Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Mu 2007, anthu a ku China pafupifupi 47 miliyoni anasowa madzi akumwa chifukwa cha chilala choopsa kwambiri chomwe sichinachitikepo pazaka 10 m’mbuyomu. Komanso anthu 42 miliyoni anakhudzidwa ndi chimphepo, ndipo anthu 180 miliyoni anakhudzidwa ndi madzi osefukira.—XINHUA NEWS AGENCY, CHINA.

“Mu 2003, pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse okhala ndi pathupi padziko lonse anachotsa mimba. Ku Ulaya, chiwerengero cha ochotsa mimba chinali munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse . . . M’mayiko omwe kale anali Soviet Union, . . . pafupifupi anthu 45 pa 100 alionse anachotsa mimba mu 2003.”—BRITISH MEDICAL JOURNAL, BRITAIN.

Masewera Achiwawa Apavidiyo M’tchalitchi

Nyuzipepala ya The New York Times inati: “Abusa ndi mapasitala ambiri adzudzulidwa chifukwa cha njira imene akugwiritsa ntchito pokopa achinyamata kuti azibwera m’mipingo yawo.” Iwo akugwiritsa ntchito “masewera achiwawa apavidiyo” omwe ndi “otchuka kwambiri.” Masewerawa anapangira anthu achikulire. Wosewera amayerekezera kukhala msilikali ndipo amafunika kupha adani ake pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Ngakhale zili choncho, nyuzipepalayi ikuti mabungwe a achinyamata achipolotesitanti ndi mipingo ina akupitirizabe “kudzaza matchalitchi awo ndi makina ambirimbiri okhala ndi ma TV akuluakulu kuti achinyamata azikhamukirako kukachita masewera oomberanawo.”

Kuba M’dzina la Ana

Ana ambiri akukumana ndi vutoli, ndipo zimenezi zikuwaphera mwayi wodzapeza ngongole m’tsogolo ndiponso kuwononga chibale, inatero nyuzipepala ya The Wall Street Journal. Nthawi zambiri anthu amene amaba m’njira imeneyi amakhala achibale awo ndipo pangapite zaka zambiri asanadziwike. Nyuzipepalayi inati: “Anthu ambiri sadziwa kuti munthu wina akugwiritsa ntchito dzina lawo mwachinyengo . . . mpaka pamene iwo ayamba kufunsira ntchito, laisensi yoyendetsera galimoto, ngongole zolipirira sukulu kapena kugulira nyumba.” Ena amadziwa msanga pamene bungwe lopereka ngongole lifuna kuti abweze ngongole imene yaunjikana m’dzina lawo.

Sanadziwe Kuti Atenga Zida Zanyukiliya

Pa August 30, 2007, ndege yankhondo yamtundu wa B-52 ya ku United States inauluka m’dzikoli kwa maola atatu ndi theka itanyamula mabomba anyukiliya 6, amene “anawamangirira mosadziwa ku mapiko a ndegeyo,” inatero nyuzipepala ya The Washington Post. Nyuzipepalayi inanena kuti oyendetsa ndegeyo komanso anthu ogwira ntchito kubwalo la ndege la asilikali amene anamangirira mabombawo, sanadziwe kuti alakwitsa “mpaka patadutsa maola 36.” Malipoti akuti: “Akuluakulu a asilikali a mu mlengalenga anati mabombawo anali osatchera ndipo sakanabweretsa ngozi iliyonse kwa anthu.” Komabe, munthu wina anati: “Ngakhale zili choncho, zimenezi ndi zodetsa nkhawa kwambiri.”

Nkhunda Zimayeza Kuwonongeka kwa Mpweya

Akatswiri a pa Yunivesite ya Rajasthan kumpoto kwa India, ananena kuti kafukufuku amene anachita ku mzinda wa Jaipur wasonyeza kuti nkhunda zingagwiritsidwe ntchito kuyeza kuwonongeka kwa mpweya m’mizinda. Gobar Times ya ku New Delhi, yomwe imaikidwa mkati mwa magazini ya Down to Earth, inanena kuti: “Fumbi la zitsulo lopezeka m’mizinda yomwe kuli nkhundazi, limalowa mu nthenga zake ndipo limakhalabe [mu nthengazo] ngakhale zitathothoka.” Popeza kuti nkhunda zimakonda kukhala malo amodzi, kuchuluka kwa fumbi la zitsulo monga cadmium, chromium, mkuwa ndi mtovu mu nthenga zawo, kungakhale chizindikiro cha mmene mpweya wawonongekera m’deralo.