Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchita Zinthu Mwachilungamo N’kothandiza

Kuchita Zinthu Mwachilungamo N’kothandiza

 Kuchita Zinthu Mwachilungamo N’kothandiza

“Munthu amasangalala ndi chakudya chimene wachipeza mwachinyengo, koma pambuyo pake, m’kamwa mwake mumadzaza miyala.”—Miyambo 20:17.

KODI kuchita zinthu mwachinyengo kungathandize kuti bizinezi yanu iziyenda bwino? Ayi. Chinyengo n’chimene chingachititse kuti bizinezi yanuyo isokonekere kwambiri. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ukamachita zinthu mwachinyengo, anthu samakudalira ndipo m’kupita kwa nthawi, bizinezi imagwa.

Phindu Lochita Zinthu Mwachilungamo

Kaya mukudziwa kapena ayi, kuchita zinthu mwachilungamo n’kothandiza kwambiri. Umboni wa zimenezi ndi zimene zinamuchitikira Franz, yemwe tinamutchula m’nkhani yapitayi. Iye anati: “Nditangoyamba ntchito, mabwana anga anandiyesa m’njira zosiyanasiyana popanda ineyo kudziwa. M’kupita kwa nthawi ndinazindikira kuti mabwanawo ankandiyesa ndipo ndinasangalala kwambiri kuti ndinachita bwino pa zinthu zimene ankandiyesazo. Chifukwa chochita zinthu mwachilungamo, mabwana anga anandipatsa maudindo ena komanso amandilola kuchita zinthu zambiri mwaufulu. Ndikudziwa kuti pali anthu ena anzeru kwambiri amene angachite bwino ntchito imene ndimagwira kuposa ineyo. Koma ndikuona kuti amandidalira chifukwa chakuti ndimachita zinthu mwachilungamo.”

Chinyengo Chingakuikeni M’mavuto

David, munthu wabizinezi yemwe tinamutchula poyamba uja, anati: “Ndikaona anthu akuphwanya malamulo chifukwa chofuna kupeza ndalama mwachangu, mumtima ndimati, ‘Pangapite nthawi yaitali bwanji, koma adzagwidwa basi.’ Kunena zoona, kuchita zinthu zachinyengo kumabweretsa mavuto. Pakampani yathu tinkakana kuchita zinthu mwachinyengo. Makampani ambiri amene ankapanga zachinyengo, anagwa, ndipo eni akewo anamangidwa. Kampani yathu inapewa mavuto amenewa.”

Munthu wina dzina lake Ken, ankafuna kutsegula famu ya ng’ombe m’dziko lina kum’mwera chakum’mawa kwa Africa. Munthuyu akanatha kupatsa akuluakulu a boma ziphuphu n’cholinga choti asamulipiritse msonkho komanso kuti katundu wake alowe m’dzikolo mofulumira. Koma iye anati: “Anthu ambiri ankachita zinthu zachinyengo. Chifukwa chofuna kuchita zinthu mwachilungamo, zinatitengera zaka 10 kuti atilole kutsegula famuyo. Koma timaona kuti tinachita bwino chifukwa anthu amene ankapereka ziphuphu aja ankavutitsidwa ndi akuluakulu a boma kuti aziwapatsa ndalama zina za ziphuphu.”

Ngati Bizinezi Sikuyenda Bwino

Ngati bizinezi sikuyenda bwino, ena amaganiza zoyamba kuchita zinthu mwachinyengo. Komabe, anthu amene amayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo, zinthu zimawayendera ngakhale pa nthawi yomwe chuma sichikuyenda bwino.

Mwachitsanzo, Bill yemwe kampani yake inagwa pa nthawi yomwe chuma sichinkayenda bwino ku United States, anati: “Makampani ambiri amene tinkachita nawo bizinezi anagwa ndipo zimenezi zinachititsanso kuti kampani yathu isamayende bwino. Pa nthawiyi makampaniwa n’kuti ali ndi ndalama zathu zankhaninkhani. Zinthu zitafika poipa kwambiri, ndinapita kukafunsira ntchito kukampani ina yomwe inkachita bizinezi yofanana ndi yathu. Titakambirana kwa masiku awiri, mabwana a kampaniyo anandilemba ntchito ineyo ndi anthu enanso ambiri amene  ankagwira ntchito pakampani yanga. Anandiuza kuti andilemba ntchito chifukwa chakuti ndili ndi mbiri yochita zinthu mwachilungamo.”

Anthu onse omwe tawatchula pamwambawa, ndi a Mboni za Yehova. Anthu amenewa amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pochita bizinezi komanso zinthu zina pa moyo wawo. Ndipo mukaganizira zimene afotokoza, mukhoza kuona kuti kuchita zinthu mwachilungamo kwawathandiza kwambiri.

Komabe, nthawi ndi nthawi mungakumane ndi zinthu zokuchititsani kuona ngati kuchita zachinyengo n’kothandiza. Koma kodi kupeza chuma chifukwa chochita zinthu zachinyengo kungakupangitseni kukhala ndi moyo wosangalala?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Kaya mukudziwa kapena ayi, kuchita zinthu mwachilungamo n’kothandiza kwambiri

[Chithunzi patsamba 7]

“Anandiuza kuti andilemba ntchito chifukwa chakuti ndili ndi mbiri yochita zinthu mwachilungamo”—Anatero Bill, wa ku United States