Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zinachitikira Kuti?

1. Kodi izi zinachitikira pafupi ndi mzinda uti?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 6:7-9; 7:54-60.

Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapu awa.

Damasiko

Yerusalemu

Betelehemu

2. Kodi Sitefano akugendedwa chifukwa chiyani?

․․․․․

3. Kodi Sitefano anapempha kuti Mulungu awachitire chiyani anthu amene amamugendawo?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi zimene Sitefano anachitira anthuwo mukuziona bwanji? Mukanakhala inuyo kodi mukanatani, ndipo n’chifukwa chiyani mukanachita zimenezo?

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU HEZEKIYA?

4. Kodi bambo ake a Hezekiya anali ndani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 18:1.

․․․․․

5. Ngakhale kuti bambo a Hezekiya anali oipa kwambiri, kodi Hezekiya anali ndi mbiri yotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 18:5.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi n’chiyani chinathandiza Hezekiya kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 18:6.

Ngati m’bale wanu atasiya kutumikira Mulungu, kodi mungatsanzire bwanji Hezekiya?

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 5 Kodi mmene thupi lathu limagwirira ntchito zimatsimikizira chiyani? Salmo 139:․․․

TSAMBA 8 Kodi mtendere wa Mulungu ungatichitire chiyani? Afilipi 4:․․․

TSAMBA 13 Kodi kupuma pang’ono kuli bwino kuposa chiyani? Mlaliki 4:․․․

TSAMBA 23 Kodi Mulungu amakonda munthu wotani? 2 Akorinto 9:․․․

● Mayankho ali patsamba 11

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Yerusalemu.

2. Sitefano akuimbidwa mlandu wochitira mwano Mulungu.

3. Mulungu awakhululukire.

4. Mfumu Ahazi.

5. Panalibenso mfumu ina kupatula iyeyu imene inali yodzipereka kwambiri pa kulambira koona.