Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwana wa Nyani Atalira Momvetsa Chisoni

Mwana wa Nyani Atalira Momvetsa Chisoni

Mwana wa Nyani Atalira Momvetsa Chisoni

YOLEMBEDWA KU CAMEROON

Pitchou ndi nyani wamkazi ndipo anabadwira ku nkhalango ina pakati pa Africa. Pamene Pitchou anali ndi chaka chimodzi, alenje anapha mayi ake ndi anyani ena amtundu wake wa gorila kuti apeze ndiwo. Koma Pitchou anapulumuka chifukwa chakuti anali wamng’ono kwambiri, choncho anangom’sunga kuti akagulitse kwa anthu ofuna kuweta. Kenako Pitchou anayamba kudwala ndipo ankangokhalira kulira.

PITCHOU ndi chitsanzo chimodzi chabe cha anyani ambirimbiri amene ndi amasiye. Pali zinthu zambiri zimene zachititsa vutoli. Choyamba ndi kuchita malonda oletsedwa a nyama yam’tchire. Poona kuti m’malesitilanti ndiponso anthu ena amakonda kwambiri nyama yam’tchire, alenje amasaka nyama usana ndi usiku m’nkhalango kuti apeze ndalama zambiri. Kwinaku anthu ena amene amagula nyama kwa alenjewa, amapeza misika yosaloleka koma yotentha m’dziko lawo ndi kumayiko ena kumene amakagulitsa anyani amoyo komanso nyama yawo.

Chinthu chachiwiri ndi kudula mitengo mwachisawawa. Nkhalango zikawonongedwa, nyama zimasowa malo okhala, malo obisala, malo odyera komanso malo oberekera ndi kulerera ana. Zinthu ziwiri zomwe tatchulazi zimayendera limodzi. Tikutero chifukwa chakuti mwa zina, misewu yomwe imapangidwa ndi anthu odula mitengo imathandiza alenje kuti azilowa m’nkhalango mosavuta. Mmenemo iwo amapha mosavuta nyama chifukwa zimakhala zitasokonezeka ndiponso zopanda malo obisala. Zinthu zinanso zimene zawonjezera vutoli ndi monga kuchulukana kwa anthu, kusowa kwa zakudya zomanga thupi, kuwonjezereka kwa mizinda, njira zamakono zophera nyama, komanso nkhondo ndiponso kupezeka kwa mfuti chisawawa. Chifukwa cha zimenezi, anyani ndi mitundu ina ya nyama zam’tchire, atsala pang’ono kutha, ndipo izi zikuchititsa vuto la nkhalango zopanda nyama. Koma tisaganize kuti vuto ndi lokhali. Tikutero chifukwa chiyani? Nyama zimamwaza mbewu zimene zimathandiza kuti nkhalango zikhale ndi zomera zosiyanasiyana komanso zathanzi. Choncho nyama zikatha, zomera zimakhalanso pa mavuto.

Ngakhale kuti kupha nyama kukuyambitsa mavuto ngati amenewa, anthu sakusiya. M’madera ena ku West Africa pa zaka 10 zokha, chiwerengero cha anyani ena chinatsika ndi 90 peresenti. Akatswiri a nyama zakutchire ku Cameroon akuti: “Ngati mchitidwe wopha nyama popanda chilolezo upitirira, ndiye kuti posachedwapa anyani amtundu wa gorila adzatheratu m’nkhalango.” *

Kupulumutsa Ana Amasiye

Chifukwa cha vutoli, mabungwe oteteza zachilengedwe, monga la Limbe Wildlife Centre, lomwe lili m’mphepete mwa phiri la Cameroon ku West Africa cha kum’mwera kwa Sahara, amateteza nyama zimene zatsala pang’ono kutha. Ku Limbeko, alendo amaona anyani amitundu yosiyanasiyana monga gorila, chimpanzi, mandrill, ndi mitundu ina 13 komanso nyama zina. Pa zaka zingapo zapitazi, nyama zamasiye ndi zosowa pokhala pafupifupi 200 zasamaliridwa kumalowa mwa kuzipatsa malo otetezeka, chakudya ndi mankhwala. Chinthu chinanso chimene amachita ku Limbe ndicho kuphunzitsa anthu amene amabwera ku malowa kuchokera ku Cameroon komweko, mayiko apafupi ndi mayiko ena akutali, za kufunika koteteza nyama. M’chaka china posachedwapa, kunabwera alendo oposa 28,300.

Tsopano tiyeni tipitenso kwa Pitchou. Pokhudzidwa ndi kulira komvetsa chisoni kwa mwana wa nyaniyu, anthu oona anamugula kwa alenjewo ndi kumupititsa ku Limbe. Kanyanika katafika kumeneko, anakayeza bwinobwino m’chipatala chawo. Kuwonjezera pa kuvutika maganizo, kanyanika anakapeza ndi chifuwa, kuchepa kwa madzi m’thupi, kupewera kwa zakudya m’thupi, kutsegula m’mimba, ndi matenda apakhungu. Chifukwa cha matenda apakhunguwa, kanyanika anakapatsa dzina lakuti Pitchou, limene m’chilankhulo chakomweko limatanthauza “wamawangamawanga.” Zosangalatsa n’zakuti mankhwala amene Pitchou anapatsidwa anamuthandiza ndipo sanafunikire opaleshoni, imene amatha kupanga pa chipatala chawocho.

Monga mmene amachitira ndi nyama zomwe zabwera ku malowa, Pitchou atangofika anamusunga kwayekha masiku 90. Kenako anamutulutsa n’kukamuika limodzi ndi anyani anzake 11 mumpanda, mosasiyana ndi kutchire. Anthu ogwira ntchito pamalowa anasangalala kwambiri ataona kuti anyani enawo amulandira bwino mnzawo watsopanoyo. Zimenezi si zachilendo, ndipo posapita nthawi Pitchou anazolowerana ndi anzakewo.

Chifukwa cha mgwirizano ndi ubwenzi umene umakhalapo pakati pa nyamazi ndi anthu ozisamalira, anthuwo ndi nyamazo amakondana kwambiri. Kuona zimene zimachitika pamalowa kungathandize mlendo kumvetsa udindo umene Mulungu anapatsa anthu, pamene anauza banja loyamba kuti liziyang’anira dziko lapansi ndi nyama.—Genesis 1:28.

Kodi Ana Amasiyewa Ali ndi Tsogolo Lotani?

Cholinga chachikulu cha bungweli ndi kubwezera nyamazo m’nkhalango. Koma zimenezi zili ndi mavuto ake. Nyama zomwe zazolowera kusamalidwa ndi anthu zimavutika kuti zikhale zokha. Ndiponso zingakhale pa ngozi yokhala ndiwo kwa anthu ena. Mayiko ambiri a mu Africa agwirizana kuti akhazikitse malo otetezedwa m’malire a mayikowo ndiponso kukhwimitsa chitetezo cha malo omwe alipo kale. Mwina dongosolo limeneli lidzathandiza kuti nyama zamasiye zibwerere ku nkhalango mwamsanga ndi kuthandizanso kuteteza osati anyani okha komanso nyama zonse zam’tchire m’derali.

Pakali pano, zikuoneka kuti zinthu zimene zikuwonjezera vutoli monga dyera, umphawi, kuchulukana kwa anthu, ndiponso kudula mitengo mwachisawawa, zipitirirabe kuphetsa anyani ndi nyama zina. Mkulu wa bungwe la Limbe Wildlife Centre, Felix Lankester, ananena kuti ngati sitichitapo kanthu mwamsanga kukhwimitsa chitetezo, “mitundu ina ya nyama zakutchire idzatheratu. Zotsatira zake . . . zingakhale zakuti nyama zomwe tikuzisamalirazi sizidzapezekanso m’nkhalango.”

Zimenezi ndi zomvetsa chisoni. Koma chomvetsa chisoni kwambiri ndicho kuona anthu akuvutika ndi njala ndiponso matenda, komanso kuona ana otupa mimba, misozi ili m’maso, akufa chifukwa chosowa chakudya. Tsoka la Pitchou likusonyeza mmene zinthu zaipira padzikoli, makamaka kukondera ndi kupanda chilungamo.

Koma chosangalatsa n’chakuti Mlengi wathu akudziwa zimene zikuchitika padziko lapansi. Posachedwapa iye adzathetsa zonse zimene zimachititsa nkhanza, kuvutika, ndi kutha kwa zachilengedwe ndipo adzakhazikitsa mtendere pakati pa zamoyo zonse.—Yesaya 11:6-9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Akatswiri a zaumoyo amachenjeza kuti kugwira ndi kudya nyama zam’tchire kungathenso kufalitsa matenda oopsa kwambiri monga anthrax ndi Ebola, ndi tizilombo tina tofanana ndi kachilombo ka HIV, kuchoka ku nyama kupita kwa anthu.

[Chithunzi pamasamba 23, 23]

Pitchou akudwala ndiponso atachira

[Chithunzi patsamba 23]

Nyani wotchedwa “guenon” wamakutu ofiira

[Chithunzi patsamba 23]

Nyani wotchedwa “drill” akusamalira mwana wake

[Chithunzi patsamba 24]

Polowera ku Limbe Wildlife Centre

[Chithunzi patsamba 24]

Akusamalira Bolo, mwana wamasiye wa gorila

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

All photos pages 22 and 23: Limbe Wildlife Centre, Cameroon

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Both photos: Limbe Wildlife Centre, Cameroon