Moyo Mpaka Kalekale?

Kwa zaka zambiri, anthu akhala akufunitsitsa kupeza yankho la funso limeneli. Kodi tingapeze yankho lokhutiritsa, lomwe lingafotokoze bwino chifukwa chake anthufe timakalamba komanso chifukwa chimene timafunira  kuti tizikhala ndi moyo wautali? Inde, yankho lilipo ndipo tikhoza kulipeza m’Baibulo.

Baibulo limasonyeza kuti anthu ndi nyama amafanana pa zinthu zina koma anthu analengedwa mwapadera. Mwachitsanzo, lemba la Genesis 1:27, limasonyeza kuti Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mulungu anatilenga m’njira yoti tizitha kukondana, kuchita zinthu mwachilungamo komanso mwanzeru. Mulungu sangafe, choncho iye anatilenganso ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Lemba la Mlaliki 3:11, limati: “[Mulungu] anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”

Umboni wina wosonyeza kuti Mulungu anatilenga kuti tizikhala ndi moyo kwa nthawi yaitali, ndi mmene ubongo wathu umagwirira ntchito. Ubongo wathu umatha kuphunzira zinthu zambirimbiri n’kumazikumbukira. Buku lina linanena kuti ubongo umatha kukumbukira zinthu zakalekale komanso kuphunzira zinthu zambirimbiri “koma sungafike poti wadzadza n’kukanika kuphunziranso zinthu zina.” (The Encyclopedia of the Brain and Brain Disorders) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu potilenga ankafuna kuti tiziphunzira zinthu mpaka kalekale. Choncho zimene anthufe timachita zimasonyeza kuti Mulungu anatilenga kuti tikhale ndi moyo mpake kalekale. Ndiyeno n’chifukwa  chiyani anthufe timadwala ndiponso timakalamba n’kumwalira?

N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kumwalira?

Mwamuna ndi mkazi oyambirira anali ndi matupi opanda uchimo komanso anali ndi ufulu wosankha zochita. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, anasankha kusamvera Mulungu amene anawalenga. * (Genesis 2:16, 17; 3:6-11) Zimene anachitazi zinachititsa kuti azidziimba mlandu komanso kuti azichita manyazi. Kuyambira pamenepo, matupi awo anayambanso kufooka zomwe zinachititsa kuti m’kupita kwa nthawi akalambe n’kumwalira. N’chifukwa chake lemba la 1 Akorinto 15:56, limanena kuti: “Mphamvu imene imabala imfa ndiyo uchimo.”

Chifukwa chakuti tinachokera kwa Adamu ndi Hava, tonsefe timabadwa tili ochimwa, kapena kuti tili ndi mtima wofuna kuchita zoipa. N’chifukwa chake lemba la Aroma 5:12 limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’

Kodi zonsezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti sayansi singathandize kuti anthu akhale ndi moyo wautali. Mulungu yekha ndi amene angathane ndi uchimo. Baibulo limasonyeza kuti Iye adzachitadi zimenezi.

“Iye Adzameza Imfa Kwamuyaya”

Mulungu anayamba kale kuchita zinthu zoti achotse uchimo ndi imfa. Iye anatumiza Yesu Khristu kuti adzatifere. Kodi imfa ya Yesu imatithandiza bwanji? Yesu anabadwa alibe uchimo ndipo “sanachite tchimo.” (1 Petulo 2:22) Choncho, akanatha kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Koma anapereka moyo wake kuti atiwombole ku machimo athu. Baibulo limanena kuti Yesu anapereka moyo wake “dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Posachedwapa, dipo limeneli lidzagwira ntchito yake mokwanira. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Taonani malemba otsatirawa:

  • “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”Yohane 3:16.

  • “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.

  • Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”1 Akorinto 15:26.

  • “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu.  . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Ndiyeno kodi tidzakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limasonyeza kuti anthu ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Zimenezi zidzachitika Mulungu akadzachotsa anthu oipa onse. (Salimo 37:28, 29) Yesu ankaganizira za chiyembekezo chimenechi pamene anauza munthu amene anapachikidwa pambali pake kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.

Pofika pano taona kuti n’zomveka kuti anthufe timafuna kukhala ndi moyo kwa nthawi yaitali chifukwa ndi mmene Mulungu anatilengera. Ndipo adzakwaniritsadi chikhumbo chimenechi. (Salimo 145:16) Komabe, kuti tidzasangalale ndi moyo umenewo pali zinthu zimene tiyenera kuchita. Mwachitsanzo, tiyenera kukhulupirira Mulungu. Lemba la Aheberi 11:6 limanena kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chimenechi ngati waphunzira mfundo zolondola za m’Baibulo. (Aheberi 11:1) Inunso mukhoza kukhala ndi chikhulupiriro choterocho ngati mutaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu kapena mukhoza kupita pa webusaiti ya www.jw.org/ny.

^ ndime 21 Chifukwa chakuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, panayambikanso nkhani zikuluzikulu zokhudza Mulungu. Nkhani zimenezi zingatithandizenso kumvetsa chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika. Kuti mudziwe zambiri werengani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pa webusaiti ya www.jw.org/ny.