Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

 Kuchokera kwa Owerenga

Ndinasiya Ntchito ya Ndalama Zambiri (June 2010) Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi. Ndili ndi zaka 39 ndipo ndikulera ndekha ana atatu. Ndimakhala ku Russia ndipo m’dera lathu ntchito zimasowa, koma nkhani ya Martha Teresa Márquez inandithandiza kwambiri. Nkhaniyi inafotokoza kuti Martha amaphika samusa n’kumagulitsa n’cholinga choti azipeza ndalama zomuthandiza kupitirizabe kuchita upainiya. Nditawerenga nkhaniyi, ndinaganiza zoyamba kuphika tizakudya tinatake totchedwa piroshki. Bizinezi imeneyi yandithandiza kwambiri. Panopa banja lathu lonse limadalira bizineziyi. Chifukwa cha bizinezi imeneyi, ana anga akuphunzira ntchito zosiyanasiyana zimene zingadzawathandize m’tsogolo, komanso ayamba kuchita zinthu mwanzeru.

G. M., Russia

Kodi Mungatani Kuti Muchepetse Vuto Lochita Chibwibwi? (May 2010) Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani yanu. Nkhaniyi inali ndi mfundo zolondola kwambiri zokhudza chibwibwi. Bungwe lathu likuyesetsa kwambiri kudziwitsa anthu amene ali ndi chibwibwi kuti pali zinthu zambiri zimene angachite polimbana ndi vutoli.

J. F., Pulezidenti wa bungwe lina loona za anthu achibwibwi ku United States (The Stuttering Foundation)

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha? (December 2010) Ndakhala m’banja zaka 10 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Nthawi zonse ndimalimbana ndi “munga m’thupi.” Ndili ndi vuto lofuna kugonana ndi amuna anzanga. Ngakhale kuti ndinakwatira, koma vutoli silinathebe. Kunena zoona, ndinkakhumudwa kwambiri chifukwa choona kuti ndikulephera kuthana ndi vuto langali. Koma nkhaniyi inandilimbikitsa kwambiri kuti ndisataye mtima. Ngakhale kuti maganizo ofuna kugonana ndi amuna anzanga ndimakhala nawobe, ndimayesetsa kuti ndisachite zomwe ndikuganizazo.—2 Akorinto 12:7.

Sititchula dzina, United States

Ndinayamba kulimbana ndi vuto losirira amuna anzanga ndili ndi zaka zisanu zokha. Panopa ndili ndi zaka 61 ndipo vutoli lidakalipobe. Mfundo imene inandichititsa chidwi kwambiri mu nkhani yanu ndiyakuti anthu amene amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna anzawo kapena akazi anzawo akhoza kudziletsa ngati akufunadi kukondweretsa Mulungu. Munanena kuti pali anthu ambirimbiri amene amakhala ndi chilakolako chogonana ndi amuna kapena akazi anzawo, koma amayesetsa kupewa khalidweli. Ndinachitanso chidwi ndi mfundo yakuti “ena mwa anthu amenewa ndi osakwatira ndipo akusowa munthu womanga naye banja ndipo enanso ambiri ali m’banja koma mnzawoyo ali ndi vuto,” koma amatha kukhala mosangalala, ngakhale kuti pali mavuto amenewa. Choncho, ndikuyamikira kwambiri chifukwa chotilimbikitsa ife amene tikulimbana ndi vuto limeneli.

Sititchula dzina, United States