Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupanikizika N’koopsa Kwambiri

Kupanikizika N’koopsa Kwambiri

Kupanikizika N’koopsa Kwambiri

“Ndimapanga anthu opaleshoni m’zipatala zosiyanasiyana ndipo nthawi zambiri ndimagwira ntchito usana ndi usiku. Ndikamachoka kuchipatala china kupita kuchipatala china, ndimapanikizika kwambiri chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto m’misewu.”—Anatero Dr. Peter Stuart, wa ku South Africa.

MUYENERA kuti mukumvetsa mmene Dr. Stuart amamvera ngakhale kuti mwina inuyo mumapanikizika ndi zinthu zosiyana kwambiri ndi zimenezi. Anthu amapanikizika ndi zinthu zosiyanasiyana monga kuyendetsa galimoto m’misewu yodzaza magalimoto, kusagwirizana ndi anthu ena kunyumba kapena kuntchito, ndi zinthu zina zambiri. Ndipo kupanikizika sikunayambe lero.

Zaka zoposa 3,000 zapitazo, msilikali wina wodziwa nkhondo ananena kuti: “Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta.” (Salmo 55:5) Aka sikanali koyamba kuti munthu ameneyu apanikizike. Ali mnyamata ku ubusa, analimbana ndi mkango, chimbalangondo ndiponso anamenyana ndi munthu wamphamvu kwambiri yemwe ankafuna kumupha.—1 Samueli 17:4-10, 23, 24, 34-36, 41-51.

Komabe, sikuti kupanikizika ndi koipa nthawi zonse. Nthawi zina kungatithandize kuti tichite bwino zinthu zinazake. Mwachitsanzo, anthu akakumana ndi zinthu zoopsa, amatha kuchita zinthu zodabwitsa zoti sakanatha kuchita akanakhala kuti sanapanikizike. Komanso ngati mwapatsidwa ntchito inayake yofunika kwambiri, nthawi zina mumaigwira bwino ntchitoyo ngati mukumva kuti mwapanikizika chifukwa nthawi imeneyi mumakhala ndi mphamvu zowonjezereka.

Koma vuto limakhalapo ngati munthu amangokhala wopanikizika komanso wotopa nthawi zonse. Munthu wina wochita kafukufuku anati: “Kupanikizika n’koopsa kwambiri chifukwa kumayambitsa matenda ambiri kuposa chinthu china chilichonse.” Ngati mumapanikizika, kodi n’chiyani chimene mungachite kuti musamapanikizike kwambiri?

Dziwani kuti malangizo othetsera vutoli alipo ndipo athandiza anthu ambiri. Malangizowa amapezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ngakhale kuti Baibulo si buku lonena zachipatala, malangizo ake ndi othandiza kwambiri. Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthu amapanikizika kwambiri masiku ano ndipo limatchula zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azipanikizika. Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuti tisamapanikizike kwambiri pamoyo wathu.