Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wokaona Nkhosa Zam’tchire

Ulendo Wokaona Nkhosa Zam’tchire

Ulendo Wokaona Nkhosa Zam’tchire

M’mawa wina kunja kutacha bwino m’mwezi wa May, tinatenga mapu, makamera, zipewa, ndi nsapato zokhuthala ndipo tinakwera m’galimoto yathu yotha kuyenda m’misewu yoipa. Ulendowu tinkapita ku nkhalango ya Paphos, mu mdadada wa mapiri otchedwa Troodos ku Cyprus, kumene tinkafuna kukaona nkhosa zam’tchire, zomwe sizioneka wambawamba. Kodi nyama zimenezi ndi zotani?

NKHOSA zam’tchire zilipo zamitundumitundu, ndipo zimapezeka m’chigawo chonse chozungulira nyanja yamchere ya Mediterranean. Mtundu wa nkhosa zam’tchire zimene tinkafuna kukaona n’za ku Cyprus ndipo akuti n’zokongola ngati mphalapala, komanso ndi zopepuka thupi ngati mbuzi. Zimapezeka m’mapiri mokhamokha.

Tinachoka mu msewu waukulu n’kukhotera njira ya m’mphepete mwa mapiri kenaka tinayenda m’chigwa chokongola. M’mphepete mwa mapiriwo muli midzi, ndipo m’chigwamo anabzalamo zipatso zosiyanasiyana. Koma posakhalitsa tinafika mu msewu woipa ndipo m’malo ena galimoto yathu inkachita kupendekekera kuphedi. Kenako tinafika kumene tinali kupita, ku ofesi ya oyang’anira nkhalango. Tsopano tinali m’kati mwa nkhalango ya Paphos, yaikulu maekala 150,000, yomwe ili ndi mitengo ya paini ndi ya mkungudza. Tinaitanitsa khofi n’kumacheza ndi woyang’anira nkhalango wina amene anali atavala yunifolomu yobiriwira dzina lake Andreas, ndipo anali wosangalala kutifotokozera za nkhosa zam’tchirezi.

Iye anati nkhosa yam’tchire ndi nyama yaikulu kwambiri pa nyama zonse zam’tchire za ku Cyprus zoyamwitsa ana. Kale, nkhosazi zinalipo zambirimbiri pachilumbachi. Zithunzi zambiri zomwe Agiriki ndi Aroma ankakongoletsera nyumba zawo zinkakhala za nkhosa zam’tchirezi, ndipo zolembedwa zakale kwambiri zimafotokoza momwe anthu apamwamba ankakondera kusaka nyama zimenezi m’nkhalango ya Paphos.

Pamene Andreas anali kutilondolera ku malo enaake otchingidwa ndi mpanda, anatiuza zinthu zina zokhudza mbiri ya nkhosa zam’tchirezi. Mwachitsanzo, anatiuza kuti chiwerengero cha nkhosa zam’tchirezi chinachepa kwambiri alenje atayamba kugwiritsa ntchito mfuti posaka. Mu 1938 m’pamene malamulo osakira nyama ku Cyprus anawasintha kuti aziteteza nkhosazi. Anthu oyang’anira nkhalango ndi apolisi anagwira ntchito limodzi kuti athetse kupha nyama mopanda chilolezo. Patapita chaka, analetsa kusaka nyama m’nkhalangomu. Malamulo amenewa, limodzi ndi ena amene anakhazikitsidwa m’ma 1960, athandiza kuti chiwerengero cha nkhosa zam’tchire chiwonjezeke.

Nyama Zoyambirira Kuziona

Tinamutsatira Andreas pa malo ena otchingidwa ndi mpanda ndipo tinasunzumira kupyola maudzu ndi mitengo. Andreas anatiuza ndi manja kuti tikhale chete ndipo tinayenda naye pang’ono kukwera kamtunda. Pamwambapo tinaona nkhosa zazikazi zitatu ndi ana awiri akudya udzu pamalo owala bwino a udzu ufupiufupi. Nkhosa zazikuluzo zinali zotalika pafupifupi masentimita 90, ndipo zinali ndi ubweya wabulawuni, ndi kumimba kotuwa.

Zitsamba zimene zinkadyazo zimapezeka zambiri m’nyengo imeneyi, ndipo nkhosa zikuluzikuluzo zinali zotanganidwa n’kudya moti sizinatilabadire n’komwe. Koma anawo anasiya kusewera n’kuyamba kutitsatira koma mokayikira. Tinasangalala kwambiri kuona zimenezi. Koma atangomva kukhethemula kwa kamera yathu imodzi, anadzidzimuka ndipo nthawi yomweyo gulu lonselo linathawa kulowa m’nkhalangomo.

Posangalala ndi zomwe tinaonazo, tinakonza zoti tidzayende pansi m’nkhalangomo kuti mwina tidzaone nkhosazi zili m’tchire. Andreas anatiuza kuti mwina tidzapite mbandakucha, nthawi imene nyamazo nthawi zina zimapita m’mphepete mwa nkhalangoyi pofuna chakudya. Popeza tinakonza zoti tigone m’matenti m’chigwamo, phiri lomwe linayang’anizana ndi chigwacho mwina likanakhala malo abwino kufunamo nyamazo. Anatiuza kuti nkhosa zam’tchire zimapita m’malo okwera a m’phiri m’miyezi yotentha, koma mu nthawi yozizira, pamwamba pa mapiri pakakhala pokutidwa ndi chipale chofewa, zimafunafuna zitsamba m’munsi, ndipo nthawi zina zimatuluka m’nkhalangoyo.

Nyama zazimuna ndi zazikazi zimakwerana miyezi yotentha ikadutsa. Mu nthawi yozizira, nkhosa zam’tchire zimayendera limodzi m’magulu okhala ndi nyama 10 mpaka 20. Nkhosa zikayamba kubereka ana mu April ndi May, zimapatukana n’kukhala m’magulu ang’onoang’ono, ngati gulu limene tinaona m’malo otchingidwa aja. Nkhosa zamphongo nthawi zambiri zimadya zili zokha.

Tinakumana ndi Nkhosa Yamphongo M’tchire!

M’mawa kwambiri tsiku lotsatira, tinakwera galimoto kulowera m’phiri, ndipo tinaiimika penapake pathyathyathya pokhala udzu ufupiufupi. Kenako tinayenda kulowa m’nkhalangomo dzuwa lisanakwere kwambiri. Mu nkhalangomo munali zii, ndipo pakati pa mitengoyo panali nkhungu. Titaima kuti tisangalale ndi batalo, tinaona nkhosa imodzi. Inali yamphongo, yaikulu ndiponso yamphamvu, ndipo ubweya wambiri umene inali nawo m’nyengo yozizira unali utayoyoka. Kunsi kwa khosi lake kunali ubweya wakuda. Inapotolera mutu wake kumbali monyadira, ndipo inatiyang’anitsitsa ndi maso okhala ndi zikope zakuda, komanso inanunkhiza mpweya kuti imve fungo lathu. Nyanga zake zinali zokhuthala ndiponso zopindika ndipo iliyonse iyenera kuti inali yotalika mwina masentimita 40. Inali yolemera kuposa nkhosa zazikazi zomwe tinaona dzulo zija, ndipo iyenera kuti inali yolemera makilogalamu pafupifupi 35.

Ifeyo matupi athu anangoumiratu, ndipo tinabanika. Komabe, nyama yochenjerayi ikuoneka kuti inamva fungo lathu, chifukwa inagwedezera mutu wake uku ndi uku, kenako n’kuthawa. Zomwe tinaona ndi kuphunzira m’masiku awiri zinatigometsadi. Zinatichititsanso kuyamikira kwambiri Mlengi, amene ananena kuti: “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi.”—Salmo 50:10.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Nkhosa yam’tchire ya ku Cyprus (yomwe ili chakumbuyoyo) ndiponso ya ku Ulaya

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Top right: Oxford Scientific/photolibrary/Niall Benvie; European Mouflon: Oxford Scientific/photolibrary