Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachinyengo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachinyengo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachinyengo?

“Kuchita zachilungamo pa nkhani za malonda n’kwachikale, ndipo amene amayesetsa kupewa chinyengo zinthu sizimawayendera.”—Anatero Stephen, wa ku United States.

KODI inuyo mukugwirizana ndi maganizo amenewa? Kunena zoona, anthu amene amachita zachinyengo amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino. Chifukwa choona zimenezi, anthu ena amayambanso kuchita zachinyengo ngakhale kuti poyamba anali anthu achilungamo.

Kufuna Kulemera. Anthu ambiri amafuna atakhala ndi ndalama komanso katundu wambiri. Choncho mwayi ukapezeka amalolera kuchita zachinyengo kuti apeze zimene akufuna.

● “Ndinapatsidwa udindo wosankha makampani oti azigulitsa katundu wawo ku kampani yathu, koma nthawi zambiri makampani amenewa amafuna kuti azindipatsa ziphuphu kuti apeze mwayi umenewu. Anthu ambiri zimawavuta kukana ziphuphu.”—Anatero Franz, wa ku Middle East.

Kufuna Kupeza Phindu Lochuluka. M’zaka zaposachedwapa, makampani ambiri akhala akukumana ndi mavuto a zachuma. Komanso makampaniwa akukumana ndi mavuto ena monga kuzolowera njira zamakono zopangira katundu ndiponso kupikisana ndi makampani opanga katundu wofanana ndi wawo. Ndiponso anthu ogwira ntchito amaona kuti kuchita zachinyengo ndi njira yokhayo imene ingawathandize kukwanitsa zimene mabwana awo akuwayembekezera kuti achite.

● “Tinkaona kuti tiyenera kuchita zachinyengo basi. . . . Apo ayi kampani yathu igwa.”—Anatero Reinhard Siekaczek, amene nthawi ina anamangidwa chifukwa cha ziphuphu.—The New York Times.

Kukakamizidwa ndi Anthu Ena. Nthawi zina anthu ogwira nawo ntchito kapena makasitomala amapempha kapena kukakamiza anzawo kuti azichita nawo zachinyengo.

● “Bwana wa kukampani inayake imene timagulitsako katundu wathu wambiri anandiuza kuti ndimupatse kangachepe, kuti kampani yakeyo ipitirize kugula katundu ku kampani yathu.”—Anatero Johan, wa ku South Africa.

Chikhalidwe. M’zikhalidwe zina, si zachilendo anthu a bizinezi kupatsana mphatso. Koma nthawi zina, zingakhale zovuta kudziwa ngati cholinga cha mphatsoyo chili kuthokoza chabe kapena kuhonga. M’mayiko ambiri, anthu ena ogwira ntchito zaboma, amafuna kuti apatsidwe ndalama asanagwire ntchito inayake ndipo akapatsidwa ndalamazo amagwira ntchitoyo modzipereka kwambiri.

● “Nthawi zambiri zimavuta kusiyanitsa pakati pa ndalama imene yaperekedwa ngati chiphuphu ndi ndalama yoperekedwa n’cholinga chothokoza.”—Anatero William, wa ku Colombia.

Umphawi Komanso Dera Lochokera. Anthu amene ndi ovutika kwambiri kapena amene amakhala m’mayiko amene chinyengo chili paliponse, amakakamizika kuchita zachinyengo. M’madera amenewa, anthu amene amayesetsa kuchita zachilungamo amaonedwa kuti sadziwa kusamalira mabanja awo.

● “Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto kuchita zachinyengo, bola usagwidwe.”—Anatero Tomasi, wa ku Congo Kinshasa.

Maganizo Omwe Amalimbikitsa Zachinyengo

Anthu ambiri amaona kuti n’zovuta kwambiri kupewa chinyengo. Kafukufuku wina amene anachitika ku Australia, anasonyeza kuti pa mabwana 10 alionse, mabwana 9 amaona kuti chinyengo “n’choipa koma n’zosatheka kuchipewa.” Anthu amene anafunsidwa pa kafukufukuyu ananena kuti akhoza kulolera kuchita chilichonse kuti apeze mwayi winawake kapena kuti asangalatse kampani yawo.

Ndipotu anthu amene amachita zachinyengo amadziona ngati ndi anthu achilungamo. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Magazini ina inati: “Anthu ambiri amayesetsa kuchita zachinyengo mmene angathere kuti apeze phindu, koma amayesetsanso kwambiri kupeza zifukwa zodzikhululukira n’cholinga choti azidziona kuti ndi anthu achilungamo.” (Journal of Marketing Research) Zimenezi zikusonyeza kuti iwo amaona mopepuka zinthu zachinyengo zimene amachita.

Mwachitsanzo, munthu akabera kapena kupusitsa mnzake anganene kuti “ndamuimba” kapena “ndamuchangamutsa,” pomwe ndalama ya chiphuphu angaitchule kuti “ya fanta.”

Enanso amaona kuti palibe vuto ndi kuchita zachinyengo malinga asagwidwe. Tom, yemwe amagwira ntchito pakampani ina yokhudzana ndi za ndalama, ananena kuti: “Anthu ambiri amaganiza kuti munthu wachilungamo ndi amene amachita zinthu popanda kugwidwa, osati kwenikweni amene amachita zinthu moona mtima.” David, yemwe kale ankachita bizinezi, ananena kuti: “Ngakhale kuti anthu sasangalala akadziwa kuti munthu wina wachita zachinyengo, iwo amaonabe kuti chinyengocho chilibe vuto malinga ngati sunagwidwe. Ndipo anthu amene amachita zachinyengo osagwidwa, amaonedwa kuti ndi anzeru komanso ochenjera.”

Anthu ambiri amanena kuti popanda kuchita zachinyengo zinthu sizingawayendere. Munthu wina, yemwe wachita bizinezi kwanthawi yaitali, anati: “Mtima wampikisano umachititsa anthu kunena kuti, ‘Munthu uyenera kuchita china chilichonse, ngakhale choipa, kuti upeze mwayi winawake.’” Koma kodi zimenezi n’zoona? Ayi, chifukwa anthu amene amaganiza kuti kuchita zachinyengo kulibe vuto amakhala ‘akudzinyenga ndi maganizo onama’. (Yakobo 1:22) Nkhani yotsatira ifotokoza ubwino wochita zinthu mwachilungamo.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Anthu ambiri amaganiza kuti munthu wachilungamo ndi amene amachita zinthu popanda kugwidwa, osati kwenikweni amene amachita zinthu moona mtima”

[Chithunzi patsamba 5]

Anthu ambiri amanena kuti popanda kuchita zachinyengo zinthu sizingawayendere bwino