Tinapeza Zimene Tinkafuna
Tinapeza Zimene Tinkafuna
Yosimbidwa ndi Bert Tallman
Ndimakumbukira ndili kamnyamata m’dera la anthu otchedwa Blood, omwe ndi gulu la anthu a mtundu wa Blackfoot ku Alberta, Canada. Tinkakhala kufupi ndi mapiri a Rockies ku Canada ndiponso pafupi ndi nyanja yokongola ya Louise.
NDINABADWIRA m’banja la ana 9, ana amunafe 7 ndi aakazi awiri. Ineyo, azichimwene anga ndiponso alongo anga tinkakonda kukacheza kunyumba kwa agogo athu aakazi. Agogowa ankagwira ntchito mwakhama ndipo anatiphunzitsa chikhalidwe chamakolo cha anthu amtundu wathu wa Blackfoot. Tinaphunzira kuthyola zipatso, kuphika ndiponso kulima dimba. Agogo aamuna ndiponso bambo anga ankanditengera kokasaka ndiponso kopha nsomba. Tinkapha nyama zamtundu wa mphalapala kuti tipeze ndiwo ndiponso zikopa. Makolo athu anali olimbikira ntchito ndipo ankayesetsa kuti anafe tisamavutike. Moyo wanga m’dera limeneli unali wosangalatsa.
Agogo anga aakazi atamwalira mu 1963, zinthu zinasintha kwambiri. Panthawiyi n’kuti ndili ndi zaka zisanu ndipo kumwalira kwawo kunandikhudza. Zonse zomwe anthu ankanena sizinanditonthoze ngakhale pang’ono. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, ndinkadzifunsa kuti, ‘Ngati kuli Mlengi, kodi iye ali kuti? N’chifukwa chiyani anthufe timafa?’ Nthawi zina ndinkang’ung’udza chifukwa chokhumudwa. Mayi ndi bambo akafuna kudziwa kuti chalakwika n’chiyani, ndinkangowauza kuti mutu ukundipweteka.
Kukumana ndi Azungu
Agogo anga aakazi asanamwalire, sitinkakumana ndi azungu kawirikawiri. Nthawi zonse ndikaona mzungu, ndinkamva anthu akunena kuti: “Uyunso ndi woipa, wadyera ndiponso wopanda chifundo ngati azungu ena onse. Amenewa si anthu ayi.” Ndinachenjezedwa kuti ndi azungu ochepa okha amene ali abwino komanso azungu ndi anthu osadalirika. Ngakhale kuti ndinkachita chidwi ndikakumana nawo, ndinkakhala wosamala chifukwa azungu am’dera lathu ankatiseka ndi kutinyoza.
Agogo anga atangomwalira, bambo ndi mayi anayamba kumwa mowa kwambiri, ndipo zimenezi zinapangitsa nthawi imeneyi kukhala yovuta kwambiri pamoyo wanga. Ndili ndi zaka 8, anthu awiri a chipembedzo cha Mormon anayamba kumabwera kunyumba kwathu. Ankaoneka kuti anali anthu abwino. Mayi ndi bambo anavomera kuti anthuwo anditenge kuti ndizikakhala ndi azungu. Cholinga cha zimenezi, malinga ndi zimene ndinali kudziwa, chinali kusintha chikhalidwe cha ana a enidziko. Zikuoneka kuti chifukwa cha mavuto, mayi ndi bambo anaona kuti ndi bwino kuti ineyo ndizikakhala ndi banja lina. Ndinakhumudwa nazo kwambiri, chifukwa iwo ndi amene anandiuzanso kuti azunguwo ndi anthu osadalirika. Sindinafune kupita, ndipo ndinayesetsa kuzemba. Koma pamapeto pake ndinagwirizana nazo, mayi ndi bambo atandiuza kuti ndipita limodzi ndi mchimwene wanga wamkulu.
Komabe, titafika ku Vancouver, British Columbia, ine ndi mchimwene wanga anatisiyanitsa,
ndipo ine anandipititsa kutali pafupifupi makilomita 100. Zimenezi zinandipweteka kwambiri. Ngakhale kuti banja limene ndinkakhala nalo linali labwino, zinali zovuta kwambiri ndipo ndinkachita mantha. Ndinabwerera kwathu patadutsa miyezi pafupifupi 10.Nditabwerera Kunyumba
Ndinali wosangalala kubwerera kunyumba ngakhale kuti zinthu kunyumbako sizinali bwino kwenikweni. Nditakwanitsa pafupifupi zaka 12, mayi ndi bambo anasiya kumwa mowa. Zimenezi zinali zabwino, koma panthawiyi n’kuti ndikukhala moyo wotayirira, chifukwa ndinali nditayamba mankhwala osokoneza bongo ndiponso kumwa mowa. Mayi ndi bambo anandilimbikitsa kuchita zinthu zina, monga masewera okwera pa ng’ombe zolusa amene ndinkawakonda. Masewera amenewa ankafuna amunamuna. Ndinaphunzira kukwera pamsana pa ng’ombe zolusa zomwe zimakonda kuponda anthu. Ndinkakhala pamsana pa ng’ombe masekondi osachepera 8 osagwa kwinaku nditagwira ndi dzanja limodzi chingwe chimene amachimanga pamimba pa ng’ombeyo.
Nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 15, akuluakulu apamudzi anandiyambitsa chipembedzo chamakolo. Ndinachikonda kwambiri chifukwa sindinkalemekeza zipembedzo za azungu. Ndinkaona kuti miyambo ya mtundu wa Blackfoot inkalimbikitsa kukoma mtima ndi chilungamo, zomwe sizinkapezeka m’zipembedzo zambiri zachikhristu. Ndinkasangalala kukhala ndi anthu amtundu wathu, kukambirana nkhani zoseketsa ndiponso kuona kugwirizana kwa mabanja ndi mabwenzi athu.
Panthawiyi, ndinadziwanso kuti kwa zaka zambiri m’mbuyomo, anthu amtundu wathu anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Ndinauzidwa kuti azungu anatibweretsera matenda ndipo anapha njati zonse zomwe tinkadalira pamoyo wathu. Ndiponso, akuti mkulu wa asilikali a dziko la United States, Colonel R. I. Dodge, ananena kuti: “Iphani njati zonse. Mukapha njati imodzi, ndiye kuti mmwenye mmodzi wapita.” Ndinauzidwa kuti maganizo amenewa anaziziritsa nkhongono anthu amtundu wathu wa Blackfoot ndipo ankadziona kuti alibe kolowera.
Komanso akuluakulu ena aboma ndi anzawo achipembedzo anali atayesetsa kwambiri kusintha anthu amtundu wathu, omwe ankawaona kuti ndi mbuli zokhazokha. Iwo ankakhulupirira kuti anthuwa anafunika kusintha chilichonse monga chikhalidwe, zikhulupiriro, zochita ndi chinenero chawo, kuti atengere za azungu. Ku Canada, ana ena amtundu wathu ankachitiridwa nkhanza kusukulu zogonera komweko zoyang’aniridwa ndi tchalitchi. Ena anayamba mankhwala osokoneza bongo, mowa, chiwawa, ndiponso kudzipha. Ndipo mavuto amenewa adakalipobe m’midzi ina mpaka pano.
Pothawa mavuto amenewa, anthu ena amtundu wathu anasiya chikhalidwe cha Blackfoot. Iwo anayamba kulankhula Chingelezi kwa ana awo, m’malo mwa chinenero cha mtundu wathu wa Blackfoot, ndipo anayesetsa kutengera chikhalidwe cha azungu. Ngakhale anachita zimenezi, sizinawathandize chifukwa ankanyozedwa ndi azungu. Komanso ankanyozedwa ndi anthu ena amtundu wathu, powatchula kuti “amwenye okhala ngati maapulo,” ofiira kunja koma oyera mkati.
Zinali zokhumudwitsa kuona anthu amtundu wathu akuvutika m’njira zambiri. Ndinkafunitsitsa kuona zinthu zitasintha m’dera lomwe ndinkakhala ndi m’madera ena ku Canada ndi United States.
Ndinkafunafuna Mayankho
Nditapitirira zaka 15, ndinkaganiza kuti anthu sadzasiya kundisala. Nthawi zina maganizo anga odziona ngati wotsika ankandichititsa kuipidwa ndi zinthu. Ndipo ndinayamba kudana ndi azungu. Koma mayi ndi bambo komanso azakhali anandichenjeza kuti si bwino kusunga chidani ndi kufuna kubwezera. M’malo mwake, anandilimbikitsa kukhululukira ena ndi kuwakonda ndiponso kusalabadira za anthu atsankho. M’kupita kwa nthawi, ndinapeza kuti malangizo amenewa ndi ogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Kuwonjezera pamenepo, ndinkafunabe kupeza mayankho a mafunso amene ankandivutitsa kuyambira ndili mwana. Ndinayamba kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani tili padzikoli ndipo n’chifukwa chiyani kupanda chilungamo kukupitirirabe?’ Sindinkamvetsa chifukwa chimene timakhalira ndi
moyo nthawi yochepa kenako n’kumwalira. Ndinathedwa nzeru.A Mboni za Yehova akagogoda kunyumba kwathu, ndinkatumidwa kukawatsegulira. Nthawi zonse ndinkawalemekeza chifukwa ankaoneka kuti alibe tsankho. Ngakhale kuti ndinkavutika kuwafunsa mafunso anga bwinobwino, tinali kukambirana mfundo zosangalatsa. Ndimakumbukirabe tsiku limene John Brewster ndi Harry Callihoo, Mboni yamtundu wathu wa Blackfoot, anabwera kunyumba kwathu. Tinakambirana kwa nthawi yaitali tikuyenda m’dambo. Iwo anandipatsa buku ndipo ndinaliwerenga mpaka kufika pakatikati kenako linandisokonekera.
Ndinayamba Mipikisano Yokwera pa Ng’ombe Zolusa
Ndinapempha nzeru kwa anthu achikulire apamudzi pathu. Ngakhale kuti ndinayamikira malangizo awo, iwo sanandiyankhe mogwira mtima mafunso anga okhudza moyo. Ndili ndi zaka pafupifupi 16, ndinachoka panyumba ndipo ndinalowerera kwambiri m’mipikisano ya masewera okwera pa ng’ombe zolusa. Tikamaliza masewerawa, tinkachita mapwando komwe nthawi zambiri tinali kumwa mopitirira muyeso ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Chikumbumtima changa chinkandipweteka kwambiri chifukwa ndinkadziwa kuti khalidwe loterolo linali lolakwika ndipo Mulungu sankasangalala ndi moyo wanga. Nthawi zambiri ndinali kupemphera kwa Mlengi kuti andithandize kuchita zabwino ndi kupeza mayankho a mafunso amene ankandivutitsa aja.
Mu 1978, ndili ku Calgary, ndinadziwana ndi Rose. Mmodzi wa makolo ake anali wamtundu wathu wa Blackfoot ndipo wina anali wa mtundu wa Cree. Tinkakonda zinthu zofanana, ndipo tinkalankhulana momasuka. Tinayamba chibwenzi ndipo kenako tinakwatirana mu 1979. Banja lathu linakula chifukwa tinakhala ndi mwana wamkazi, Carma, ndi wamwamuna, Jared. Rose wakhala mkazi wokhulupirika ndi wothandiza komanso mayi wodziwa bwino kulera ana. Tsiku lina pamene ine ndi banja langa tinapita kukaona mchimwene wanga wamkulu, ndinapeza buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Zimene ndinawerenga zinandipatsa chidwi ndipo zinali zogwira mtima. Koma nditangoyamba kumvetsa uthenga wa m’Baibulo, ndinafika pa mbali imene masamba ena a bukulo panalibe. Ine ndi Rose tinayesetsa kufunafuna masambawo, koma sitinawapeze. Ngakhale zinali choncho, sindinasiye kupemphera.
Tinapita kwa Wansembe
Mu 1984, Rose anabereka mwana wathu wachitatu wamkazi, dzina lake Kayla. Anali mwana wokongola. Koma patangodutsa miyezi iwiri yokha, Kayla anamwalira ndi matenda obadwa nawo a mtima. Tinali ndi chisoni chachikulu, ndipo sindinadziwe mmene ndingamutonthozere Rose. Iye anandilimbikitsa kuti tipite kwa wansembe wa Katolika wa m’mudzi mwathu kuti akatilimbikitse ndi kutiyankha mafunso athu.
Tinamufunsa kuti atiuze chifukwa chake mwana wathu anamwalira ndi kumene anapita. Iye anatiuza kuti Mulungu wamutenga Kayla chifukwa anafuna kuti akakhale mngelo. Ndinadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu watenga mwana wathu kuti akhale mngelo ngati iye ali Mlengi Wamphamvuyonse? Mwana wamng’ono ngati amene uja angakachite chiyani?’ Wansembeyo sanatsegule Baibulo ngakhale pang’ono. Tinachoka kumeneko tili okhumudwa.
Pemphero Linatithandiza Kwambiri
Tsiku lina, Lolemba m’mawa chakumapeto kwa November 1984, ndinapemphera kwa nthawi yaitali, kuchonderera Mulungu kuti andithandize kukhala munthu wabwino. Ndiponso ndinapempha kuti andithandize kumvetsa zimene zinali kuchitika komanso cholinga cha moyo. M’mawa womwewo, Diana Bellemy ndi Karen Scott, anagogoda pakhomo pathu. Anthu amenewa anali a Mboni za Yehova. Iwo anali anthu abwino kwambiri ndipo anali osangalala kundiuza uthenga umene anali nawo. Ndinamvetsera ndipo anandipatsa Baibulo ndi buku lakuti Kupulumuka Kulowa m’Dziko Lapansi Latsopano. * Kenako tinagwirizana kuti Diana abwere ndi mwamuna wake Darryl mlungu womwewo.
Iwo atachoka, ndinazindikira kuti zimene zinachitikazo ndi yankho la pemphero langa. Ndinasangalala kwambiri mwakuti ndinalephera kukhala pansi, ndipo ndinkangozungulirazungulira
m’nyumbamo, kudikirira kuti Rose abwere kuntchito ndidzamuuze zimene zinachitikazo. Ndinadabwa kumva Rose akundiuza kuti iyenso anali kupemphera usiku wonse, ndipo anali kupempha Mulungu kuti amuthandize kupeza chipembedzo choona. Lachisanu mlungu womwewo, tinayamba kuphunzira Baibulo. Kenako tinauzidwa kuti tsiku loyamba limene Karen ndi Diana anafika panyumba pathu, anali kufunafuna nyumba zina zimene anakonza kuti akalalikireko koma sanazipeze. Ndiyeno ataona nyumba yathu, zinawavuta mumtima kuti angobwerera osatilalikira.Pamapeto Pake Ndinapeza Mayankho
Achibale ndi mabwenzi athu anadabwa titayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kutida. Pofuna kuti tisiye, iwo ankatiuza kuti tikuwononga moyo wathu ndipo sitikugwiritsa ntchito bwino nzeru ndi luso lathu. Koma ife sitinafune kusiyana ndi Bwenzi lathu latsopano, Mlengi wathu Yehova. Chinanso, tinali titapeza chuma chamtengo wapatali, chimene ndi mfundo zosowa za choonadi ndi zinsinsi zopatulika zimene zili m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Mateyo 13:52) Ine ndi Rose tinabatizidwa kukhala Mboni za Yehova mu December 1985. Tsopano achibale athu amalemekeza kwambiri Mboni za Yehova, chifukwa aona moyo wathu mmene wasinthira kuyambira pamene tinabatizidwa.
Inde, ndinapeza zimene ndinkafuna. Baibulo limayankha mafunso ofunika kwambiri mosavuta komanso molondola. Ndinasangalala nditadziwa cholinga cha moyo, chifukwa chake timafa komanso lonjezo la Mulungu lakuti n’zotheka kukumananso ndi mwana wathu Kayla, n’kumuona akukula m’dziko lamtendere. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:4) Patapita nthawi, ndinamvetsanso kuti sitiyenera kuchitira nkhanza thupi lathu, kusalemekeza moyo, kapena kulimbikitsa mpikisano. (Agalatiya 5:26) Pofuna kusangalatsa Mulungu, ndinasiya masewera okwera pa ng’ombe zolusa ngakhale kuti zinali zovuta kuchita zimenezo.
Kudziwa Baibulo molondola kwatimasula ku zikhulupiriro zimene anthu ambiri amtundu wathu amavutika nazo, monga zakuti kadzidzi akabwera panyumba kapena galu akamalira, ndiye kuti pabanjapo wina afa. Sitiopanso kuti mizimu imene amati ili m’zamoyo kapena zopanda moyo ingativulaze. (Salmo 56:4; Yohane 8:32) Tsopano timachita chidwi ndi zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga. Ndili ndi mabwenzi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana amene ndimawatchula kuti abale ndi alongo, ndipo iwo amandiona kuti ndine wofanana nawo komanso mtumiki mnzawo wa Mulungu. (Machitidwe 10:34, 35) Ambiri a iwo akuyesetsa kuphunzira chikhalidwe, miyambo ndi chinenero cha mtundu wathu wa Blackfoot kuti azitha kulalikira uthenga wa m’Baibulo mogwira mtima.
Banja lathu limakhala m’dera la anthu otchedwa Blood, kum’mwera kwa Alberta, kumene tili ndi famu yaing’ono ya ziweto. Timakondabe chikhalidwe chathu, kuphatikizapo chakudya, nyimbo ndi magule amakolo athu. Ifeyo sitivina nawo magulewo, amene amatchedwanso kuti powwow, koma nthawi zina timangoonerera. Ana anganso ndinawaphunzitsa chikhalidwe chathu ndiponso mawu ena ndi ena a chinenero cha mtundu wathu wa Blackfoot. Anthu ambiri amtundu wathu amadziwika ndi makhalidwe abwino monga kukoma mtima, kudzichepetsa ndi kukonda achibale komanso mabwenzi. Amadziwikanso ndi kuchereza alendo ndiponso kulemekeza anthu ena, kuphatikizapo anthu amitundu ina. Ndimasangalalabe ndi makhalidwe amenewa.
Timasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito nthawi ndi chuma chathu pothandiza ena kuphunzira za Yehova ndiponso kumukonda. Mwana wathu, Jared, amagwira ntchito yongodzipereka paofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kufupi ndi mzinda wa Toronto. Ndine mkulu mumpingo wakwathu wa Macleod ndiponso ine, Rose ndi Carma ndife apainiya okhazikika, kapena kuti alaliki anthawi zonse. Timasangalala kwambiri kulalikira m’chilankhulo chathu. N’zosangalatsa kuona anthu akulabadira choonadi chonena za Mlengi ndi zolinga zake.
Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Ukamufunafuna Iye udzamupeza.” (1 Mbiri 28:9) Ndikuthokoza kwambiri kuti iye wakwaniritsa lonjezo lake chifukwa wathandiza ine ndi banja langa kupeza zimene tinkafuna.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 22 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Panopa anasiya kulisindikiza.
^ ndime 27 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Panopa anasiya kulisindikiza.
[Mawu Otsindika patsamba 13]
‘Ngati kuli Mlengi, kodi iye ali kuti? N’chifukwa chiyani anthufe timafa?’
[Mawu Otsindika patsamba 16]
‘Anthu ambiri amtundu wathu amadziwika ndi makhalidwe monga kukoma mtima ndi kudzichepetsa’
[Chithunzi patsamba 12]
Agogo anga aakazi anandiphunzitsa chikhalidwe cha mtundu wathu wa Blackfoot
[Chithunzi patsamba 15]
Ndinalowerera kwambiri m’masewera okwera pa ng’ombe zolusa
[Chithunzi patsamba 15]
Kapepala kapadera kakuti “You Can Trust the Creator” kamene kali m’chinenero chathu ndi m’zinenero zina
[Chithunzi patsamba 15]
Tsopano ndimasangalala kuphunzitsa ena Baibulo
[Chithunzi patsamba 15]
Ine ndi banja langa panopa